Gwiritsani Ntchito Mabuku Athu Mwanzeru
1 Kugwiritsa ntchito kwathu mabuku mwadongosolo kunayamba ndi kugaŵira makope okwanira 6,000, a magazini a Nsanja ya Olonda a July 1, 1879. Kuyambira nthaŵi imeneyo, mabuku osiyanasiyana ambiri zedi akhala akusindikizidwa komanso kufalitsidwa m’ziŵerengero zikuluzikulu.
2 Makonzedwe a Zopereka Zaufulu: Mu November 1999, kunafotokozedwa kuti magazini ndi mabuku aziperekedwa kwa ofalitsa ndi anthu achidwi mwanjira ya zopereka zaufulu, kutanthauza kuti, sazipemphedwa kapena kuuzidwa mtengo wa ndalama zoti apereke akafuna mabuku. Pamene tagaŵira mabuku, tidzalandira zopereka zaufulu zochirikizira ntchito ya padziko lonse yofalitsa uthenga wabwino. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova adalitsa makonzedwe ameneŵa.—Yerekezani ndi Mateyu 6:33.
3 Mmene Tidzichitira M’munda: Tipitiriza kuchitira umboni monga mwa nthaŵi zonse ndiponso tidzigaŵira zofalitsa kwa anthu achidwi kuti apeze chidziŵitso chambiri pa nkhani imeneyo. Ngati sakusonyeza chidwi, palibe chifukwa chowapatsira mabuku. Sitikufuna kuwononga lililonse la mabuku athu mwa kugaŵira anthu amene alibe chidwi. Koma, pamene mwininyumba wasonyeza chidwi ndipo wavomera kuti aŵerenga bukulo, tingam’gaŵire. Tikufuna kugwiritsa ntchito mabuku athu mwanzeru.
4 Nazi zina zimene munganene mukatha kusonyeza buku: “Ngati mungakonde kuŵerenga bukuli, ndikusiyirani.” Mosakayikira mwininyumba adzafunsa kuti: “Mumachita ndalama zingati?” Mungayankhe kuti: “Sitichita malonda. Sitikugulitsa mabukuŵa. Ntchito imene tikuchita lero m’dera lanuli ikuchitika padziko lonse modzifunira m’mayiko 233 ndi cholinga chothandiza anthu kudziŵa njira ya kumoyo wosatha. Ngati mungafune kupereka ndalama zothandizira ntchitoyi, muchita bwino kwambiri.”
5 Pamene mukugaŵira magazini, mungafunse mafunso pankhani ina ndipo mungati: “Ndikufuna muone mayankho m’magazini iyi. Ngati mungafune kuŵerenga magazini aŵiri awa, ndingakusiyireni.” Akalandira, mungawonjezere kuti: “Ndakondwa kuti mwalandira nkhani imeneyi. Ndikukhulupirira kuti ikuthandizani kwambiri. Bwanji ndidzabwerenso mlungu wamaŵa kudzamva malingaliro anu? Mudzaona kuti Nsanja ya Olonda imasindikizidwa m’zinenero 132 ndipo makope pafupifupi 22,328,000 amafalitsidwa padziko lonse. Ntchito imeneyi imachirikizidwa ndi zopereka zaufulu. Ngati mungakonde kupereka kangachepe kuthandiza ntchito yophunzitsa ya padziko lonseyi, tilandira ndi manja aŵiri.”
6 Nthaŵi zina, kukamba za zopereka zaufulu zothandizira ntchito yathu ya padziko lonse kungakhale kosafunikira. Mwachitsanzo, mwininyumba wachidwi angafunse kuti: “Mungopereka?” Tingayankhe kuti: “Ngati mukufuna kuŵerenga bukuli ndi kutinso likhale lanu, mungatenge. Ndidzabweranso mlungu wamaŵa kudzapitiriza kukambirana ndiponso kudzakuuzani zambiri za ntchito yathu ya padziko lonse.” Pamaulendo otsatira tingam’fotokozere mwininyumba mmene timapezera ndalama zolipirira ntchito yathu. Musanene kuti tsopano magazini ndi mabuku n’zaulere, koma nenani kuti timagaŵira popanda mtengo wake weniweni.
7 Kapenanso mwininyumba mwamsanga angalandire buku ndi kunena kuti, “Zikomo.” Mungayankhe kuti: “Chabwino. Ndikhulupirira mudzasangalala nalo. Ambiri amadabwa komwe kumachokera ndalama zolipirira ntchito imeneyi, popeza ikuchitika padziko lonse. Ambiri amene amalandira mabuku athu amasonyeza kuyamikira zimene akaphunzire ndipo amapereka mwaufulu kangachepe kothandiza kupitiriza kusindikiza ena. Anthu akachita zimenezi, timalandira ndi manja aŵiri.”
8 Kodi Ali ndi Chidwi Chenicheni? N’kwachidziŵikire kuti si cholinga chathu kungogaŵira mabuku chisawawa. Tikufuna mabuku athu kukwaniritsa cholinga chake chothandiza anthu owongoka mtima kuphunzira zochuluka za zifuno zabwino kwambiri za Yehova. Kungakhale kuwononga kumangosiya mabuku kwa anthu amene sayamikira zinthu zauzimu. (Aheb. 12:16) Kugaŵira mabuku kopindulitsa kumadalira luso lathu la kuzindikira amene ali ndi chidwi chenicheni. Kodi chidwi chimenecho tingachione bwanji? Chizindikiro chabwino ndicho kukoma mtima kwa munthuyo ndi kufunitsitsa kulankhula nafe. Kapena kumvetsera pamene mukulankhula, kuyankha mukawafunsa, ndiponso kufotokoza maganizo awo kumasonyeza kuti akusangalala ndi makambiranowo. Kukulankhulani mwaulemu ndi mwaubwenzi kumasonyeza kuti akufunitsitsa. Kukutsatirani pamene mukuŵerenga Baibulo kumatanthauza kuti akulemekeza Mawu a Mulungu. Nthaŵi zambiri, n’koyenera kufunsa ngati adzaŵerenga buku limene mukugaŵira. Komanso, munganene kuti mudzabweranso kudzapitiriza kukambiranako. Kuvomera mosanyinyirika kungasonyezenso kuti ndi wachidwi. Mukaona maumboni osonyeza chidwi chenicheni otereŵa, ndiye kuti munthuyo adzagwiritsa ntchito mabuku alionse amene mungam’patse.
9 Kusintha m’kachitidwe ka ntchito yathu kumeneku kukuperekanso umboni wina wakuti ‘sitichita malonda nawo mawu a Mulungu.’ (2 Akor. 2:17) Ndipo kukutsimikizanso kuti ndife osiyana ndi dziko.—Yoh. 17:14.
10 Popeza kuti Babulo Wamkulu ali pafupi kuwonongedwa, magulu onse achipembedzo akukumana ndi zitsutso. Cholinga chathu chachikulu n’chakuti ntchito yofunika kwambiri yolalikira Ufumu padziko lonse ipitebe patsogolo popanda kudodometsedwa, kuti anthu ena ambiri apulumuke.—Mat. 24:14; Aroma 10:13, 14.