Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ndinu Bwenzi la Mulungu?—Chimene Mapemphero Anu Amavumbula
    Nsanja ya Olonda—1997 | July 1
    • zolakwa zathu, tingatonthozedwe ndi mawu a pa 1 Yohane 3:19, 20: “Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, m’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”

      Komabe, sitiyenera kusangalala ndi chisamaliro ndi chikondi cha Mulungu pamene tili m’mavuto chabe. Yehova ali ndi chidwi ndi chilichonse chimene chingakhudze mkhalidwe wathu wauzimu ndi maganizo. Inde, sitiyenera kuganiza kuti malingaliro ndi nkhaŵa zathu nzazing’ono zosati nkutchulidwa m’pemphero. (Afilipi 4:6) Mukakhala ndi bwenzi lanu, kodi mumangokambitsirana nkhani zikuluzikulu zokha za m’moyo wanu? Kodi simukambitsirananso tinkhani tina ndi tina? Mofananamo, muyenera kumasuka kukamba chilichonse ndi Yehova chokhudza moyo, podziŵa kuti “Iye asamalira inu.”​—1 Petro 5:7.

      Monga mudziŵa, ubwenzi sungakhalitse ngati mumangokamba zanu zokha. Momwemonso, m’mapemphero athu tisamangotchula za ife tokha. Tiyeneranso kutchula chikondi chathu ndi kukhudzidwa mtima kwathu ndi Yehova ndi zokonda zake. (Mateyu 6:9, 10) Pemphero si mpata woti tizingopemphera chabe chithandizo kwa Mulungu komanso ndi nthaŵi yoti tizimthokoza ndi kumtamanda. (Salmo 34:1; 95:2) Phunziro laumwini lidzatithandiza ‘kudziŵa’ zimenezi, popeza limatithandiza kukhala wozoloŵeranapo ndi Yehova ndi njira zake. (Yohane 17:3) Kuŵerenga buku la Masalmo ndi kuona mmene atumiki ena okhulupirika amalankhulirana ndi Yehova mudzakuona kukhala kothandiza.

      Ubwenzi ndi Yehova ndi chinthu cha mtengo wapatalidi. Chonde tiyeni tisonyeze kuti tikuyamikira mwa kupanga mapemphero athu kukhala aubwenzi kwambiri, ochokera pansi pa mtima, ndi aumwini. Tikatero tidzakhala ndi chimwemwe monga chomwe chinanenedwa ndi wamasalmo, yemwe anati: “Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa.”​—Salmo 65:4.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1997 | July 1
    • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

      Tinasangalala ndi phunziro lathu la fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. Malinga ndi chidziŵitso chatsopano chofotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, kodi tinganenebe kuti Mboni za Yehova lerolino zikuchitako ntchito yolekanitsa?

      Inde. Ndi chifukwa chabwino, ambiri aganiza zimenezi chifukwa Mateyu 25:31, 32 amati: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, inasonyeza chifukwa chake mavesiwa adzakwaniritsidwa chisautso chachikulu chitayamba. Yesu adzadza ndi ulemerero wake ndi angelo ake, nadzakhala pa mpando wake wachiweruzo. Ndipo adzalekanitsa anthu. Motani? Adzagamula mlandu malinga ndi zimene anthu anachita kapena zimene sanachite nthaŵiyo isanafike.

      Tingayerekezere zimenezi ndi kuzenga mlandu kumene kumafika pa kupereka chiweruzo pamlandu wa m’khoti. Umboni umapezeka panyengo yaitali khoti lisanagamule ndi kupereka chilango. Umboni wakuti kaya anthu amene ali ndi moyo tsopano adzakhala nkhosa kapena mbuzi wakhala ukupezeka kwa nthaŵi yaitali. Ndipo ukali kubwera. Koma pamene Yesu akhala pa chimpando chake, mlanduwo udzakhala utatha. Adzakhala wokonzeka kupereka chiweruzo. Adzalekanitsa anthu ku kudulidwa kosatha kapena ku moyo wosatha.

      Komabe, ngakhale kuti kulekanitsa anthu ku moyo kapena ku imfa kotchulidwa pa Mateyu 25:32 kuli mtsogolo, sikuti sipadzakhala kulekanitsa, kapena kugaŵa, nthaŵiyo isanafike. Baibulo, pa Mateyu chaputala 13, limatchula ntchito ina yolekanitsa yoyambirira. Nzosangalatsa kuti buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona, masamba 179-80, limafotokoza ntchitoyi pamutu wakuti “Kulekanitsidwa kwa Anthu”.a Bukulo limati: “Palinso zochitika zina zapadera zimene Yesu anazigwirizanitsa kwambiri ndi mapeto a dongosolo la zinthu. Chimodzi cha izi ndicho kulekanitsa ‘ana a ufumu’ kwa ‘ana a woipayo.’ Yesu analankhula za ichi m’fanizo lake la munda wa tirigu umene mdani anabzalamo namsongole wambiri.”

      Bukulo linali kunena za fanizo la Yesu lopezeka pa Mateyu 13:24-30 ndipo lomasulidwa m’mavesi 36-43. Onani m’vesi 38 kuti mbewu yabwino ya tirigu imaimira ana a Ufumu, koma namsongole amaimira ana a woipayo. Mavesi 39 ndi 40 akusonyeza kuti pa “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano”​—nthaŵi imene tikukhalamo tsopano​—namsongoleyo akusonkhanitsidwa. Kulekanitsidwa ndi kumtentha pomaliza pake, kumuwononga.

      Fanizo limeneli likunena za Akristu odzozedwa (amene m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi akutchedwa abale a Yesu). Komabe, mfundo njomveka yakuti ntchito yofunika kwambiri yolekanitsa ikuchitikadi nthaŵi zino, odzozedwa akulekanitsidwa kwa aja odzitcha Akristu komanso amene amasonyeza kuti ali “ana a woipayo.”

      Yesu anapereka zitsanzo zina za anthu akuwagaŵa, kapena kuwalekanitsa. Kumbukirani kuti anati za njira yotakata yomka nayo kuchiwonongeko: ‘Ali ambiri amene aloŵa pa icho.’ (Mateyu 7:13) Mawu amenewo samangonena zimene zidzachitika pomaliza pake. Amanena zimene zinali kuchitika, monga zilili tsopano kuti ali oŵerengeka omwe akupeza njira yopapatiza yomka nayo kumoyo. Kumbukiraninso kuti potumiza atumwi ake, Yesu anatero kuti iwo adzapeza ena oyenera. Ena sadzakhala oyenera, ndipo atumwiwo anayenera kusansa fumbi la mapazi awo “likhale mboni ya paiwo.” (Luka 9:5) Kodi si zoona kuti zonga zimenezo zimachitika pamene Akristu akuchita utumiki wawo wapoyera lerolino? Ena amalabadira, pamene ena amakana uthenga wa Mulungu umene timawaperekera.

      Nkhani za mu Nsanja ya Olonda zonena za nkhosa ndi mbuzi zinati: “Pamene chiweruzo chofotokozedwa m’fanizolo chili patsogolopa, ngakhale tsopano lino kanthu kena kofunika kwambiri kakuchitika. Ife Akristu tikuchita ntchito yopulumutsa moyo ya kulengeza uthenga wogaŵanitsa anthu. (Mateyu 10:32-39).” M’lemba limenelo la Mateyu chaputala 10, timaŵerenga kuti Yesu ananena kuti kumtsatira kudzachititsa magaŵano​—atate ndi mwana, mwana wamkazi ndi amake.

      Pomaliza, abale odzozedwa a Kristu apititsa patsogolo ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi. Pamene anthu aumva ndi kuchitapo kanthu, kuulandira kapena kuukana, amakhala akudzisonyeza okha mmene alili. Ife anthu sitingathe, ndipo sitiyenera, kunena kuti, ‘Munthu uyu ndi nkhosa; uja ndi mbuzi,’ m’lingaliro la Mateyu chaputala 25. Chikhalirechobe, kusonyeza kwathu anthu uthenga wabwino kumawapatsa mwaŵi wosonyeza kumene aima​—chimene ali ndi mmene amachitira ndi abale a Yesu. Chotero, monga umboni umene ukuchuluka pamlandu wa m’khoti, kulekanitsa amene akuchirikiza abale a Yesu ndi amene akukana kuwachirikiza kukuonekera. (Malaki 3:18) Monga momwe Nsanja ya Olonda inasonyezera, posachedwapa Yesu adzakhala pa chimpando chake ndi kupereka chilango, akumalekanitsa anthu mwachiweruzo m’lingaliro lake lonse, ku moyo kapena ku kudulidwa.

      [Mawu a M’munsi]

      a Lofalitsidwa mu 1983 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena