Nyimbo 115
‘Kondananidi’
1. Chikondi chachikulu
Chiri cha chipiliro
Chipezetsa chiyanjo,
Potumikira.
M’lungu anatumiza
Yesuyo Bwenzi lathu,
Kudzakonza unansi
Tikhale naye.
Ife owopa M’lungu
Tikhale ndi chikondi,
Poyenda mwa Kristudi,
Kukondanadi.
M’dziko la udanili
Tisonyeze chikondi.
Tilondole njirayo—
Kutsanzira Ya, Kutsanzira Ya.
2. Chikondi chosanyenga
Sichikhumudwitsidwa,
Chisonyeza ulemu
Kwa abalewo.
Chiri choleza mtima,
Sichiri chathu chokha,
Chifulatira zonse
Kwa owopa Ya.
Mapeto ayandika,
O tizindikiretu
Chikondicho chikule
Kwa anthu onse!
Tiyeni tikondane
Ndi nzeru yakumwamba.
Titsanzire Mulungu
Kunthaŵi zonse, Kunthaŵi zonse.