Nyimbo 108
Mawu a Yehova Ngokhulupirika
1. Monga mvula yochoka kumwamba
Ichititsa zinthu kumera,
Mofananadi ndi mawu a Ya;
Adzapambana ndi kuwoneka.
2. Yoswa anauza Israyeli
Za ubwino wa Ya kwa iwo.
Zinthu zolonjezedwa ndi M’lungu
Zinachitika; kusonya mphavu.
3. Ya anati kwa olonjezedwa
Mawu ake ali owona.
‘Ndilumbira ndithu’ atero Ya.
Zitipatsa chiyembekezodi.
4. Tingatsimikize m’mawu Ake.
Lonjezo lake lipambana.
Akukonza Dongosolo lina,
Tidzamutamandabe Yehova.