Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 3/15 tsamba 8-13
  • Musaphonye Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musaphonye Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ufulu Umene Mulungu Ali Nawo
  • Polekezera pa Ufulu wa Anthu
  • Nchifukwa Ninji Ufulu Uli ndi Polekezera?
  • Ufulu Weniweni Utheketsedwa
  • Kusaphonya Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
  • Gwiritsirani Bwino Ntchito Ufulu Wanu Woperekedwa ndi Mulungu
  • Tikulandirani ku Misonkhano Yachigawo ya “Okonda Ufulu!”
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Tingapeze Bwanji Ufulu Weniweni?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 3/15 tsamba 8-13

Musaphonye Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu

‘Pamene pali mzimu wa [Yehova, “NW”] pali ufulu.’​—2 AKORINTO 3:17.

1. Kodi nchifukwa ninji Yesaya 65:13, 14 amagwira ntchito kwa Mboni za Yehova?

YEHOVA ali Mulungu waufulu. Ndipo ufulu woperekedwa ndi Mulungu uli dalitso lotani nanga! Chifukwa chakuti atumiki ake odzipatulira ali ndi ufulu woterowo, mawu aŵa a Mfumu Ambuye Yehova amagwira ntchito kwa iwo: ‘Tawonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; tawonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; tawonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi; tawonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.’​—Yesaya 65:13, 14.

2. Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova ali okhupuka mwauzimu?

2 Anthu a Mulungu amasangalala ndi mkhalidwe wokhupuka wauzimu umenewu chifukwa chakuti amatsogozedwa ndi mzimu wake, kapena mphamvu yogwira ntchito. Mtumwi Paulo anati: ‘[Yehova, NW] ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali mzimu wa Yehova pali ufulu.’ (2 Akorinto 3:17) Kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha ufulu woperekedwa ndi Mulungu? Ndipo kodi tifunikira kuchitanji kuti tiugwiritsire ntchito mokwanira?

Ufulu Umene Mulungu Ali Nawo

3. Kodi Mulungu ali ndi ufulu wamtundu wanji, ndipo chifukwa ninji?

3 Yehova ndiye yekha ali ndi ufulu wotheratu. Palibe cholengedwa chake chirichonse chomwe chingaikire malire ufulu wake chifukwa ali Mulungu Wamphamvuyonse ndi Mfumu Yachilengedwe chonse. Monga momwe munthu wokhulupirika Yobu ananenera kuti, ‘adzambwezetsa ndani? Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani?’ (Yobu 9:12) Mofananamo, Nebukadinezara mfumu ya Babulo anakakamizika kuvomereza kuti: ‘Palibe woletsa dzanja [la Mulungu], kapena wakunena naye, Muchitanji?’​—Danieli 4:35.

4. Kodi nchifukwa ninji Yehova amaikira malire ufulu wake?

4 Komabe, malamulo amakhalidwe abwino olungama a Yehova mwiniyo amampangitsa kuikira malire ufulu wotheratuwo. Ichi chinasonyezedwa pamene Abrahamu anawonetsa nkhaŵa yake pa nzika za Sodomu ndipo anafunsa kuti: ‘Kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?’ Yankho la Mulungu likusonyeza kuti amazindikira thayo lakuchita chimene chiri choyenera. Iye sakadawononga Sodomu ngati mukanakhalabe anthu alionse olungama. (Genesis 18:22-33) Mulungu amaikiranso malire ufulu wake chifukwa chakuti chikondi chake ndi nzeru zimampanga kukhala wosakwiya msanga ndipo amadziletsa.​—Yesaya 42:14.

Polekezera pa Ufulu wa Anthu

5. Kodi ndizinthu zina ziti zimene zimaika polekezera pa ufulu wa anthu?

5 Ngakhale kuti Yehova ali ndi ufulu wotheratu, ena onse amachita mogwirizana ndi malire ochititsidwa ndi chibadwa chawo, maluso, ndi malo awo okhala, limodzinso ndi zinthu zina zonga kufupika kwa moyo wamakono wa anthu ochimwa. Mulungu analenga munthu ndi ufulu wangwiro wogwira ntchito mkati mwa malo amene Yehova anamuikira. Pali zifukwa zina zimene ufulu wa munthu uliri ndi polekezera, osati wotheratu.

6. Kodi kuŵerengeredwa kwathu kwa Mulungu kumayambukira motani ufulu wathu?

6 Choyamba, ufulu wamunthu uli ndi polekezera chifukwa chakuti Mulungu analenga munthu kuti achite chifuno Chake. Yehova ali ‘woyenera kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa analenga zonse, ndi mwa chifuniro chake zinakhala, nizinalengedwa.’ (Chivumbulutso 4:11) Chotero munthu ali ndi kudziyankhira kwa Mpangi wake, yemwe moyenerera anapanga malamulo akuti anthu adzilamulidwa nawo. Mu Israyeli wakale pansi pa Chilamulo cha Mose, Mulungu anafuna kuti anthu amene analakwira dzina lake kapena kuswa lamulo la Sabata aphedwe. (Eksodo 20:7; 31:14, 15; Levitiko 24:13-16; Numeri 15:32-36) Ngakhale kuti ife monga Akristu sitiri pansi pa Chilamulo, ufulu wathu uli ndi polekezera chifukwa tiri oŵerengera mlandu kwa Yehova, amene ali Woweruza wathu, Wopereka Lamulo, ndi Mfumu.​—Yesaya 33:22; Aroma 14:12.

7, 8. (a) Kodi malamulo achilengedwe amaika motani polekezera pa ufulu wamunthu? (b) Kodi ndimalamulo ena ati a Mulungu amene amaika polekezera pa ufulu wathu monga anthu?

7 Chachiŵiri, ufulu wa anthu uli ndi polekezera chifukwa cha malamulo achilengedwe a Mulungu. Mwachitsanzo, chifukwa cha lamulo la mphamvu yokoka, munthu sangadumphe kuchokera pa nyumba yosanja yaitali popanda kudzivulaza kapena kudzipha. Mwachiwonekere, malamulo achilengedwe a Mulungu amaika polekezera pa ufulu wamunthu wakuchita zinthu zina.

8 Chachitatu, ufulu wamunthu uli ndi polekezera chifukwa cha malamulo a Mulungu achikhalidwe cha mtima. Mwachidziŵikire, mwawona kukwaniritsidwa kwa zimene Paulo analemba pa Agalatiya 6:7, 8: ‘Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera mu mzimu adzatuta moyo wosatha.’ Mosakaikira, malamulo a Yehova Mulungu achikhalidwe cha mtima amaikanso polekezera pa ufulu wathu, koma kuwamvera kumafunikira kuti tipeze moyo.

9. Kodi kukhala kwathu mbali ya chitaganya cha anthu kumaika motani polekezera pa ufulu wathu?

9 Chachinayi, ufulu wa munthu uli ndi polekezera chifukwa chakuti ali mbali ya chitaganya cha anthu. Chifukwa chake, iye ayenera kukhala ndi ufulu kokha kumlingo umene sukudodometsa wa ena. Akristu ayenera kugonjera ku ‘maulamuliro aakulu’ aboma, kuwamvera iwo malinga ngati sakufunikiritsa kuti tiswe malamulo a Mulungu. (Aroma 13:1; Machitidwe 5:29) Mwachitsanzo, tiyenera kumvera malamulo onena za kukhoma misonkho, liŵiro limene tingayendetsere galimoto, ndi zina zotero. Chenicheni chakuti tiyenera kumvera malamulo amenewo a “Kaisara” chimasonyezanso kuti ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu suli wotheratu.​—Marko 12:17; Aroma 13:7.

Nchifukwa Ninji Ufulu Uli ndi Polekezera?

10, 11. Kodi nchifukwa ninji Yehova anapatsa anthu ufulu wokhala ndi polekezera?

10 Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapatsa anthu ufulu wokhala ndi polekezera? Chifukwa chimodzi chinali chakuti Mlengi akhale ndi zolengedwa zaluntha padziko lapansi zimene zikamdzetsera ulemu ndi chitamando mwa mawu awo abwino ndi khalidwe. Anthu akhoza kuchita zimenezi, pamene kuli kwakuti zinyama sizingatero. Zinyama, pokhala kuti zimalamulidwa ndi chibadwa, sizimadziŵa kanthu ponena za chikhalidwe cha mtima. Mungathe kumphunzitsa galu kusatenga kanthu kena, koma simungamphunzitse kulakwa kwa kuba. Nyama pokhala ndi zochita zake zobadwa nazo, titero kunena kwake, singapange zosankha zimene zimabweretsa thamo ndi ulemu kwa Mulungu, pamene kuli kwakuti munthu akhoza kudzisankhira mwaufulu kutumikira Mpangi wake kuchokera m’chikondi ndi chiyamikiro.

11 Mulungu amaŵapatsanso anthu ufulu umenewu kaamba ka phindu lawo ndi chimwemwe. Iwo angagwiritsire ntchito ufulu wawo wokhala ndi polekezera mwakupanga ndi kutulukira zinthu, kukoma mtima ndi kugwirizana. Anthu alinso ndi ufulu wakusankha zinthu m’nkhani zonga ngati ntchito yodzisankhira ndi malo okhala. Lerolino, kaŵirikaŵiri zinthu zachuma ndi zandale zimachepetsa ufulu wakusankha, koma izi zingachitike chifukwa cha umbombo wa anthu, osati chifukwa cha njira imene poyambirira Mulungu analengera anthu.

12. Kodi nchifukwa ninji namtindi wa anthu ali muukapolo?

12 Ngakhale kuti Yehova anapatsa anthu ufulu waukulu, namtindi wa anthu ali muukapolo wogwiritsa mwala. Kodi chinachitika nchiyani? Anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, anaphonya chifuno cha ufulu woperekedwa ndi Mulungu. Iwo anapyola malire a Mulungu pa ufulu wawo natokosa ulamuliro woyenera wa Mulungu pa iwo monga Mfumu Ambuye, Yehova. (Genesis 3:1-7; Yeremiya 10:10; 50:31) Posakhutira ndi kugwiritsira ntchito ufulu wawo kulemekeza Mulungu, iwo anaugwiritsira mwadyera, kudzisankhira chimene chinali cholondola ndi chimene chinali cholakwa, mwakutero anagwirizana ndi Satana m’kupandukira kwake Yehova. Komabe, mmalo mopeza ufulu wowonjezereka, Adamu ndi Hava ochimwawo anayang’anizana ndi ziletso zokakamizidwa pa iwo ndi ukapolo, kutha kwa ufulu wawo, ndipo pomalizira pake imfa. Mbadwa zawo zinalandira choloŵa cha kutaika kwa ufulu kumeneku. ‘Pakuti onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.’ ‘Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.’​—Aroma 3:23; 5:12; 6:23.

13. Kodi nchifukwa ninji Satana wakhala wokhoza kuika anthu muukapolo?

13 Chifukwa cha chipanduko cha mu Edeni, Adamu ndi mbadwa zake anakhalanso muukapolo kwa Satana Mdyerekezi. Eya, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo”! (1 Yohane 5:19) Chifukwa cha mphamvu zake ndi maluso zoposazo Satana wakhala wokhoza kunyenga ndi kupangitsa akapolo anthu onse otalikana ndi Mulungu. Ndiponso, anthu adyera alamulira anthu anzawo kuwavulaza. (Mlaliki 8:9) Chotero, anthu onse tsopano ali muukapolo wa uchimo ndi imfa, kwa Satana ndi ziŵanda zake, ndi madongosolo adziko a ndale, chuma, ndi chipembedzo.

Ufulu Weniweni Utheketsedwa

14. Kodi chiyembekezo cha anthu cha ufulu weniweni chiri chogwirizana ndi chiyani?

14 Kumasuka ku uchimo, imfa, ndi Mdyerekezi ndi dziko lake kuli kogwirizana ndendende ndi chikhumbo cha Mulungu chakuthetsa nkhani yonena za kuyenera kwa uchifumu wake wapadziko lonse. Chifukwa chakuti Satana anadzutsa nkhaniyi, Yehova wamulola iye kukhalapobe, monga momwedi Iye analolela Farao kukhalapo kwa kanthaŵi. Ichi chinachitidwa kuti Yehova asonyeze kotheratu mphamvu yake ndikuti dzina lake lilengezedwe padziko lonse lapansi. (Eksodo 9:15, 16) Posachedwapa Mulungu adzadzilemekeza monga Mfumu Yachilengedwe chonse ndipo adzayeretsa dzina lake lopatulika mwakuchotsa chitonzo chimene chipanduko chochitidwa ndi Satana, Adamu, ndi Hava chinadzetsa. Chotero, owopa Yehova adzamasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa ndipo adzaloŵetsedwa m’dziko latsopano la ufulu woperekedwa ndi Mulungu.​—Aroma 8:19-23.

15. Kodi Yesu anachita mbali yotani m’kubwezeretsa ufulu kwa anthu?

15 Kuti abwezeretse ufulu kwa anthu, Mulungu anatuma Mwana wake kudziko lapansi monga munthu. Mwakupereka modzifunira moyo wake waumunthu wangwiro, Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anapereka nsembe yadipo, maziko akumasulira anthu. (Mateyu 20:28) Iye analengezanso uthenga waufulu. Pachiyambi pa uminisitala wake, anagwiritsira ntchito kwa iyemwini mawu aŵa: ‘Mzimu wa [Mfumu, NW] Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende.’​—Yesaya 61:1; Luka 4:16-21.

16. Kodi Ayuda a m’zaka za zana loyamba anayenera kuchita chiyani kuti apeze ufulu weniweni?

16 Kodi ndimotani mmene anthu akapezera ufulu umenewo? Yesu anati: ‘Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’ Chotero, otsatira a Yesu amasangalala ndi ufulu wauzimu. (Yohane 8:31, 32, 36) Ndiponso, Yesu anauza bwanamkubwa Wachiroma Pontiyo Pilato kuti: ‘Ndinabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga.’ (Yohane 18:37) Ayuda omwe anavomereza chowonadi monga momwe chinalalikidwa ndi kuchitiridwa chitsanzo ndi Yesu analapa machimo awo, kuwongolera njira yawo yolakwa, nadzipereka kwa Yehova, ndipo anabatizidwa monga momwe anachitira Yesu. (Mateyu 3:13-17; Machitidwe 3:19) Mwanjira imeneyi anakhala ndi ufulu wokhala ndi malire woperekedwa ndi Mulungu.

17. Kodi nchifukwa ninji Yehova amapatsa atumiki ake ufulu?

17 Yehova amapatsa atumiki ake okhulupirika ufumu makamaka kuti alemekeze uchifumu wake komanso kuti apeze chitonthozo kapena phindu. Iye anamasula Aisrayeli ku ukapolo wa Igupto kotero kuti amlemekeze monga ufulu wa ansembe, mboni zake. (Eksodo 19:5, 6; Yesaya 43:10-12) Mofananamo, Yehova anatulutsa anthu ake muukapolo wa Babulo kwakukulukulu kuti akamangenso kachisi wake ndi kubwezeretsa kulambira kowona. (Ezara 1:2-4) Pamene akapolowo anadzitanganitsa ndi zosangalatsa za iwo eni zakufuna zinthu zakuthupi, Yehova anatuma aneneri ake Hagai ndi Zekariya kukaŵakumbutsa mathayo awo kwa Mulungu. Kugwiritsira ntchito moyenerera ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu kunatulukapo kumalizidwa kwa kachisi, ku ulemerero wa Mulungu, ndiponso chitonthozo ndi ubwino kwa anthu ake.

Kusaphonya Chifuno cha Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu

18. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti atumiki amakono a Yehova sanaphonye chifuno cha ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu?

18 Bwanji nanga ponena za atumiki amakono a Mulungu? Monga gulu, sanaphonye chifuno cha ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu. M’ma 1870 iwo anayamba kumasuka ku zolakwa za Babulo ndi kusangalala ndi ufulu Wachikristu wowonjezereka. Ichi chinali chogwirizana ndi Miyambo 4:18, imene imati: ‘Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.’ Komabe, monga momwedi anthu akale a Mulungu analoŵera muukapolo ku Babulo kwakanthaŵi, choteronso atumiki a Yehova analoŵa muukapolo wina wake kwa Babulo Wamkulu mu 1918. (Chivumbulutso 17:1, 2, 5) Ziŵalo za ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga zimenezo zinakondwera pamene ‘mboni ziŵiri’ zophiphiritsira zinali kwala zakufa mwauzimu. Koma mwakukoma mtima kwapadera kwa Mulungu, atumiki ake odzozedwa anatsitsimulidwa, kumasulidwa mwauzimu mu 1919. (Chivumbulutso 11:3, 7-11) Akumagwiritsira ntchito ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu, anakhala mboni zokangalika za Wam’mwambamwamba. Chotero, kunali koyenerera chotani nanga kuti iwo, mu 1931, analandira mwachisangalalalo dzinalo Mboni za Yehova! (Yesaya 43:10-12) Makamaka chiyambire 1935 mpamene Mboni zodzozedwa zagwirizana ndi a ‘khamu lalikulu,’ omwe amayembekezera kulandira moyo wamuyaya padziko lapansi. Iwonso sakuphonya chifuno cha ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu.​—Chivumbulutso 7:9-17.

19, 20. (a) Kodi ndinjira imodzi iti imene anthu a Yehova amagwiritsira bwino ntchito ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu? (b) Kodi ndi m’njira ina yodziŵika iti imene Mboni za Yehova zimagwiritsira bwino ntchito ufulu umene Mulungu wazipatsa?

19 Anthu a Yehova akugwiritsira bwino ntchito ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu makamaka m’njira ziŵiri zodziŵika. Choyamba, amaugwiritsira ntchito kulondola njira yolungama. (1 Petro 2:16) Ndipo adzipezera mbiri yabwino yotani nanga! Mwachitsanzo, munthu wina analoŵa m’Nyumba Yaufumu ku Zurich, Switzerland, nati anafuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Atafunsidwa chifukwa chake, iye anati mlongo wake anali Mboni ndipo anachotsedwa kaamba ka chisembwere. Iye anati: ‘Ndilo gulu limene ndifuna kugwirizana nalo​—gulu limene silimalekerera mkhalidwe woipa.’ Panali chifukwa chabwino chimene New Catholic Encyclopedia idanena kuti Mboni za Yehova zapeza mbiri yakukhala “kamodzi kamagulu odzisungira bwino koposa padziko lapansi.”

20 Mboni za Yehova zimagwiritsiranso ntchito ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu mwakukwaniritsa ntchito yawo yakulalikira mbiri yabwino ya Ufumu, monga momwe anachitira Yesu. (Mateyu 4:17) Kudzera mwamawu apakamwa ndi mabuku, ponse paŵiri mwanthaŵi zonse ndi mwamwaŵi, iwo akulengeza Ufumu wa Yehova. Mwakuchita tero amadzipindulitsa kwakukulu mwakulimbikitsa chikhulupiriro chawo ndi kuŵalitsa chiyembekezo chawo. Ndiponso, ntchito imeneyi idzapulumutsa ponse paŵiri iwo eni ndi awo amene akuwamva. (1 Timoteo 4:16) Ponena za ntchito imeneyi, bukhu la Dynamic Religious Movements limati: “Kukakhala kovuta kupeza ziŵalo za kagulu kalikonse zimene zimagwira ntchito mwamphamvu kwambiri pachipembedzo chawo monga momwe zimachitira Mboni.”

21. Kodi pali umboni wotani wakuti Yehova akudalitsa uminisitala wa anthu ake?

21 Ha, Yehova akutidalitsa chotani nanga m’kukwaniritsa chifuno cha ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu! Izi zingathe kuwonedwa palipoti lachaka chatha la utumiki wakumunda​—chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu oposa mamiliyoni anayi, limodzi ndi opezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu oposa mamiliyoni khumi. M’kupenda kumodzi, Ireland anali ndi ziŵerengero zapamwamba 29 zotsatizanatsatizana za ofalitsa mwezi ndi mwezi; Mexico anali ndi ziŵerengero zapamwamba 78 m’miyezi 80; ndipo Japani ali ndi ziŵerengero zapamwamba 153 zotsatizanatsatizana!

Gwiritsirani Bwino Ntchito Ufulu Wanu Woperekedwa ndi Mulungu

22. Kodi ndi mfundo yaikulu yotani ya mafunso ena odzutsa maganizo amene tingadzifunse?

22 Ngati ndinu mmodzi wa Mboni zodzipatulira za Yehova, kodi mukuugwiritsira bwino ntchito ufulu wanu woperekedwa ndi Mulungu? Aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndiri wosamala kugwiritsira ntchito ufulu wanga woperekedwa ndi Mulungu kotero kuti ndipeŵe kukhumudwitsa munthu aliyense mwakhalidwe lolakwa? Kodi mwachikumbumtima ndimamvera malamulo a Kaisara, ngakhale kuti ndimaika malamulo a Mulungu patsogolo? Kodi ndimagwirizana kotheratu ndi akulu mumpingo? Kodi ndikugwiritsira ntchito ufulu wanga woperekedwa ndi Mulungu mokwanira m’kulalikira mbiri yabwino? Kodi nthaŵi zonse ndimakhala ‘wakuchuluka muntchito ya Ambuye’? Kodi ndikulondola ntchito yakuthupi pamene ndingathe kugwiritsira bwino koposa ufulu wanga woperekedwa ndi Mulungu kufutukula uminisitala wanga, kukalimira mathayo okulirapo mumpingo kapena utumiki wanthaŵi zonse?’​—1 Akorinto 15:58.

23. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tisaphonye chifuno cha ufulu woperekedwa ndi Mulungu?

23 Tiyeni tonsefe ‘tilawe, ndipo tiwone kuti Yehova ndiye wabwino.’ (Salmo 34:8) Tiyeni timkhulupirire, kugwirizana ndi malamulo ake, ndi kulemekeza dzina lake loyera mwakulengeza mwachangu Ufumu wake. Kumbukirani kuti iwo ‘akufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta.’ (2 Akorinto 9:6) Chotero, tiyeni tipereke utumiki wamtima wonse kwa Yehova ndi kusonyeza kuti sitikuphonya chifuno cha ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi Mulungu ali ndi ufulu wotani?

◻ Kodi ufulu wa anthu uli ndi polekezera potani?

◻ Kodi ufulu weniweni unatheketsedwa motani?

◻ Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipeŵe kuphonya chifuno cha ufulu woperekedwa ndi Mulungu?

[Chithunzi patsamba 9]

Ufulu wa anthu umaikiridwa malire ndi zinthu zonga lamulo la mphamvu yokoka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena