-
Babulo WamkuluKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa anthu amene sanadziŵe chowonadi cha Baibulo koma amene anakhala ndi moyo nafa kaleromonga mbali ya Babulo Wamkulu?
Mac. 17:30: “Nthaŵi za kusadziŵako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima.”
Mac. 24:15: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Kuti ndianthu “osalungama” ati amene adzaukitsidwa, Mulungu adzasankha.)
Yobu 34:12: “Ndithudi zowonadi, Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.”
-
-
BaibuloKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Baibulo
Tanthauzo: Mawu olembedwa a Yehova Mulungu kwa anthu. Anagwiritsira ntchito alembi aumunthu okwanira 40 mkati mwa nyengo ya zaka mazana 16 kulilemba, koma Mulungu mwiniyo anatsogoza kwenikweni kulembedwako mwa mzimu wake. Chotero liri louziridwa ndi Mulungu. Mbali yaikulu ya cholembedwacho njopangidwa ndi mawu enieni onenedwa ndi Yehova ndi malongosoledwe onena za ziphunzitso ndi ntchito za Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Mmenemu timapezamo mawu onena za malamulo a Mulungu kaamba ka atumiki ake ndi zimene adzachita kukwaniritsa chifuno chake chachikulu kaamba ka dziko lapansi. Kuti azamitse chiyamikiro chathu kaamba ka zinthu zimenezi, Yehova anasunganso m’Baibulo cholembedwa chosonyeza zimene zimachitika pamene anthu ndi mitundu amvetsera Mulungu ndi kugwira ntchito mogwirizana ndi chifuno chake, kudzanso chotulukapo pamene ayenda m’njira ya iwo eni. Kupyolera mwa cholembedwa cha m’mbiri chodalirika chimenechi Yehova amatidziŵitsa ntchito zake ndi anthu ndipo motero ndi umunthu wake wodabwitsa.
Zifukwa zophunzirira Baibulo
Baibulo lenilenilo limati nlochokera kwa Mulungu, Mlengi wa anthu
2 Tim. 3:16, 17: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”
Chiv. 1:1: “Chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achiwonetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa.”
2 Sam. 23:1, 2: “Atero Davide mwana wa Jese . . . mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mawu ake anali pa lilime langa.”
Yes. 22:15: “Atero Ambuye Yehova wamakamu.”
Tikayembekezera uthenga wa Mulungu kwa anthu onse kukhala wopezeka kuzungulira dziko lapansi. Baibulo, lathunthu kapena mbali yake, latembenuzidwira m’zinenero zokwanira 1 800. Kufalitsidwa kwake, kukufikira mabiliyoni ambiri. The World Book Encyclopedia imati: “Baibulo ndiro bukhu loŵerengedwa mofala koposa mabukhu onse m’mbiri. Mwinamwake lirinso lachisonkhezero kuposa onse. Makope ochulukirapo a Baibulo agaŵiridwa kuposa a bukhu lina lirilonse. Latembenuziridwanso m’zinenero zochulukirapo kuposa bukhu lina lirilonse.”—(1984), Vol. 2, p. 219.
Ulosi wa Baibulo umalongosola tanthauzo la mikhalidwe ya dziko
Atsogoleri adziko ambiri amavomereza kuti mtundu wa anthu uli pa mphembenu pa tsoka. Baibulo lidaneneratu mikhalidwe imeneyi kalekale; limalongosola tanthauzo lake ndi chimene chidzakhala chotulukapo chake. (2 Tim. 3:1-5; Luka 21:25-31) Limasimba zimene tiyenera kuchita kuti tipulumuke chiwonongeko choyandikiracho chadziko, kuti tikhale ndi mwaŵi wa kupeza moyo wamuyaya m’mikhalidwe yolungama pano padziko lapansi.—Zef. 2:3; Yoh. 17:3; Sal. 37:10, 11, 29.
Baibulo limatikhozetsa kuzindikira chifuno cha moyo
Limayankha mafunso onga akuti: Kodi moyo unachokera kuti? (Mac. 17:24-26) Kodi nchifukwa ninji tiri pano? Kodi ndiko kokha kuti tikhale ndi moyo zaka zoŵerengeka, kupeza zimene tingathe m’moyo, ndiyeno nkufa?—Gen. 1:27, 28; Aroma 5:12; Yoh. 17:3; Sal. 37:11; Sal. 40:8.
Baibulo limasonyeza mmene tingakhalire ndi zinthu zenizenizo zimene okonda chilungamo amakhumba koposa
Limatiuza kumene tingapeze atsamwali abwino amene amakondanadi wina ndi mnzake (Yoh. 13:35), chimene chingatipatse chitsimikiziro chakuti tidzakhala ndi chakudya chokwanira kaamba ka ife eni ndi mabanja athu (Mat. 6:31-33; Miy. 19:15;
-