Nyimbo 127
Unyinji wa Abale
1. Abale m’yanda miyanda
Aima ndi ine
Mboni zodalirika,
Zosunga umphumphu.
Miyanda miyandadi,
Khamu lamphamvudi.
M’mitundu yonse padziko
Atamanda M’lungu.
2. Abale m’yanda miyanda,
Ovala zoyera,
Ali m’kachisi wa Ya,
’Sana ndi usiku.
Miyanda miyandadi.
Adziŵitsa anthu
Kuti chipulumutsocho
Chiri kwa Yehova.
3. Abale m’yanda miyanda
—Alalika ‘mbiri
Yabwinoyo yosatha,’
Anthu onse amve.
Amalalikirabe,
Nkana apsinjidwa,
Kristu awatsogolera,
Apeza mtendere.