Nyimbo 132
Tetezerani Mtima Wanu
1. Tetezani mitima’nu,
Mudzapeza moyo.
Landirani Mawu ake
Mukudziŵa kuti
Zochita zathu ziyamba
Ndi kuganizira.
Tetezera maganizo,
Moyenera Kristu.
2. M’lungu apatsa thandizo
Kuteteza mtima.
Fikani ndi chitamando,
Mudzasamalidwa.
Phunziro la Mawu
Ake Lidzatithandiza
Ndi kuyanjana ndi onse
Oyenda m’kuŵala.
3. Sunganibe maganizo
Pazinthu zowona,
Pazoyera ndi zokoma,
Ndi zoyamikika.
Mudzakhala ndi mtendere
Polingalirabe,
Mtima wotetezeredwa
Udikira moyo.