Nyimbo 110
Khalani Wokhululukira
1. Mwachikondi M’lungu wathu,
Napanga makonzedwe,
Natumiza Mwana wake,
Chithandizo napatsa.
Pamene ife tilapa,
Akhululukiradi
Mwachiwombolo cha Kristu,
Tipemphatu chifundo.
2. M’lungu akhululukira
Yemwe amutsanzira,
Nakhululukira ena,
Kusonyeza chifundo.
Poti ife siangwiro,
Tilakwa nthaŵi zonse
Pa zirizonse zoipa.
Tikhululukireni.
3. Ndithu masiku ngoipa
Tikhululukiretu;
Chikondi tisonyezebe
Nzeru yodzera m’mwamba.
Kukhululukira ena
Uchikulire ngwathu,
Mwachidziŵitso chakuya
Tisungetu mtendere.
4. Kukhululuka kowona
Ife tikukulitse.
Kudzatithandizatunso,
Kuthetsa makaniwo.
Pamene tikhululuka,
Tifanana ndi M’lungu,
Wokonda kukhululuka,
Atama chisomocho.