-
ZilengezoUtumiki wa Ufumu—1998 | May
-
-
Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! June: Lililonse la mabuku otsatirawa a masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko: Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere,” Happiness—How to Find It, Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Latsopano, “Let Your Kingdom Come,” Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?, Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona, ndi Your Youth—Getting the Best Out Of It. July ndi August: Mungagwiritsire ntchito lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabrosha akuti Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Prolems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? mungawagaŵire pamene kuli koyenera.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chitumbuka
Kesi Yosungiramo Magazini
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chingelezi
New World Translation of the Holy Scriptures (Saizi yapakati; DLbi12) lakuda—Chingelezi
Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu—Chingelezi
Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki—Cingelezi
◼ Makompakiti Disiki Atsopano Omwe Alipo:
Kingdom Melodies, Voliyumu 6
-
-
Phunziro la Buku la MpingoUtumiki wa Ufumu—1998 | May
-
-
Phunziro la Buku la Mpingo
Ndandanda ya maphunziro a mpingo m’brosha lakuti: Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
May 4: Mlungu Woyamba
May 11: Mlungu Wachiŵiri
May 18: Mlungu Wachitatu
May 25: Mlungu Wachinayi
-
-
Lipoti Lautumiki la JanuaryUtumiki wa Ufumu—1998 | May
-
-
Lipoti Lautumiki la January
Av. Av. Av. Av.
Chiŵerengero cha: Maola Mag. M.O. Maph.
Apai. Apad. 4 129.8 25.8 95.3 6.3
Apainiya 2,902 86.6 2.9 31.5 2.8
Apai. Otha. 2,566 57.2 1.1 20.9 1.8
Ofalitsa 36,132 10.5 0.2 3.8 0.4
PAMODZI 41,604 Obatizidwa: 184
-
-
Kodi Mukulinganiza Kudzatani m’Chilimwe?Utumiki wa Ufumu—1998 | May
-
-
Kodi Mukulinganiza Kudzatani m’Chilimwe?
1 Kodi si zoona kuti tingafikire zolinga zathu zopindulitsa ngati tikonzekera mmene tingagwiritsirire ntchito bwino kwambiri nthaŵi yathu? Miyezi ikudzayi ingatipatse mipata yosiyanasiyana yakufikira zolinga zateokrase. (Miy. 21:5) Kodi zina mwa zimenezo nziti?
2 Msonkhano wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu” uli chochitika chimodzi chimene tonsefe tiyenera kuchiphatikiza polinganiza zinthu zathu chilimwe chino. Pemphani nthaŵi kuntchito kapena kusukulu kuti tsiku lililonse la msonkhanowo mudzapezekepo.
3 Bwanji osalinganiza kudzaonjezera utumiki wanu wakumunda m’miyezi ikudzayi, poti tsopano nyengo yadzinja yatha, mungakhale ndi nthaŵi yambiri yowonongera pantchito yolalikira. Maholide a sukulu adzapatsa achinyamata mpata wakuchita upainiya wothandiza m’mwezi umodzi kapena ingapo ikudzayo. Enanso angalinganiziretu kudzachita upainiya wothandiza m’August, poti padzakhala milungu isanu yathunthu ndi maholide aŵiri. Mmene tizitsiriza chaka chautumiki August uno, tidzayesetsa ndithu kuti aliyense agwire nawo ntchito kwambiri mu utumiki.
4 Kodi mukulinganiza kudzathandiza mpingo wina wapafupi womwe ukufuna chithandizo pofola gawo lake? Woyang’anira dera angauze akulu zimene zikufunikira m’dera lanu. Kapena, ngati mungayenerere, ndipo mwina mungakonde kufunsira ku Sosaite kuti mukafole gawo losafoledwafoledwa kapena lopanda munthu, pemphani fomu kwa akulu anu. Ngati mudzakhala paholide kutali ndi kwanu, linganizani kudzamapezeka pamisonkhano ndi kuloŵa nawo mu utumiki wakumunda ndi mpingo wakomweko. Ngati mudzakachezera achibale omwe sali Mboni za Yehova, linganizani pasadakhale njira zimene mungakawauzire choonadi.
5 Kodi mukulinganiza kudzatani m’miyezi ikudzayi? Mosakayikira, mungakonde kuti mupume. Komabe musanyalanyaze mipata yambiri yomwe ilipo imene ingakulimbikitseni mwauzimu mwa kufunafunabe Ufumu choyamba.—Mat. 6:33; Aef. 5:15, 16.
-