Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 14
  • Ophunzira Oyamba a Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ophunzira Oyamba a Yesu
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Anayamba Kupeza Ophunzira
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Amene Anakhala Ophunzira a Yesu
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yohane Abatiza Yesu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yesu Anasankha Atumwi 12
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 14

Mutu 14

Ophunzira Oyamba a Yesu

PAMBUYO pa masiku 40 m’chipululu, Yesu akubwerera kwa Yohane, amene anamubatiza. Pamene akuyandikira kwa iye, mwachiwonekere Yohane akusonya kwa Yesu nafuula kwa awo amene alipo kuti: “Wonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi! Ndiye amene ndinati, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.” Ngakhale kuti Yohane ngwamkulu kuposa mbale wakeyo Yesu, Yohane akudziŵa kuti Yesu anakhalako iye asanakhale monga munthu wauzimu kumwamba.

Komabe, milungu yochepekera yapitayo, pamene Yesu anadza kudzabatizidwa, mwachiwonekere Yohane sanadziŵe motsimikizirika kuti Yesu anali Mesiyayo. “Ndipo sindinamdziŵa iye,” akuvomereza motero Yohane, “koma kuti awonetsedwe kwa Israyeli, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.”

Yohane akupitirizabe kufotokoza kwa omvetsera ake chimene chanachitika pamene anabatiza Yesu: “Ndinawona mzimu alikutsika kuchokera kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye. Ndipo sindinamdziŵa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzawona mzimu atsikira nakhala pa iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi mzimu woyera. Ndipo ndawona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu Ndiyemweyu.”

Tsiku lotsatira Yohane waima ndi aŵiri a ophunzira ake. Kachiŵirinso, pamene Yesu akuyandikira, iye akuti: “Wonani Mwanawankhosa wa Mulungu!” Pa ichi ophunzira aŵiri awa a Yohane Mbatizi akutsatira Yesu. Mmodzi wa iwo ndiye Andreya, ndipo wina mwachiwonekere ndiye munthu weniweniyo amene analemba zinthu zimenezi, amene atchedwanso Yohane. Yohane uyu mogwirizana ndi zisonyezero, alinso mbale wake wa Yesu, mwachiwonekere akumakhala mwana wa mchemwali wa Mariya, Salome.

Potembenuka ndi kuwona Andreya ndi Yohane akumutsatira, Yesu akufunsa kuti: “Mufunafuna chiyani?”

“Rabi,” iwo akufunsa motero, “mukhala kuti?”

“Tiyeni, mukawone,” Yesu akuyankha motero.

Iri pafupifupi 4 koloko madzulo, ndipo Andreya ndi Yohane akukhalabe ndi Yesu tsiku lonse limenelo. Pambuyo pake Andreya akuchita chidwi kotero kuti akufulumira kukafunafuna mbale wake, amene amatchedwa Petro. “Tapeza ife Mesiya,” iye akumuuza motero. Ndipo iye akutengera Petro kwa Yesu. Mwinamwake Yohane panthaŵi imodzimodziyo akupeza mbale wake Yakobo nabwera naye kwa Yesu; komabe, mosiyana ndi ena, Yohane akuchotsa chidziŵitso chonena za iye mwini mu Uthenga wake.

Tsiku lotsatira, Yesu akupeza Filipo, wa ku Betsaida, mzinda umodzimodziwo umene unali kwawo kwa Andreya ndi Petro. Iye akumuitana kuti: “Tsata ine.”

Pamenepo Filipo akupeza Natanayeli, amene akutchedwanso Batolomeyo, ndipo akuti: “Iye amene Mose analembera za iye m’Chilamulo, ndi Aneneri, tampeza ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.” Natanayeli akukayikira. “Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi?” iye akufunsa motero.

“Tiye ukawone,” akumfulumiza motero Filipo. Pamene iwo akufika kwa Yesu, Yesu akuti ponena za Natanayeli: “Wonani, Mwisrayeli ndithu, mwa iye mulibe chinyengo.”

“Munandidziŵira kuti?” Natanayeli akufunsa motero.

“Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuwona iwe,” Yesu akuyankha motero.

Natanayeli akuzizwa. “Rabi [kutanthauza Mphunzitsi], inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli,” iye akutero.

“Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuwona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi?” Yesu akufunsa motero. “Udzawona zoposa izi.” Pamenepo iye akulonjeza kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, mudzawona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa munthu.”

Mwamsanga pambuyo pa izi, Yesu, limodzi ndi ophunzira ake amene wapeza chatsopano, akuchoka ku Chigwa cha Yordano napita ku Galileya. Yohane 1:29-51.

▪ Kodi ophunzira oyamba a Yesu ndani?

▪ Kodi ndimotani mmene Petro, kudzanso mwinamwake Yakobo, akudziŵikitsidwira kwa Yesu?

▪ Kodi nchiyani chimene chikukhutiritsa Natanayeli kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena