Kudziŵikitsa Dzina la Yehova M’dziko Lonse
1 Pamene Yesu amauza ophunzira ake kukhala Mboni “kufikira malekezero ake a dziko,” anali atawasonyeza kale chitsanzo chakuti iwo atsatire. (Mac. 1:8) Nthaŵi iliyonse ndiponso paliponse pamene anapeza anthu, analankhula za chifuno cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu. Potsanzira Yesu, kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kakugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ‘kudziŵikitsa [dzina la Yehova] m’dziko lonse.’—Yes. 12:4, 5.
2 Zimene Zimachitika Masiku Akale: M’zaka za m’mbuyomo, ulaliki unali kufalitsidwa m’manyuzipepala; anakonza Seŵero la Pakanema la Chilengedwe ndipo anaonetsa anthu ambiri zedi; anagwiritsanso ntchito galimoto zokhala ndi zokuzira mawu; ndiponso anagwiritsa ntchito kwambiri galamafoni, ndipo kwanthaŵi yochepa anagwiritsa ntchito wailesi. Amachita zonsezi n’cholinga cholalikira uthenga wabwino. Ndithudi, zimene zagogomezedwa nthaŵi zonse ndi kukumana ndi anthu mwachindunji kotero kuti tithe kukulitsa chidwi chimene tapeza. Chotero, utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndiwo wakhala njira yabwino kwambiri podziŵikitsa dzina la Yehova kulikonse.—Mac. 5:42.
3 Zimene Zikuchitika Masiku Ano: Chifukwa cha kusintha kwa nthaŵi, dziko likusinthanso kwambiri, ndipo m’malo ambiri anthu sapezekapezeka panyumba. Anthu ochepa ndiwo amapeza nthaŵi yoŵerenga ndi kusinkhasinkha pa zinthu zauzimu. Tiyenera kusintha utumiki wathu mogwirizana ndi zimenezo. Kuphatikiza pa kupitiriza kufola gawo mwa kupita ku nyumba ndi nyumba, timalimbikitsidwa kupita komwe kuli anthu ndiponso kukhala “okonzeka nthaŵi zonse” kuchita chodzikanira cha chiyembekezo chili mwa ife. (1 Pet. 3:15) Izi zikutanthauza kuyesetsa kulalikira kwa anzathu ogwira nawo ntchito, anzathu akusukulu, anthu oyenda mumsewu ndi poimikapo galimoto, kusitolo ndi sitolo, ndi kulikonse komwe kungapezeke anthu. Popeza Yehova akutichirikiza, zoyesayesa zathu zimayenda bwino. Kodi muli m’gulu lofikira anthu kulikonse kumene angapezeke?
4 Tiyenitu aliyense payekha achite zotheka podziŵikitsa dzina la Yehova m’gawo lathu. Tingapeze chikhutiro chochuluka pokwaniritsa utumiki wathu, pamene tikudikira Yehova kukoka anthu a mtima woongoka.—Yoh. 6:44.