Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hs mutu 4 tsamba 57-80
  • Kugwira Ntchito kwa Mzimu Woyera pa Anthu a m’Nthawi Zakale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwira Ntchito kwa Mzimu Woyera pa Anthu a m’Nthawi Zakale
  • Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NCHITO ZAKALE ZOLIMBA MTIMA MWA NJIRA YA MZIMU WOYERA
  • NCHITO YAKE YOSONKHEZERA PAMENE OWERUZA ANALAMULIRA
  • WODZOZEDWA WA YEHOVA
  • KUONERATU ZOCHITA ZA NTHAWI ZATHU
  • Mphatso ya Yehova ya Mzimu Woyera
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Anthu Okhulupirika Akale Amene Anatsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano
    Nsanja ya Olonda—2011
  • “Chilengedwe Chatsopano” Chiyamba Kugwira Ntchito!
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
Onani Zambiri
Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
hs mutu 4 tsamba 57-80

Mutu 4

Kugwira Ntchito kwa Mzimu Woyera pa Anthu a m’Nthawi Zakale

1. Kodi ndi motani Baibulo mwa iro lokha monga bukhu limatsutsira awo amene amakana kuti kuli chinthu chotero chonga mzimu woyera?

KULI kopanda pake kwa anthu okhulupirira zinthu zakuthupi a lero lino kutsutsa kuti kulibe chinthu chotero’cho chonga mzimu woyera. Chipatso cha kugwira ntchito kwake pa anthu a m’nthawi zakale chikali nafebe, pa dziko lonse. Chipatso chimene’cho chapulumuka zoyesayesa za anthu ndi mitundu kuchiononga. Kodi chimene’cho n’chiani? Bukhu losakhoza kuonongedwa lochedwa Baibulo Lopatulika. Mosasamala kanthu za chitsutso choopsya chochitidwa ndi anthu ndi ziwanda, Bukhu lopatulika limene’lo liri bukhu lofalitsidwa kopambana pakati pa mabukhu onse olembedwa ndi anthu. Pali amuna ndi akazi amene adzatetezera Bukhu limene’lo ndi miyoyo yao ya iwo eni.

2. Kodi n’chifukwa ninji Baibulo siliri losiyana ndi mabukhu ena onse ponena za manja ogwiritsiridwa ntchito mu’kulilemba?

2 Ndithudi Baibulo Loyera liri losiyana ndi mabukhu ene onse. Chifukwa ninji? Osati kokha m’kukhala kwake lolembewa ndi anthu wamba a banja lathu laumunthu. Palibe ali yense amene amanena kuti Baibulo linalembedwa ndi manja koposa aja a anthu wamba. Koma kodi iwo anali anthu a mtundu wotani? Kodi zolemba zao zinali zochokera kwa eni? Zimene’zi ziri n’chochita pa nkhani’yo.

3-5. (a) Kodi Baibulo lumatiuzanji ponena za m’mene linalembedwera (b) Kodi ndi motani m’mene Petro amatsimikizirira chimene’chi mu 2 Petro 1:15-21?

3 Baibulo lenileni linatiuza kuti za m’kati mwa mabukhu ang’ onoang’ono makuni asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi limodzi zinalembedwa ndi anthu. Baibulo lenileni’lo limatiuza mtundu wa anthu amene anali olilemba ake. Limasonyeza’nso imene inali mphamvu yosaoneka yosonkhezera anthu amene’wo kuchita kulemba’ko. Panali mzimu kutseri kwao polemba. Mzimu’wo suyenera kunenedwa kukhala wochokera kwa Satana Mdierekezi, pakuti kwa nthawi yonse’yi iye wakhala woyedzamira ku kusocheretsa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Mzimu wokhala kutseri kwa kulembedwa kwa Baibulo sunali mzimu umene uli kutseri kwa dongosolo la zinthu lakale liripo’li. Koma ponena za mtundu wa anthu amene anachita kulemba’ko ndi ponena za mzimu umene unawasonkhezera kulemba, tiyeni tione mau achidule a mtumwi Petro, wophedwera chikhulupiriro cha Chikristu choona:

4 “Koma ndizachita’nso changu kosalekeza kuti nditachoka ine [m’kuphedwera chikhulupiriro], mudzakhoza kukumbukira izi. Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakum’dzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.

5 “Ndipo tiri nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu; ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.” 2 Petro 1:15-21.

6. Kodi ndi chichirikizo chotani chimene chiripo cha kuchula kwa Petro kusandulika kwa Kristu, ndi chimene chinapangitsa makalata ake awiri kukhala zolemba zouziridwa?

6 Petro iye mwini anakhala mmodzi wa anthu amene’wo amene analemba ndi kulankhula zochokera kwa Mulungu ‘pamene anagwidwa ndi mzimu woyera.’ Chifukwa cha chenicheni chimene’chi, Petro anapereka umboni wokhulupirika ku chimene iye ndi atumwi’ wo Yakobo ndi Yohane, monga mboni zoona ndi maso, anaona ndi kumva pamene Yesu Kristu anasandulika pamaso pao pa phiri lalitali m’Palestina. Ophunzira ena atatu a Kristu anapereka mbiri yolembedwa yonena za kusandulika kwa Yesu Kristu kumene’ko miyezi ingapo imfa yake yachiwawa isanachitike kunja kwa malinga a Yerusalemu. (Mateyu 17:1-9; Marko 9:2-9; Luka 9:28-36) Chotero umboni wa Petro ukuchirikizidwa ndi anthu odalirika. M’Baibulo, makalata awiri okhala ndi dzina la Petro analembedwa ndi iye, munthu; koma chenicheni chimene’chi sichinapangitse zolembedwa za makalata ake kukhala zopangidwa ndi munthu chabe. Makalata a Petro anali ndi mzimu woyera kutseri kwake. Chifukwa cha chimene’cho iwo anali ouziridwa ndi Yehova Mulungu, Magwero a mzimu woyera.

7. Mu 2 Petro 3:15, 16 kodi ndi motani m’mene Petro amasonyezera kuti zolemba za Paulo zikuikidwa pa mpambo wa kukhala mbali ya Baibulo louziridwa?

7 M’kalata yake yachiwiri Petro akutamanda zolemba za mtumwi Paulo kukhala mbali ya zolembedwa zouziridwa za Baibulo. Petro anati: “Yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monga’nso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye anakulemberani; monga’nso m’akalata ake onse pokamba momwemo zaizi; m’menemo muli zina zobvuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monga’nso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni.” (2 Petro 3:15, 16) Lero lino pali otsutsa amene amanena kuti munthu wamba (Paulo) analemba makalata amene’wo, kotero kuti iwo ali opangidwa ndi munthu. Otsutsa otere akupotoza Malemba, “ndi kudziononga nao eni.”

8. Ponena za Malemba olembedwa ndi anthu amene analankhula ndi kulemba zochokera kwa Mulungu, kodi n’chiani chimene Paulo ananena mu 2 Timoteo 3:16, 17?

8 Ponena za Malemba Opatulika olembedwa ndi anthu amene analemba ndi kulankhula zochokera kwa Mulungu, mtumwi Paulo ananena izi: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu [kwenikweni, lopumiridwa (theopneustos)], ndio lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iri yonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17, ndi Kingdom Interlinear.

9. Mwa kuyang’ana ku Malemba amene’wo kodi Paulo anali wokhoza kutsimikizira chiani ponena za maziko a Chikristu?

9 Paulo iye mwini anali “munthu wa Mulungu waluso wotero.” Iye anali wodziwa bwino kwambiri Malemba akale Achihebri. Mwa njir a ya maumboni ku Malemba ouziridwa amene’wo Paulo anali wokhoza kutsimikizira maziko operekedwa ndi Mulungu kaamba ka Chikristu choona.—Machitidwe 17:3.

10. Kodi n’chifukwa ninji maulosi a Baibulo apitirizabe kikwaniritsidwa ngakhale kufikira tsopano, ngakhale kuli kwakuti anthu sanadziwe m’mene Mulungu akachititsira maulosi kukwaniritsidwa?

10 Pali chifukwa chake maulosi amene ali m’Baibulo amapitrizirabe kukhala oona, ngakhale m’zaka zathu za zana la makumi awiri. Chifukwa’cho n’chakuti maulosi amene’wa sayenera kukhala zoneneratu za anthu chabe amene amayesa kupanga matanthauziridwe a iwo eni ponena za m’mene mkhalidwe wa zochitika za dziko udzakhalira. Mosemphana ndi zimene’zo, maulosi a Baibulo ali ochokera kwa Mulungu, amene’wa akumaperekedwa kupyolera mwa anthu odzipereka kwa Iye. Mulungu amachititsa maulosi ake kuchitika ngakhale kuli kwakuti anthu samadziwa m’mene Mulungu amakuchitira. Nsonga imene’yi inagogomezeredwa ndi Petro, pamene iye kwa khamu la Ayuda m’kachisi pa Yerusalemu anati: “Zimene Mulungu analalikiratu m’kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Kristu, Iye anakwaniritsa chotero . . . amene thambo la kumwamba liyenera kum’landira kufikira nthawi zakukonza’nso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.” (Machitidwe 3:18-21) Baibulo limapereka maulosi onena za Mulungu amene samanama, ngakhale, kuli kwakuti iye analankhula mwa njira ya aneneri.

11. Kodi ndi motani m’mene Petro, polankhula ndi mpingi wa ophunzira zana limodzi ndi makumi awiri mu Yerusalemu, amagogomezerera kuti maulosi a Mulungu anayerera’di kukwaniritsidwa?

11 Chifukwa chakuti maulosi a Baibulo ali ochokera kwa Mulungu mwa njira ya mzimu wake woyera, iwo ayenera kukwaniritsidwa basi. Chenicheni chimene’cho chinanenedwa moonjezereka ndi Petro pamene iye ananena ndi mpingo wa ophunzira zana limodzi mphambu makumi awiri mu Yerusalemu kuti: “Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m’kawa mwa Davide za Yudase, wokhala m’tsogoleri wa iwo adagwira Yesu.”—Machitidwe 1:15, 16.

12. Kodi ndi motani m’mene Petro ndi ophunzira ena anagwirizanira m’pemphero ndi kusonyeza kuti Salmo 2:1 lolembedwa ndi Davide linayenera kukwaniritsidwa?

12 Pambuyo pake, Petro anagwirizana ndi opunzira anzake m’pemphero limene linagogomezera m’mene ulosi wina wonenedwa ndi Davide unayenera kukwaniritsidwira. Machitidwe 4:24, 25 amati “Anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, [Ambuye] Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri m’menemo; amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiani? Nalingirira zopanda pake anthu?” (Salmo 2:1) Motero Akristu a m’zaka za zana loyamba amene’wo anazindikira kuti Malemba Opatulika Achihebri anali chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu wogwira ntchito pa anthu a m’thawi zakale.

13. (a) Malinga ndi kunena kwa 2 Samueli 23:1-3, kodi ndani amene anayenera kupatsidwa thamo kaamba ka mbali za Malemba Achihebri olembedwa ndi Davide wodzozedwa’yo? (b) Kodi ndi zinthu zotani zimene zinali zochititsa kukwaniritsidwa kwa maulosi mwa njira ya Davide?

13 Popeza kuti wamasalmo Davide akuchulidwa dzina pano mwachindunji, tingafunse bwino lomwe kuti: Kodi iye anamva bwanji ponena zakulankhula ndi kulemba zinthu zimene zinapangidwa kukhala mbali ya Malemba opatulika Achihebri? Iye samadzitama kaamba ka zolemba zake, zimene zasungidwa kukhala za phindu lapadera ndi zofunika mwapadera kwa ife lero lino. Potsimikizira zimene’zi nachi cholembedwa chonena za mfumu yodzozedwa imene’yi ya Israyeli yense, monga momwe chasungidwira kaamba ka ife mu 2 Samueli 23:1-3: “Ndipo mau otsiriza za Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Jese, atero munthu wokwezedwa ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini masalmo wokoma wa Israyeli: Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mau ake anali pa lirime langa. Mulungu wa Israyeli anati Thanthwe la Israyeli linalankhula ndi ine.” Chotero zinthu zimene zinachititsa kukwaniritsidwa kwa maulosi mwa njira ya Davide sizinali mtandadza wa kuoneratu kwake ndi luso lake la kupanga matanthauziridwe a iye mwini a zinthu. Mzimu wa Mulungu umene unali kugwira ntchito pa Davide ndi kuyendetsa zinthu kwa Mulungu ndizo zimene zinachititsa kuchitika kwake.

14. Kuphatikiza pa Davide, kodi ndi motani m’mene Yesaya ndi Yeremiya anasonyezera kuti mbali zao zolembedwa za Malemba sizinali malingaliro opangidwa ndi iwo eni?

14 Davide sindiye yekha amene anabvomereza kuti mbali ya zolembedwa zake m’Baibulo Loyera sizinali zopangidwa ndi iye mwini. Aneneri ena, amene mabukhu ao ouziridwa asungidwa m’ Baibulo, moona mtima akubvomereza kuti anali mau a Yehova Mulungu amene anadza kwa iwo. Mwa chitsanzo, Yesaya akuyamba bukhu lake lalikulu la ulosi mwa kunena kuti: “Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda. Imvani, miyamba inu, chera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena.” (Yesaya 1:1, 2) Yeremiya akuyamba bukhu lake lalikulu la ulosi, kuti: “Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m’dziko la Benjamini; amene anam’dzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.”—Yeremiya 1:1, 2.

NCHITO ZAKALE ZOLIMBA MTIMA MWA NJIRA YA MZIMU WOYERA

15. Kodi ndi motani m’mene mzimu woyera umene unachititsa kulembedwa kwa zolemba za Baibulo unadzisonyezera kukhala wamphamvu kwambiri koposa lupanga la atsogoleri ankhondo amphamvu?

15 Munthu ali yense asanyozetse modzikuza zinthu zotulutsidwa ndi mzimu woyera mu mpangidwe wa zolembedwa zopatulika. Cholembera chimene chinasonkhezeredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu m’manja mwa olemba Baibulo chatsimikizira kukhala champhamvu kwambiri koposa lupanga la Kaisara, la Napoleon Bonaparte, la Adolf Hitler. Kunena zoona, mzimu woyera wakhala wokhoza kuchita zinthu zokondweretsa kopambana koposa kulemba ndi cholembera ndi inki. Anthu a nthawi zakale akusimbidwa kukhala atachita zinthu zolimba ntima mwa njira ya nyonga yamphamvu yochokera kwa Mulungu Wamphamvuyonse.

16, 17. (a) Pamene Mose anatansira ndodo pa Nyanja Yofiira, kodi mphamvu yaikulu kwambiri’yo inachokera kuti kuti igawanitse madzi? (b) Kodi ndi motani m’mene Yesaya 63:11-14 amatsimikizirira yankho lolondola?

16 Monga chitsanzo, tiyeni titenge wolemba mabukhu asanu oyambira a Baibulo, Mose. Kalekale m’chake cha 1513 B.C.E. iye anaima pa tsidya la kumadzulo la Nyanja Yofiira. Iye anatansa ndodo yokhala m’dzanja lake lamanja pa nyanja’yo. Taonani! Madziwo anagawanika ndi kulola Aisrayeli kuoloka Aigupto olondola’wo asanawafikire. Kodi mphamvu iri yonse yaikulu kwambiri yochokera kwa Mose inachititsa chozizwitsa chimene’cho? Zosatheka! Osati kuchokera kwa mneneri Mose, koma ku Magwero akumwamba a mphamvu yonse yaikulu kwambiri kunachokera mphamvu yosatsutsika yokhoza kugawanitsa mpingiridzo wa madzi umene unapinga kupulumuka kwa Aisrayeli ku upandu waukulu. (Eksodo 14:21 kufikira 15:21) Chotero liro lino, pamene anthu a Yehova akulangidwa ndipo akudzipeza ali m’bvuto, iri’di nthawi kwa iwo yokumbukira kachitidwe kakale ka Yehova ndi kufunsa funso lakuti:

17 “Ali kuti Iye amene anawatulutsa m’nyanja pamodzi ndi abusa [Mose ndi Aroni] a gulu lake? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wake woyera pakati pao, amene anayendetsa mkono wake [wa nyonga] waulemerero pa dzanja lamanja la Mose? amene anagawanitsa madzi [a nyanja] pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha? amene anawatsogolera kupitira mwa kuya monga kavalo m’chipululu osapunthwa iwo? Monga ng’ombe zotsikira kuchigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; chomwe’cho inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.”—Yesaya 63:11-14.

18. Mofananamo, kodi ndi motani m’mene Mulungu mmodzimodzi’yo watsalira pang’ono kudzipangira ‘dzina lokongola’ m’zaka zathu za zana la makumi awiri?

18 Mavesi ochokera mu ulosi wa Yesaya amene’wo amasonyeza m’mbuyo ku nthawi imene anthu a Mose analanditsidwa ku ukapolo wao ku Igupto wakale. Kumene’ko, m’ngululu ya chaka cha 1513 B.C.E., Mulungu anadzipangira dzina losakhoza kuonongeka, dzina laulemerero wosafanana ndi wina uli wonse. Koma tsopano’nso, m’zaka zathu za zana la makumi awiri, nthawi yakwana kwa Mulungu yemwe’yu kuti ‘adzitengere mbiri yaulemerero.’ Pa mlingo waukulu kopambana iye adzachititsa chilanditso chofanana ndi chimene iye anachichita pa Nyanja Yofiira. Achimwemwe adzakhala anthu onse amene dzina la Yehova lidzakhala “laulemerero” kwa iwo pa nthawi’yo.

19. Monga momwe kwasonyezedwera mu Ahebri 11:29, kodi kunali mogwirizana ndi mkhalidwe wotani wa Mose kuti zinthu zinachitika?

19 Chotero tiyeni tisachepetse nyonga yaikulu kwambiri ya mphamvu yogwira ntchito ya Yehova. Iri yamphamvu mofananamo lero lino monga momwe inaliri zaka mazana makumi atatu mphambu zizana zapita’zo Mneneri Mose sanachepetse mphamvu yake yaikulu. Iye anali ndi chikhulupiriro m’Magwero Aumulungu a mzimu wochita zozizwitsa umene’wo. Malinga ndi kunena kwa Mose chikhulupiriro chinali njira imene zinthu zinachitikira; “Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aaigupto poyesa’nso anamizidwa.” (Ahebri 11:29) Mu mkhalidwe wotero’wo kunasonyezedwa kuti Mulungu amapfupa awo amene amasonyeza chikhulupiriro mwa iye. (Ahebri 11:6) Onani’nso colembedwa’cho pa Numeri 11:16, 17, 24-29 ponena za Mose wokhulupirika’yo ndi mzimu.

20, 21. (a) Kodi n’chifukwa ninji awo m’nthawi zakale amene anatsimikizira kukhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu anayenera kukhala anali ndi mbali yaikulu ya mzimu woyera? (b) Kodi ndi anthu atatu otani a chikhulupiriro amene akuchulidwa mu Ahebri 11:4-7, ndipo kodi amati chiani ponene za iwo?

20 Chikhulupiriro chiri mbali ya “chipatso cha mzimu.” Limatero pa Agalatiya 5:22, 23. Mwachionekere awo otsimikizira kukhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ayenera kukhala ndi mbali ya mzimu wake. Mpambo wapang’ono wa amuna ndi akazi a chikhulupiriro m’kati mwa nthawi zakale ukuperekedwa kwa ife mu Ahebri, chaputala cha khumi ndi chimodzi. Iwo amapanga mbali ya “mtambo waukulu kwambiri wa mboni wotizinga.” (Ahebri 12:1, NW) Mpambo wa mboni’wo ukubwerera m’mbuyo mpaka kwa mboni yoyambirira yosimbidwa ya Yehova Mulungu, ndiko kuti, Abele, mng’ono wa Kaini mwana wa Adamu ndi Hava. Panali mboni zina za Yehova m’kati mwa masiku amene’wo chisanachitika chigumula cha pa dziko lonse lapansi cha mu 2370-2369 B.C.E. Maina a mboni za chigumula chisanachitike za Mulungu Wam’mwamba-mwamba anaperekedwa mu Ahebri 11:4-7. Timawerenga kuti:

21 “Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, anagakhale adafa alankhulabe. Ndi chikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu anam’tenga: pakuti asanam’tenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu; koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akum’funa Iye. Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chiri monga mwa chikhulupiriro.”

22. Kuchokera m’zenizeni, kodi n’chifukwa ninji kuli koonekera bwino kuti ali yense wa antu atatu amene’wo anali ndi mbali ya mzimu woyera?

22 Abele, Enoke ndi Nowa akuchulidwa mwapadera cifukwa chakuti iwo anali opambana m’kusonyeza chikhulupiriro chao. Komabe, panali mkazi wa Nowa ndi ana amuna atatu ndi apongozi atatu amene analowa m’chingalawa limodzi ndi Nowa ndipo anapulumutsidwa chigumula cha pa dziko lonse lapansi. (1 Petro 3:19, 20) Abele ayenera kukhala anali ndi mbali yokulira ya mzimu woyera, pakuti iye anali ndi chimodzi cha zipatso zake, ndiko kuti, chikhulupiriro. Sipangakhale chikaikiro kuti Enoke mwana wa Yaredi naye’nso anali ndi mbali ya mzimu woyera, pakuti, mothandizidwa ndi zimene Yuda 14, 15 akutiuza, Mulungu anagwiritsira ntchito Enoke kupereka ulosi woyambirira wolembedwa wonenedwa ndi munthu. (Genesis 5:18-24) Nowa anagwiritsiridwa’nso ntchito monga mnereri wa Yehova. Iye anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5; Genesis 9:24-29) Kodi ndani amene angakane kuti Nowa anachita ntchito yapadera yolimba mtima pakati pa dziko la anthu opanda umulungu? Komabe, iye sanachite ntchito yolimba mtima imene’yi m’nyonga ya iye mwini. Kutseri kwake kunali mphamvu yogwira ntchito yoyera ya Mulungu.

23, 24. (a) Kodi ndi mkhalidwe wotani wa Mulungu umene unali kusonyezedwa pamene chingalawa cha Nowa chinali kumangidwa? (b) Malinga ndi kunena kwa Genesis 6:1-3, kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene Mulungu anapanga, ndipo chifukwa ninji?

23 M’nthawi ya Nowa mzimu wa Mulungu unali’nso kugwira ntchito kwa anthu. Nthawi ya kumanga chingalawa imene’yo inasonyezedwa ndi “kudekha kwa Mulungu.” (1 Petro 3:20) Mulungu anali kusonyeza kudziletsa kwakululu, chipiriro, kulola kumene’ku anthu opanduka kuti alape pamene iwo anaona kumangidwa kwa chingalawa kukuchitika ndipo anamva Nowa ‘akulalikira chilungamo.’ Koma kodi ndani amene analabadira ku ntchito ya mzimu wa Mulungu? Nowa yekha ndi mkazi wake ndi ana ao amuna Semu, Hamu ndi Yafeti limodzi ndi akazi ao atatu. Mulungu sanalinganize kupangira anthu zoyezayesa zapadera kosatha, akumayesayesa kunena kwake titero, kaamba ka iwo. Genesis 6:1-3 amatiuza chimene Mulungu anatsimikizira pa iwo ndi mikhalidwe ya pa dziko lapansi pansi pa imene iye anapanga chitsimikiziro ichi:

24 “Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka pa dziko lapansi, ndi ana akazi anawabadwira iwo, kuti ana amuna a Mulungu anayang’ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. Ndipo anti Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwo’nso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.”

25. Pamene nthawi inakwana, kodi Mulungu akachitanji kupatsa anthu chiyambi chatsopano?

25 Ukwati wa mitundu iwiri wolowerana wa “ana a Mulungu woona” obvala thupi ndi “ana akazi a anthu” umene’wo–ha, unali wobvutitsa maganizo chotani nanga! Kusintha kwa zinthu kotero’ko sikuyenera kupitirizabe popanda mapeto! Zimene’zo ndizo zimene Mulungu anatsimikizira. Chotero kwa zaka zana limodzi lokha ndi makumi awiri mzimu wake ukanatha kudzisonyeza modekha monga momwe unali kuchitira kwa anthu. Pamene nthawi inakwana, iye akadzetsa kusintha kwakululu kwambiri! Kudziletsa kwake kochitidwa kwa nthawi yaitali’ko kukachotsedwa. Maukwati olowerana a angelo auzimu obvala thupi ndi akazi a thupi akathetsedwa ndi chigumula cha pa dziko lonse lapansi chimene chikamiza ngakhale nsonga za mapiri! Akuyandama m’chingalawa chosalowa madzi, Nowa ndi banja lake la mtundu wa anthu loyera ndi losaipitsidwa likapyola bwino lomwe chigumula’cho, kupatsa mtundu wa anthu chiyambi chatsopano. Dziko la anthu opanda umulungu linene’lo silikaloledwa’nso kusautsa, kumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu. Iye sakawapanga kukhala osati n’kulangidwa.—Onani Aefeso 4:30; Yesaya 63:10; Ahebri 10:29.

26, 27. (a) Zaka zoposa mazana asanu ndi atatu Nowa atamanga chingalawa, kodi ndi ntchito ina yomanga yotani imene Mulungu anaichirikiza? (b) Kodi ndi motani m’mene chingalawa cha Nowa chinaliri pochiyerekezera ndi chihema chopatulika ndi bwalo lake?

26 Chotero mwa njira ya opulumuka a pfuko la anthu osakhala a mitundu yosiyana Mulungu anapatsa banja laumunthu chiyambi chatsopano ndi cholungama. Kaamba ka chifuno chimene’chi Mulungu anachirikiza ntchito ya Nowa ya kumanga. Zoposa zaka mazana asanu ndi atatu pambuyo pake Mulungu anachirikiza ntchito ina ya kumanga yofunika. Mu mpambo wa malamulo operekedwa kwa mneneri Mose pa Phiri la Sinai, Mulungu analamula kumangidwa kwa chihema chopatulika.

27 Pa chihema chopatulika chokomana’ko chimene’chi mafuko khumi ndi awiri a anthu a Mose, mtundu wa Israyeli, anayenera kukumanako mokhazikika ndi Mulungu wao, ndipo ansembe ake anayenera kutumikira m’kupereka nsembe zotetezera machimo kaamba ka mtundu wonse’wo. Chihema’cho ndi bwalo lake lomangidwira kumodzi sichinali nyumba yaikulu mofanana ndi m’mene chinaliri chingalawa cha Nowa. Chingalawa cha Nowa chinali cha ukulu wakuti chikanatha kulowetsamo mabwalo asanu ndi anai, mabwalo atatu a chihema ku chiri chonse cha zipinda zosanja zitatu za chingalawa cha Nowa. Kumangidwa kwa chingalawa cha Nowa kunafunikira luso la umisiri, limene Mulungu akanatha kulipereka kwa Nowa ndi ana ake amuna. Chihema cha Israyeli chinafunikira luso la umisiri wa ntchito za manja.

28. Kodi ndi motani m’mene kuliri koonekera bwino kuchokera mu Eksodo 31:1-6 kuti Mulungu anachirikiza kumangidwa kwa chinema ndi mzimu wake woyera?

28 Popeza kuti Mulungu analamula kumangidwa kwa chihema cha Israyeli cholambiriramo, iye anachirikiza kumangidwa kwake. Motani kwenikweni? Kaamba ka yankho tikutembenukira ku Eksodo 31:1-6 ndipo kuchulidwa kwa mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu:

“Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Taona ndaitana ndi kum’chula dzina lake, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda; ndipo ndam’dzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m’ntchito ziri zonse kulingirira ntchito zaluso kuchita ndi golidi ndi siliva ndi mkuwa, ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mtengo, kuchita ntchito ziri zonse. Ndipo Ine, taona, ndam’patsa Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m’mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe.”

Motero mmisiri waluso Bezaleli andzazidwa ndi mzimu wa Mulungu.

29, 30. (a) Kodi ndi kugwira ntchito kwa chiani kuchokera kwa Mulungu kumene kunachititsa kutsirizidwa kwa nyumba ya chihema m’nthawi yabwino? (b) Kodi ndi liti ndipo ndi motani m’mene Bezaleli ndi Aholiabu anaonera chibvomerezo cha Mulungu chikusonyezedwa pa ntchito yao?

29 Pokhala ndi mphamvu yanyonga yotero’yo yochokera ku Magwero a mphamvu yonse yaikulu kwambiri kutseri kwa ogwira ntchito’wo, kumangidwa kwa chihema chopatulika ndi za m’kati mwake zonse zinali zotsimikizirika kuchitidwa mpaka kutsiriza. Pofika pa mapeto a chaka cha mwezi wokhala zinthu zonse zinali zitakonzeka kuti zisonkhanitsidwe, ndipo chihema’cho chinali chokonzekera kuimikidwa. Eksodo 38:22, 23 amasimba ntchito yosangalatsa’yo, kuti: “Ndipo Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda, anapanga zonse zimene Mulungu adauza Mose. Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndipo’nso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.” Kwa Bezaleli ndi Aholiabu tsiku loyambirira la chaka cha mwezi wokhala (Nisan 1, 1512 B.C.E.) liyenera kukhala linali tsiku lokhutiritsa mtima. Pa tsiku limene’lo kunachitika kuti “kachisi wa chihema chokomana’ko” anaimikidwa molamulidwa ndi Yehova, ndipo Bezaleli ndi Aholiabu anaona chozizwitsa:

30 “Mtambo unaphimba chihema chokomana’ko, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kachisi’yo.” Umene’wu unali umboni kwa Bezaleli ndi Aholiabu wakuti iwo achita ntchito yao bwino ndi kuti Yehova anaibvomereza. Mzimu wake unali utagwira ntcito kupyolera mwa iwo.—Eksodo 40:1-34.

31, 32. (a) Kodi chihema chimene’cho chinatumikira chifuno cha Mulungu kwa utali wotani? (b) Kodi ndi motani m’mene kuliri koonekera kuti mzimu woyera unachirikiza kumangidwa ndi kutsirizidwa kwa kachisi wa Solomo?

31 Kachisi wa chihema chikomana’ko amene’yu anaima ndi kutumikira chifuno chake kwa zaka 485, kufikira Mfumu Solomo anatsiriza kumanga kachisi mu Yerusalemu mu 1027 B.C.E. ndi kum’tsegulira kaamba ka kulambiridwa kwa Mulungu.

32 Kumangidwa kwa kachisi amene’yu kochitidwa ndi Solomo mwana wa Davie kunali’nso ndi chichirikizo cha mzimu wa Mulungu, pakuti Davide analandira pulani ya kamangidwe ya nymba yatsopano imene’yi mouziridwa. Monga momwe 1 Mbiri 28:11-19 imalongosolera kuti: “Anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.” Pamene kachisi wamkulu amene’yu anatseguliridwa pa Phiri la Moriya m’Yerusalemu, Yehova anasonyeza chibvomerezo cha nyumba yatsopano yom’lambiriramo’yo: “Mtambo unadzaza nyumba’yi, ndiyo nyumba ya Yehova; ndipo ansembe sanakhoza kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambo’wo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.”—2 Mbiri 5:13, 14.

33. Kodi, nanga n’chiani chimene chiri kutseri kwa kulambiridwa koyera kwa Mulungu?

33 Chotero, tiyeni tikhale otsimikizira za chinthu chimodzi chofunika kwambiri ichi: Mzimu woyera uli kutseri kwa kulambiridwa koyera kwa Yehova. Uli wokangalika mwamphamvu kwa awo amene amachita ndi kuchirikiza kulambira kopanda uchisi kwa Mulungu mmodzi woona. Zitsanso za chimene’chi zinadzisonyeza m’kati mwa nthawi imene oweruza osankhidwa mwapadera analamulira Israyeli m’Dziko Lolonjezedwa.

NCHITO YAKE YOSONKHEZERA PAMENE OWERUZA ANALAMULIRA

34. Kodi ndi motani mmene mzimu woyera unagwirira ntchito kupyolera mwa Woweruza Otiniyeli?

34 Chifukwa cha kupatuka pa kulambira koyera, Aisrayeli analowa mu ulamuliro wotsendereza wa mfumu ya Asuri. “Ndipo pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israyeli mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyeli mwana wa Kenazi, mng’ono wake wa Kalebe.” Kodi n’chiani chimene chinachitika tsopano? “Ndipo unam’dzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israyeli, natuluka kunkhondo; napereka Yehova KusaniRisataimu mfumu ya Mesapotamiya m’dzanja lake; ndi dzanja lake linam’laka KusaniRisataimu. Pamenepo dziko linapumula zaka makumu anai.”—Oweruza 3:9-11.

35.Kodi ndi motani m’mene mzimu woyera unagwirira ntchito m’chochitika cha Woweruza Gideoni?

35 M’kupita kwa nthawi mikhalidwe inafika pakuti inafunikiritsa Yehova kudzutsa woweruza wina woti apulumutse anthu ake Israyeli. “Amidyani onse ndi Aameleki ndi ana a kum’mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m’chigwa cha Yezreeli. Koma mzimu wa Yehova unabvala Gideoni; naomba lipenga iye,” ndi banja la Abieziri analalikidwa kum’tsata iye. (Oweruza 6:33, 34) Mwa kugwiritsira ntchito munthu wachikulupiriro amene’yu, Yehova anapereka chipambano chapadera wa anthu ake, chipambano chimene chikuchulidwa m’mbiri ya Baibulo ya pambuyo pake.—Yesaya 9:4-6; Salmo 83:9-12; Ahebri 11:32, 33.

36.Kodi mzimu woyera unachitanji kupyolera mwa Woweruza Yefita?

36 Mobwerezabwereza mphamvu yogwira ntchito yoyera yochokera kwa Yehova inagwira ntchito kaamba ka anthu a chikhulupiriro amene Iye anawagwiritsira ntchito kuchita zinthu zochuka mu mbiri. Nthawi’yo inali pameneAisrayeli otsenderezedwa’wo anayenera kuyang’anizana ndi Aamoni audani’wo m’nkhondo. “Mzimu wa Yehova unam’dzera Yefita, napitira iye ku Gileadi kwa ana a Amoni.” Wofunitsitsa chipambano motamanda Yehova, Woweruza Yefita anapanga chowinda chimene chinatsimikizira kukhala cha mtengo waukulu kwa iye. Chotero Yehova anam’ gwiritsira ntchito kugonjetsa a Amoni.—Oweruza 11:29 kufikira 12:7.

37. Kodi Yehova anaukitsa yani kuti alanditse Aisrayeli m’manja mwa Afilisti, ndipo mwa njira ya chiani?

37 Zaka zina pambuyo pake, Afilisti anakhala otsendereza mwapadera kwa Aisrayeli. Chotero Mulungu anachititsa kubadwa kwa munthu wodabwitsa wochedwa Samsoni. Iye anayenera “kutsogolera m’kupulumutsa Israyeli m’manja mwa Afilisti.” Kaamba ka chifuno chimene’cho, mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu inam’chirikiza. “M’nthawi yake mzimu wa Yehova unayamba kum’ sonkhezera m’Mahanehdan pakati pa Zora ndi Esitaoli.” Chotero sikunali mwa mphamvu zakuthupi za Samsoni kuti iye anasonyeza nyonga yaikulu kopambana yoposa munthu wina ali yense amene anakhalako pa dziko lapansi kufirira tsopano.—Oweruza 13:5, 25, NW.

38. Kodi Samsoni anachitanji pamene anakumana ndi mkango wothuluma, ndipo kodi ndi motani m’mene anathetsera nkhani pamene Afilisti anacita mosayenera m’kumasulira mwambi wake?

38 Pa nthawi ina, pamene Samsoni anali kuyenda yekha, mwadzidzidzi anaonekera pamaso pake “mwana wa mkango wakomana naye nam’dzumira.” Kodi Samsoni wopanda chida’yo zinamuyendera motani? “Ndipo unam’gwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung’amba monga akadang’ amba mwana wa mbuzi, wopanda kanthu m’dzanja lake.” Mwamsanga pambuyo pake Afilisti anam’ nyenga pa mwambi’wo kotero kuti amuonongetse chuma chochuluka. Zimene’zi zinabwerera Afilisti. Kachiwiri’nso, “mzimu wa Yehova unam’gera Samsoni, natsikira iye kwa Asikeloni [m’Filistia], nawakantha amuna makumi atatu, natenga zobvala zao, nawapatsa okumika mwambi’wo.”—Oweruza 14:5-19.

39. Kodi n’chiani chimene chinachitika pamene Aisrayeli anapereka Samsoni, atamangidwa ndi zingwe zatsopano, kwa Afilisti?

39 Ngakhale zingwe zatsopano sizinatsimikizire kukhala kantu kali konse kamphamvu kwambiri kwa Samsoni pamene iye anali kuperekedwa, womangidwa, kwa Afilisti oipidwa’wo. “Mzimu wa Yehova unam’gwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga bwazi lopsyerera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyonyotsoka pa manja ake. Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha buru, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi.”—Oweruza 15:11-15.

40, 41. Kodi ndi motani m’mene Samsoni anaphera anthu ambiri pa imfa yake koposa amene iye anawapha m’kati mwa kuweruza kwake Israyeli?

40 Nchito yaikulu kopambana ya Mulungu mwa njira ya Samsoni motsutsana ndi olambira mulungu wonyenga Dagoni Achifilisti inali yotsirizira. Inasonyeza kuti mzimu wa Mulungu sumatopa ndi kufooka.

41 Ataperekedwa ndi mkazi’yo Delila ndi kuboolewa maso ndi Afilisti obwezera’wo, Samsoni anaima pakati pa mizati iwiri m’kachisi wa Dagoni pa Gaza, Filistia. Pa malo apakati amene’wo “Samsoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzake ndi dzanja lamanzere. Nati Samsoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m’mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo.”—Oweruza 16:23-30.

42. Kodi dzina la Samsoni likugwirizanitsidwa ndi yani mu Ahebri 11:32-34?

42 Samsoni akuikidwa pakati anthu a m’nthawi zakale amene’wo amene anali ndi chikhulupiriro chimene’cho mwa Mulungu chimene chiri chipatso cha mzimu Wake. “Ndipo ndinene chiani’nso?” Akufunsa motero wolemba bukhu la Ahebri m’chaputala cha khumi ndi chimodzi, Ndipo akuyankha kuti: “Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita; za Davide, ndi Samueli ndi aneneri; amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa mikango, nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofoka, anakula mphamvu kunkhondo, anapitikitsa magulu a nkhondo yachilendo.”—Ahebri 11:32-34.

WODZOZEDWA WA YEHOVA

43. Kodi ndi kusintha kotani kumene kunachitika kwa Davide kuyambira pamene Samueli anam’dzoza ndi mafuta pa Betelehemu?

43 Dzina lapadera limene wolemba Ahebri akuchula ndiro lija la Davide mwana wa Jese wa Betelehemu. Pamene iye anali mbusa wachinyamata, Davide anadzozedwa ndi mafuta ndi mneneri Samueli kukhala woyembekezera kukhala mfumu ya mafuko khumi ndi awiri onse a Israyeli. Kodi ndi chiani chimene chinatsatirapo mwamsanga pambuyo pa kudzozedwa kwake? “Mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomwe’li. Ndipo Samueli ananyamuka, namka ku Rama. [Ndipo] mzimu wa Yehova unam’chokera Sauli [mfumu yomalamulira pa nthawi’yo].” (1 Samueli 16:13, 14) Potsirizira pake Mfumu yosakhulupirika Sauli motaya mtima inatembenukira kwa wobwebweta, kum’chititsa kulankhula ndi akufa, ngati n’kotheka. Mwamsanga pambuyo pake iye anafera m’nkhondo ndi Afilisti.

44. Kodi n di motani m’mene Mulungu anachitira ndi Davide Mfumu Sauli atafera m’nkhondo?

44 Koma ponena za Davide, iye anayamba kulowa ufumu umene iye anadzodzedwera ndi Samueli. Mulungu amene iye anam’lambira mwamphamvu anam’patsa mphamvu ya kulanda zofunkha, ngakhale ya kugonjetsa Dziko Lolonjezedwa. Osati zokha’zo, koma Mulungu anamuuzira kunena ndi kulemba ulosi. Iye anakhala mneneri woona: Chotero “kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kulankhula mwa m’kamwa mwa Davide.”—Machitidwe 1:16; 4:24, 25.

45. Kamba ka ntchito za chikhulupiriro zonse zimene’zo kodi thamo likupita kwa yani, ndipo, motsimikizira mau ake m’Zekariya 4:6, kodi n’chochitika chotani chimene Zerubabele ndi Mkulu wa Ansembe Yoswa anasangalala nacho?

45 Kaamba ka ntchito zonse zodabwitsa zochitidwa ndi anthu a m’nthawi zakale amene’wo thamo liyenera kupita kwa Mulungu wa nyonga yaikulu kwambiri yosatha. Ntchito zorero’zo zimaphatikizamo kulembedwa kwa mabukhu a Malemba ouziridwa makumi atatu mphambu asanu ndi anai Achihebri, kuyambira pa Genesis kufikira ku Malaki, M’bukhu lolosera la Zekariya mau olimbikitsa akuperekedwa kwa Bwanamkubwa Zerubabele, amene anapatsidwa kuyanga’anira kumangidwa’nso kwa kachisi pa Yerusalemu amene anali ataonongedwa ndi Ababulo mu chaka cha 607-B.C.E. Mau a kwa omanga kachisi’wo anali kuti: “Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.” (Zekariya 4:6) Pochirikizidwa ndi kanthu kena kamphamvu kwambiri koposa gulu la nkhondo kapena mphamvu yakuthupi, Bwanamkubwa Zerubabele ndi wantchito mnzake, Mkulu wa Ansembe Yoswa, anayanga’anizana molimba ntima ndi malo a mdani ndipo chotero anali ndi mwai wa kuchita phwando la kumalizidwa kwa kumangidwa’nso kwa kachisi wa Yehova pa Yerusalemu m’chaka cha 515 B.C.E.

KUONERATU ZOCHITA ZA NTHAWI ZATHU

46. Kodi ndi motani m’mene ntchito za anthu zimene’zo zochititsidwa ndi mzimu woyera ziriri zoposa zenizeni za mu mbiri chabe?

46 Mau a chilimbikitso kwa Zerubabele anaperekedwa mouziridwa zaka zoposa mazana asanu Nyengo yathu Ino isanakhale. Komabe liri latanthauzo’di kwa ife lero lino monga momwe linaliri kale’lo m’nthawi ya Zekariya. Kodi n’chifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa chakuti timakhulupirira mwa Yehova monga Magwero Aumulungu a mphamvu yaikulu kwambiri yoposa yaumunthu. Ntchito zolimba mtima ndi zachikhulupiriro zimene Mulungu Wamphamvuyonse anazichita mwa kachitidwe ka mzimu wake woyera pa amuna ndi akazi a m’nthawi zakale ziri osati zenizeni za mu mbiri chabe. Izo zinali’nso kuoneratu zochita zimene Iye adzazichita kuyambira pa nthawi ya Mesiya wake, Wodzozedwa wake, kumkabe m’tsogolo, ngakhale kufikira ku mbadwo wathu.

47, 48. (a) Kodi Mesiya wonenedweratu’yo anasonyezedwa ndi munthu wobadwa mwachilendo uti? (b) Kodi kalambule bwalo wa Mesiya anayenera kudzazidwa chiyani kuyambira m’mimba mwa amake kumkabe m’tsogolo, ndipo kodi iye akachitanji?

47 Mesiya wonenedweratu’yo anadziwikitsidwa zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo ndi munthu wina amene kubadwa kwake kwenikweni nako’nso kunali kodabwitsa. Kubadwa kwake sikunali mwa njira yachibadwa ya mphamvu za kubala ya atate wake ndi amai wake. Iwo pa nthawi imene’yo anali atapitirira usinkhu wa kubala ana. Mphamavu zao za kubala zinayenera kudzutsidwa’nso m’malo mwakuti abale mwana wao mmodzi yekha, mwana wamwamuna amene atate’yo, wansembe Zekariya, akadadzam’cha Yohane.

48 M’kusimba za mwana wamwamuna wokhumbidwa kwambiri’yo mngelo Gabrieli anati kwa Zekariya pa kachisi: “[Adzadzazidwa] ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe. Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wao. Ndipo adzam’tsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya Atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.”—Luka 1:5-17; yerekezerani ndi Malaki 4:5, 6.

49. Chotero, kodi Mesiya weniweni anayenera kudzisonyeza yekha kapena kusonyezedwa, ndipo motani?

49 Pokhala wosonyezedwa ndi kalambule bwalo wotero’yo, Mesiya weniweni sanayenera kukhala munthu wina wokhumbira malo amene akaziyerekezera kukhala Mesiya ndi amene akadzilengeza kwa mtundu wa Israyeli ndi kumka nadzilengeza kotero kuti akakope gulu la atsatiri. (Yesaya 42:2-4) M’malo mwake, iye akasonyezedwa moyenerera kwa ofunafuna Mesiya ndi munthu wotumizidwa ndi Mulungu ndi wokhala ndi chichirikizo cha Mulungu.—Yesaya 40:3-5; Yohane 1:6, 7.

50. Kodi Yoweli 2:28-32 akunena kuti n’chiani chimene chikachitika Mesiya atadza?

50 Mesiya atadza ulosi wosonkhezera’wo wa Yoweli 2:28-32 unayenera kukwaniritsidwa:“Ndipo kudzachitika m’tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu amuna ndi akazi adzanenera, akulu akulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya; ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo. Ndipo ndidzaonetsa zodabwiza kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsya. Ndipo ku-dzachitika kuti ali yense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m’phiri la Ziyoni ndi m’Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehovah adzawaitana.”

51. (a) Polingalira ulosi wa Yoweli, kodi ndi mafunso otani amene ali abwino kwambiri kwa ife kuwafunsa? (b) Kodi n’chifukwa ninji tsopano munthu ayenera kuitanira pa dzina la Yehova?

51 Tsopano ndi nthawi yabwino kwambiri ya kufunsa kuti, Kodi ndani amene ali anthu amene akulandira zimene Yehova analonjeza kutsanulira pa thupi liri lonse? Pansi pa mphamvu yosonkhezera ya chimene chikutsanuliridwa anthu otero’wo ayenera kunenera. Kunenera kwao kuli kwa panthawi yake popeza kuti kuyenera kuyambirira ndi kuneneratu “lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsya.” Anthu amene amalabadira kunenera kotero’ko angadzipeze ali pakati pa anthu opulumuka’wo. Iwo angakhale pakati pa “opulumuka.” Ngati tipenda mwa mikhalikwe yonse ya nthawi yathu chiyambire 1914 C.E, “tsiku la Yehova “limene liri patsogolo pathupa limasonyeza kukhala’di “lalikulu ndi loopsya.” Kodi timakhumba ‘kupulumuka bwino lomwe’? Ngati chimene’cho chiri chikhumbo chathu, pamenepo kukukhala kwanzeru kwa ife ‘kuitanira pa dzina la Yehova,’ Uyo amene mzimu wake uli kutseri kwa dongosolo latsopano likudza’lo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena