Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Dziko
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • ena apereke ulemerero kwa Mulungu chifukwa cha zimene Akristu amachita, kuli kwachiwonekere kuti awo amene ali Akristu ayenera kukhala mboni zokangalika kudziko ponena za dzina la Mulungu ndi chifuno. Iri ntchitoyi imene Akristu owona amagogomezera kwakukulu.)

      Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mikhalidwe yamakono yadziko?

      Wonani mutu waukulu wakuti “Masiku Otsiriza.”

  • Dziko Lapansi
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Dziko Lapansi

      Tanthauzo: Liwu lakuti “dziko lapansi” limagwiritsiridwa ntchito kuposa mu lingaliro limodzi m’Malemba. Kaŵirikaŵiri timaganiza za ilo kukhala likusonya kuplaneti lenilenilo, limene Yehova mokoma mtima anakongoletsa kotero kuti lichirikize moyo wa anthu ncholinga cha kupangitsa miyoyo yathu kukhala yokhutira molemerera. Komabe, kuyenera kudziŵika, kuti “dziko lapansi” lingagwiritsiridwenso ntchito mu lingaliro lophiphiritsira, mwachitsanzo, kunena, za anthu okhala paplaneti lino kapena ku chimangidwe cha anthu chimene chiri ndi zizoloŵezi zakutizakuti.

      Kodi planetili dziko lapansi lidzawonongedwa m’nkhondo yanyukliya?

      Kodi Baibulo limasonyeza kuti nchiyani chimene chiri chifuno cha Mulungu ponena za dziko lapansi?

      Mat. 6:10: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”

      Sal. 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”

      Wonaninso Mlaliki 1:4; Salmo 104:5

      Kodi pali kuthekera kwakuti, popeza kuti mitundu ikusonyeza nkhaŵa yochepa kaamba ka chifuno cha Mulungu, kuti angawononge kotheratu dziko lapansi mwa njira ina yake kwakusankhoza kukhalika?

      Yes. 55:8-11: “[Ati Yehova:] Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu. . . . Mawu anga . . . sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”

      Yes. 40:15, 26: “Tawonani, [kwa Yehova Mulungu] amitundu akunga dontho la mu mtsuko, naŵerengedwa ngati fumbi losalala la m’miyeso. . . . Kwezani maso anu kumwamba, muwone [dzuŵa, mwezi ndi mabiliyoni anyenyezi] amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” (Mphamvu yanyukliya yopangidwa ndi amitundu njochititsa mantha kwa anthu. Koma mabiliyoni ambiri anyenyezi amapambana mphamvu yanyukliya pamlingo wooti maganizo athu ngwosakhoza kuzindikira. Kodi ndani amene analenga ndi amene amalamulira makamu onse akumwamba awa? Kodi Iye sangalepheretse amitundu kugwiritsira ntchito zida zankhondo zanyukliya mwanjira imene ikanalepheretsa chifuno chake? Kuti Mulungu angachite zimenezo kwafotokozedwa mwafanizo mwa kuwononga kwake magulu ankhondo amphamvu a Igupto pamene Farao anafunafuna kuletsa chilanditso cha Israyeli.—Eks. 14:5-31.)

      Chiv. 11:17, 18, NW: “Tikuyamikani, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli ndi amene munali, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu ndi kuyamba kulamulira monga mfumu. Koma mitundu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika, ndi nthaŵi yoikidwiratu . . . kuwononga awo owononga dziko lapansi.”

      Kodi Mulungu mwiniyo adzawononga dziko lapansi ndi moto?

      Kodi 2 Petro 3:7, 10 akuchirikiza lingaliro iri? “Miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko [“kuwonongeka,” RS] cha anthu osapembedza. . . . Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa [“wotchedwa (kunyeketsedwa),” RS, JB; “zidzazimiririka,” TEV; “zidzasonyezedwa,” NAB; “zidzavumbulutsidwa,” NE; “zidzatulukiridwa,” NW].” (Tamverani: Ma Codex Sinaiticus ndi Vatican MS 1209, onse a m’zaka za zana la 4 C.E., amati “kutulukiridwa.” Malembo apamanja apambuyo pake, otchedwa Codex Alexandrinus a m’zaka za zana la 5 ndi a m’zaka za zana la 16 opendedwa ndi Clementine a Vulgate amati “zidzawotchedwa.”)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena