Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/15 tsamba 8-9
  • Kodi Madyerero A Kututa Amakondweretsa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Madyerero A Kututa Amakondweretsa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Oloŵetsamo Zachikunja
  • Kodi Mulungu Amaziona Motani?
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Limbikirani ntchito yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/15 tsamba 8-9

Kodi Madyerero A Kututa Amakondweretsa Mulungu?

ZIPATSO zosiririka, ndiwo zamasamba zooneka bwino, ndiponso chimanga chakucha bwino zitaunjikidwa pamodzi kupanga mulu zimaoneka bwino kwambiri. Panthaŵi yotuta, zoterezi zimakongoletsa maguwa ndi magome a matchalitchi mu England monse. Monga kwina konse, mu Ulaya, madyerero osiyanasiyana amachitika ponse paŵiri kuchiyambi ndi kumapeto kwa nthaŵi ya kututa.

Kwa amene amadalira nthaka pamoyo wawo amayamika kwambiri chifukwa cha zomwe nthaka yatulutsa. Ndithudi, Mulungu anauza mtundu wakale wa Aisrayeli kuti azichita madyerero katatu pa chaka amene anali okhudzana ndi kututa mbewu. Kuchiyambi kwa ngululu, panthaŵi ya Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, Aisrayeli ankapereka kwa Mulungu mtolo wa zipatso zoyamba za balele zomwe atuta. Pa Madyerero a Masabata (kapena kuti Pentecoste) kumapeto kwa ngululu, ankapereka mikate yazipatso zoyamba za tirigu. Mu mphakasa kunkakhala Madyerero a Kututa, amene ankakhala mapeto a chaka cha ulimi cha Aisrayeli. (Eksodo 23:14-17) Madyererowa anali “masonkhano opatulika” ndi nthaŵi yachisangalalo.​—Levitiko 23:2; Deuteronomo 16:16.

Koma bwanji madyerero a kututa a masiku ano? Kodi amakondweretsa Mulungu?

Oloŵetsamo Zachikunja

Pokhumudwa ndi njira yakudziko yochitira phwando la kututa motsatira miyambo ndiponso kuledzera komwe kunkachitika pa chikondwererecho mtsogoleri wa mpingo wa Anglican ku Cornwall, England, mu 1843 anayambitsanso mwambo wa kututa wakale. Anatenga zokolola zoyamba ndipo anapanga mkate wochitira chikondwerero cha Misa m’tchalitchi chake. Motero anayambitsa madyerero a Lammas​—chikondwerero cha “Akristu” chimene ena amati chinayambira ku chipembedzo chakale cholambira Lugh, mulungu wa Asetiki.a Motero, madyerero amakono a Aanglican ali ndi chiyambi chachikunja.

Koma bwanji za zikondwerero zina zimene zimachitika kumapeto kwa nthaŵi yakututa? Malinga ndi Encyclopædia Britannica, zambiri mwa zochitika pa mapwando amenewa zidayambira pa “kukhulupirira mizimu kwa kuti chimanga chili ndi mzimu wake kapena kuti amake chimanga.” M’zigawo zina alimi ankakhulupirira kuti mzimu unkakhala mumtolo womalizira kukolola. Kuti apirikitse mzimuwo, ankamenyetsa zokololazo pansi. M’madera ena ankatenga makhwatha a chimanga ndi kuluka “chidole chachimanga” chomwe ankachisunga bwino kuti chiŵapatse “mwaŵi” mpaka nthaŵi yobzala chaka chotsatira. Kenaka ankalimira pansi m’nthaka ngala za mbewuzo nchikhulupiriro chakuti zidzadalitsa mbewu zatsopanozo.

Nthano zina zakale zimagwirizanitsa nyengo yokolola ndi kulambira mulungu wa ku Babulo Tamuzi, mwamuna wa mulungu wachikazi wachonde Ishtar. Kubudula ngala za chimanga kunkaimira imfa ya mwadzidzidzi ya Tamuzi. Nthano zinanso zakale zimagwirizanitsa nthaŵi yotuta ngakhale ndi kupereka anthu nsembe​—machitidwe amene Yehova Mulungu amanyansidwa nawo.​—Levitiko 20:2; Yeremiya 7:30, 31.

Kodi Mulungu Amaziona Motani?

Zochita za Yehova ndi mtundu wakale wa Aisrayeli zimaonetseratu poyera kuti Yehova, Mlengi ndi Magwero a moyo, anafuna kuti alambiri ake alambire iye yekhayekhayo. (Salmo 36:9; Nahumu 1:2) M’masiku a mneneri Ezekieli, machitidwe akulirira mulungu Tamuzi anali ‘chonyansa chachikulu’ pamaso pa Yehova. Zimenezi, pamodzi ndi miyambo ina yonyenga yachipembedzo, zinachititsa Mulungu kusamvera mapemphero a olambira monyengawo.​—Ezekieli 8:6, 13, 14, 18.

Yerekezerani zimenezi ndi zimene Yehova Mulungu analangiza Aisrayeli pa za kututa. Pa Madyerero a Kututa, Aisrayeli ankapanga msonkhano wamwambo pamene ana ndi nkhalamba, olemera ndi osauka, ankakhala m’misasa yokongoletsedwa ndi masamba a mitengo yophuka bwino. Kwa iwo, inali nthaŵi yachikondwerero chachikulu, komanso inali nthaŵi yokumbukira kuomboledwa kumene Mulungu anachitira makolo awo panthaŵi ya Kutuluka mu Aigupto.​—Levitiko 23:40-43.

Panthaŵi ya madyerero a Aisrayeli, nsembe zinkaperekedwa kwa Yehova, Mulungu woona yekha. (Deuteronomo 8:10-20) Koma kunena za zikhulupiriro za mizimu zimene zanenedwa poyambazo, palibe pomwe Baibulo limanena kuti dzinthu, monga mitolo ya tirigu, ili ndi mzimu.b Ndipo Malemba amasonyeza bwino kuti mafano alibe moyo, satha kulankhula, kuona, kununkhiza, samva kukhudzidwa, ngakhale kupatsa owalambira chithandizo.​—Salmo 115:5-8; Aroma 1:23-25.

Lerolino Akristu sali pansi pa pangano la Chilamulo limene Mulungu anathetsa ndi mtundu wakale wa Aisrayeli. Ndithudi, Mulungu ‘anachikhomerera ichi pamtengo wozunzirapo wa Yesu.’ (Akolose 2:13, 14) Atumiki a Yehova a masiku ano amatsatira “chilamulo cha Kristu” ndipo amayamikira kwambiri zonse zimene Mulungu amawaphunzitsa.​—Agalatiya 6:2.

Mtumwi Paulo ananena poyera kuti madyerero a Ayuda anali “mthunzi wa zilinkudzazo,” anawonjeza kuti “koma thupi ndi la Kristu.” (Akolose 2:16, 17) Motero, Akristu oona amagwirizana ndi Malemba kuti: “Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda. . . Simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.” (1 Akorinto 10:20, 21) Kuwonjezera apo, Akristu amamvera malangizo akuti “musakhudza kanthu kosakonzeka.” Kodi madyerero akututa a kwanuko ndi ogwirizana ndi zachikunja kapena kulambira konyenga ndi konyansa pamaso pa Mulungu? Ndipo Akristu oona ayenera kupeŵa kusakondweretsa Yehova mwakusachita nawo kulambira kodetsedwa kotero.​—2 Akorinto 6:17.

Mwana woyamika akalandira kanthu kwa atate ake, kodi amathokoza yani? Mlendo wosamdziŵa kapena kholo lake? Mwa mapemphero a pansi pamtima, olambiradi Mulungu amathokoza Yehova, Atate wawo wakumwamba, chifukwa cha kupatsa kwake moolowa manja.​—2 Akorinto 6:18; 1 Atesalonika 5:17, 18.

[Mawu a M’munsi]

a Liwu lakuti “Lammas” lachokera ku Chingelezi Chakale kutanthauza “phwando la mkate.”

b Insight on the Scriptures imati: “Neʹphesh (sou) sikutchulidwa mogwirizana ndi kulengedwa kwa zomera za pa ‘tsiku’ lachitatu la kulenga (Gen. 1:11-13) kapenanso pambuyo pake, popeza zomera zilibe mwazi.”​—Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena