Nyimbo 73
“Nzeru Iri ndi Odzichepetsa”
1. Tikayenda ndi Mulungu,
Tifune kudzichepetsa,
Kudziŵa ukulu wa Ya
Ndi kuchepetsetsa kwathu!
2. Tiri ‘akapolo chabe’!
Timavomereza izi.
Ngatitu tidzichepetsa,
Tidzapindula kwambiri!
3. ‘Tiyende monga a’ng’ono,’
Anatero Mbuye wathu.
Tikakhala odzikuza,
Tilephera malangizo.
4. Titumikire mwa mantha,
Chifukwa timakonda Ya.
Kuyenda modzichepetsa
Ndiyo nzeru yakumwamba.