Nyimbo 221
Achichepere! Tsanzirani Chikhulupiliro Chawo
1. Samueli anapita ku Silo
Kukatumikira, nakulirako.
Anali mneneri mu Israyeli,
Mnaziriyo analemekeza Ya.
Eli anali ndi ana oipa.
Kodi adzaipitsa Samueli?
Ayi Samueli ndi womveradi.
Sadzachoka munjira ya Yehova.
2. Timoteonso anali kamwana
Nakhala mkulu wodziŵa Malemba.
Zophunziridwazo anazichita.
Anafunabe kukhulupirika.
Mumpingo wake anali ndi mbiri,
Wovomerezedwa popanda mtsutso.
Anayendayendadi ndi Paulo;
Utumiki unadalitsa onse.
3. Asungwana Kumbukirani buthu
La chikhulupiliro mwa Yehova.
Ngakhale mu’kapolo analimba;
Changu chake chinasonkheza ena.
Kwa mkazi wa Namani ananena:
‘Mneneri wa Mulungu achiritsa.’
Kazembe Wachisuri anamvera.
Buthulo linadzetsa madalitso.
4. Anyamata, asungwana nonsenu
Tsanzirani zitsanzo zowonazi.
Tiri ndi chidaliro ‘m’nthaŵi ino.’
Yehova wasankha owatumiza.
Achicheperenu menyani nkhondo
Ndi atumiki okonda Mulungu.
Timveketse chenjezo ndi thamolo
Ndi kugaŵana mphotho pomaliza.