Lingaliro la Baibulo
Kodi Kudzimana Konyanya Ndiyo Njira Yopezera Nzeru?
“ANTHU odzipatula anavala matangadza, maunyolo, malamba amingaminga ndiponso zovala mkhosi zamingaminga . . . Ena ankagubuduzika pa minga ndi zomera zina zobaya, kudzilumitsa dala ku tizilombo, kudzitentha ndi moto ndi kunyeketsa zilondazo mpaka zitachita mafinya. Mwambo wawo unali kudya chakudya pang’ono, ena amaposerapo mwa kumadya zoola zokhazokha kapena zakudya zina zonyansa.”—The Saints, lolembedwa ndi Edith Simon.
Ameneŵa anali anthu odzimana. Kodi nchifukwa ninji ankadzizunza okha choncho? M’buku lakuti For the Sake of the World—The Spirit of Buddhist and Christian Monasticism, alembi ake akulongosola kuti “makamaka kuyambira nthaŵi ya Socrates (m’zaka za zana lachisanu B.C.E.) anthu ambiri anali kukhulupirira kuti moyo wongokhala ndi zofunika zokha, wosacholoŵana ndi zosangalatsa thupi ndi chuma, ndiwo unali njira yopezera nzeru yeniyeni.” Odzimanaŵa anali kukhulupirira kuti kusautsa thupi lawo kudzawonjezera njala yawo yauzimu ndi kuwapatsa chidziŵitso chenicheni.
Nzovuta kupereka tanthauzo lomvekera bwino la kudzimana konyanya. Kwa ena, zimangotanthauza kudziletsa kapena kudzikana. Akristu oyambirira ankaona khalidwe lotero monga loyenera. (Agalatiya 5:22, 23; Akolose 3:5) Yesu Kristu mwiniyo analimbikitsa moyo wosafuna zambiri, wosacholoŵana chifukwa cha nkhaŵa zimene moyo wokonda chuma umabweretsa. (Mateyu 6:19-33) Komabe, anthu kaŵirikaŵiri amaganiza kuti kudzimana konyanya ndiko kutsata njira yodzikhaulitsa kwambiri ndiponso yonkitsa nthaŵi zambiri, monga zomwe zanenedwa pamwambazo. Kodi machitidwe akudzimana konyanya ameneŵa, makamaka onkitsa kwambiriwo, ndiwodi njira yopezera nzeru?
Kozikidwa pa Zikhulupiriro Zabodza
China mwa ziphunzitso zomwe zayambitsa kudzimana konyanya ndilo lingaliro lakuti chuma ndiponso zinthu zosangalatsa thupi nzoipa mwachibadwa, choncho zimapinga kupita patsogolo kwauzimu. Ganizo lina lomwe limayambitsa kudzimana konyanya ndi chikhulupiriro chakuti munthu ali ndi thupi ndi sou. Anthu odzimana amakhulupirira kuti thupi loonekali ndi ndende ya sou ndi kuti thupilo ndi mdani wake.
Kodi Baibulo limanena chiyani? Malemba amasonyeza kuti pamene Mulungu anatsiriza kulenga dziko lapansi, anati zonse zomwe anali atapanga—zinthu zonse zooneka zomwe analenga—zinali “zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Mulungu ankafuna kuti mwamuna ndi mkazi azisangalala ndi zinthuzo m’munda wa Edeni. Dzina lenilenilo Edene limatanthauza “Chisangalalo” kapena “Kukondwera.” (Genesis 2:8, 9) Adamu ndi Hava anali angwiro ndipo anali paunansi wabwino ndi Mlengi wawo kufikira pamene anachimwa. Kuyambira nthaŵi imeneyo kumka mtsogolo, kupanda ungwiro kunakhala chopinga pakati pa Mulungu ndi munthu. Komabe, kukhutiritsa zikhumbo zoyenera za munthu kapena kusangalala ndi zinthu zakuthupi zokondweretsa zomwe Mulungu anapereka mogwirizana ndi malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino sikungamlepheretse Mulungu kumvana ndi olambira ake!—Salmo 145:16.
Ndiponso, Baibulo limaphunzitsa bwino kuti munthu, pokhala analengedwa kuchokera kunthaka ndipo anapangidwa wa thupi, ndiye sou. Malemba savomereza ganizo lakuti sou ndi chinthu chosagwirika chosafa kaya chotsekeredwa mkati mwa thupi kapenanso ganizo lakuti thupi limalepheretsa munthu kuti asakhale ndi ubwenzi wolimba ndi Mulungu.—Genesis 2:7.
Nzoonekeratu kuti chiphunzitso cha kudzimana konyanya chimapereka chithunzi cholakwika cha ubwenzi wa munthu ndi Mulungu. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti ena odzinenera kukhala Akristu adzakonda ziphunzitso zonyenga za anthu m’malo mwa choonandi cha m’Baibulo chofunika kwambiri. (1 Timoteo 4:1-5) Ponena za ena amene anali ndi ganizo limeneli, wolemba mbiri yakale yachipembedzo anati: “Chikhulupiriro chakuti zinthu zooneka ndi zauchimo . . . ndi kuti sou ya anthu iyenera kumasulidwa ku maunyolo a thupi, chinayambitsa kudzimana konyanya koopsa koletsa kudya nyama, kugonana, ndi zina zotero, zimene zikanatha kutsatiridwa ndi anthu oŵerengeka okha ‘angwiro’ kapena kuti perfecti amene anachita mwambo wapadera.” Kalingaliridwe kameneka kalibe umboni wa m’Baibulo ndipo si zimene Akristu oyambirira anakhulupirira.—Miyambo 5:15-19; 1 Akorinto 7:4, 5; Ahebri 13:4.
Kudzimana Konyanya Nkosafunika
Yesu ndi ophunzira ake sanali odzimana. Anapirira ziyeso ndi zizunzo zosiyanasiyana, koma sanali kudzizunza okha. Mtumwi Paulo anachenjeza Akristu kuti ayenera kusamala kuopera kuti angakopeke ndi ziphunzitso zonyenga za anthu ndi kusiya choonadi cha m’Mawu a Mulungu ndi kuwachititsa zinthu zosayenera, zonkitsa. Paulo anatchula za “kusalabadira thupi.” Iye anati: “Zimene zili nawotu manenedwe a nzeru m’kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.” (Akolose 2:8, 23) Kudzimana konyanya sikumapatsa munthu chiyero chapadera kapena chidziŵitso.
Kunena zoona, kumvera kwachikristu kumafuna kuyesetsa mwakhama ndi kudzilanga. (Luka 13:24; 1 Akorinto 9:27) Munthu ayenera kuchita khama kuti apeze chidziŵitso cha Mulungu. (Miyambo 2:1-6) Komanso, Baibulo lili ndi machenjezo amphamvu oletsa kuchitira ukapolo “zilakolako ndi zokondweretsa,” ndiponso kukhala “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (Tito 3:3; 2 Timoteo 3:4, 5) Komabe, ndime za m’Malemba zimenezi sizimavomereza machitidwe a kudzimana konyanya. Yesu Kristu, munthu wangwiro, anali ndi nthaŵi yosangalala yomwe inaphatikizapo kudya, kumwa, nyimbo ndi kuvina.—Luka 5:29; Yohane 2:1-10.
Nzeru yeniyeni njabwino, yosalira kupambanitsa zinthu. (Yakobo 3:17) Yehova Mulungu analenga matupi athu ndi mphamvu yosangalala nazo zokondweretsa zambiri m’moyo. Amafuna kuti ife tizikhala osangalala. Mawu ake amatiuza kuti: “Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”—Mlaliki 3:12, 13.
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
Saint Jerome in the Cavern/The Complete Woodcuts of Albrecht Dürer/Dover Publications, Inc.