Nyimbo 173
Chikondi—Chomangira Champhumphu cha Umodzi
1. Chikondicho chazirala
M’nthaŵi yamapeto.
Ife tisunge chikondi
Popeŵa kutero.
Tikatsanzira Mulungu,
Tidzapatsa onse
Chikondi cha Mulunguyo
Chochoka mumtima.
2. Chikondi chosanyengeza,
Chikondi chakuya,
Tiyeni tichikulitse
Ndi kuchipereka.
Tiyeni tifike mtima
Wa abale athu.
Okondedwa ndi Mulungu
Ife tiwakonde.
3. Dongosololi likugwa
Tikhale amodzi.
Chomangira cha umodzi
Tichigwiritsitse.
Chikondi chenichenidi
Chiri chofunika.
Chidzatidzetsa pafupi,
Mpaka ntchito itha.
4. Unansi wabwino ndi Ya
Udzatithandiza
Kukonda ena monga ’fe
Munthaŵi yovuta.
Chikondi chathu chilimbe
Mukuwona mtima.
Chomangira cha umodzi
Chikondi chitero.