Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Zilengezo
    Utumiki wa Ufumu—1999 | January
    • Zilengezo

      ◼ Mabuku ogaŵira mu January: Lililonse la mabuku a masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo. February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!. Khalani ndi bolosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu ochita chidwi, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba.

      ◼ Ofalitsa onse obatizidwa amene adzapezeka pa Msonkhano Wautumiki wa mlungu wa January 4 adzapatsidwa makadi a Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu ndi ma Identity Card a ana awo.

      ◼ Kuyambira mu February, nkhani yatsopano ya oyang’anira dera idzakhala yakuti “Kodi Mulungu ndi Weniweni Motani kwa Inu?”

      ◼ Mipingo ikonzekere kuchita Chikumbutso chaka chino pa Lachinayi, April 1, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, kuyendetsa zizindikiro za Chikumbutso sikuyenera kuchitika mpaka dzuŵa litaloŵa. Fufuzani kwa anthu odziŵa zanyengo kwanuko kuti mutsimikizire nthaŵi pamene dzuŵa lidzaloŵa m’dera lanu. Ngakhale kuti mpingo uliwonse ungafune kuchita Chikumbutso pawokha, nthaŵi zina zimenezi sizingatheke. Kumene mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mwina mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena oti agwiritse ntchito madzulo amenewo. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kuli kotheka, pologalamu ina ikatha pazipita mphindi zosachepera 40 ina isanayambe kuti mukhale ndi nthaŵi yokwanira yolonjera alendo, kulimbikitsa amene angoyamba kumene kusangalatsidwa, ndi kuti nthaŵiyo mupindule nayo mokwanira. Muyeneranso kulingalira za vuto la magalimoto ndi malo oimikapo magalimotowo, kuphatikizapo kusiya ndi kunyamula anthu. Bungwe la akulu liyenera kusankha makonzedwe amene angakhale abwino kwambiri kaamba ka mpingo wawo.

      ◼ Nkhani yapoyera yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 1999 idzakambidwa pa Lamlungu, April 18. Mutu wake udzakhala wakuti “Ubwenzi Weniweni ndi Mulungu ndi Mnansi.” Autilayini yake tidzatumiza. Mipingo imene mlungu umenewo idzakhala ikuchezeredwa ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera idzakhala ndi nkhaniyi mlungu wotsatira. Palibe mpingo umene uyenera kukhala ndi nkhaniyi lisanafike tsiku la April 18, 1999.

      ◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

      The Time for True Submission (lokonzedwera Asilamu)—Chingelezi

      Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1999—Chicheŵa, Chingelezi

      ◼ Makaseti Atsopano Omwe Alipo:

      Keep Your Eye Simple—Chingelezi

  • Phunziro la Buku la Mpingo
    Utumiki wa Ufumu—1999 | January
    • Phunziro la Buku la Mpingo

      Ndandanda ya maphunziro a mpingo m’bolosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.

      January  4: tsa. 14 mpaka tsa. 17*

      January 11: tsa. 17* mpaka tsa. 19

      January 18: tsa. 20 mpaka tsa. 25

      January 25: tsa. 26 mpaka tsa. 31

      * Kulekezera kapena kuyambira pakamutu.

  • Lipoti la Utumiki la September
    Utumiki wa Ufumu—1999 | January
    • Lipoti la Utumiki la September

      Av. Av. Av. Av.

      Chiŵerengero cha: Maola Mag. M.O. Maph.

      Apai. Apad. 6 148.7 20.5 89.3 13.5

      Apainiya 2,997 89.1 3.4 34.5 3.0

      Apai. Otha. 2,534 57.9 1.7 22.2 1.9

      Ofalitsa 36,592 10.3 0.4 4.1 0.5

      PAMODZI 42,129 Obatizidwa: 0

  • Kusintha Maola Ofunika kwa Apainiya
    Utumiki wa Ufumu—1999 | January
    • Kusintha Maola Ofunika kwa Apainiya

      1 Tonse timayamikira kukhala ndi apainiya okhazikika ndi othandiza amene amagwira ntchito zolimba m’mpingo. Ngakhale kumene gawo lili lochepa ndipo limafoledwa bwino kaŵirikaŵiri, apainiya apereka chitsanzo chabwino chifukwa cha changu chawo mu utumiki wa Ufumu. Alimbikitsa ofalitsa onse kuti akhale otanganidwa kufunafuna amene ali “ofuna.”—Mac. 13:48, NW.

      2 Sosaite yaona mavuto opitirizabe amene apainiya amakumana nawo, makamaka pofuna kupeza ntchito yaganyu imene ingawatheketse kupeza zosoŵa zawo kotero kuti apitirizebe kukhala mu utumiki wa nthaŵi zonse. Mkhalidwe wa zachuma umene uli m’mayiko ambiri wapangitsanso kukhala kovuta kwambiri kwa anthu ena kuti ayambe ntchito yaupainiya, ngakhale kuti chimenechi ndi chikhumbo chawo chachikulu. M’miyezi yapitayi, zifukwa zimenezi ndi zinanso zalingaliridwa mosamalitsa.

      3 Motero, polingalira zimene tanenazo, Sosaite yachepetsa maola ofunika kwa onse, apainiya okhazikika ndi othandiza omwe. Kuyambira chaka cha 1999, maola amene adzafunika kwa apainiya okhazikika ndi 70 mwezi uliwonse, kapena kuti 840 onse pamodzi pachaka. Apainiya othandiza adzafunika maola 50 pamwezi. Maola ofunika kwa apainiya apadera ndi amishonale sanasinthe, chifukwa Sosaite imawathandiza kusamalira zosoŵa zawo zakuthupi zikuluzikulu. Motero iwo angaike malingaliro awo onse pa ntchito yawo yolalikira ndi kupanga ophunzira.

      4 Tikukhulupirira kuti kusintha maola ofunika kumeneku kudzathandiza apainiya ambiri kusasiya utumiki wamtengo wapataliwu. Zikuyeneranso kulimbikitsa ofalitsa ochuluka kuyamba ntchito yaupainiya wokhazikika ndi wothandiza. Zimenezi zikhaletu dalitso lalikulu kwa aliyense m’mpingo!

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena