Nyimbo 117
Ukwati—Makonzedwe a Mulungu
1. Ukwati ngwa Mulungu.
Anauyambitsa.
Umaumba umodzi,
Udzetsa dalitso.
Goli lomangilira
Mwamuna ndi mkazi
Adzalambira M’lungu
—Yense ndi mnzakedi.
2. M’lungu ali ndi bukhu
La ’phungu wanzeru.
Linena za umutu,
Wa amuna onse.
‘Mkondeni monga mwini.’
Mulungu afuna.
Wochitira ulemu
Ali ngati ngale.
3. Nkhosi ziri zolimba
Ziposa ziŵiri.
Ya ’kakhala mu’kwati,
mavuto achepa.
Kupatsa nkwabwinodi.
Cho’nadi tidziŵa.
Choncho Pomtumikira,
Tipereke ndithu.