Kuchiritsa
Tanthauzo: Kuchititsa munthu amene wakhala akudwala mwakuthupi, mwamaganizo, kapena mwauzimu kuti apeze thanzi labwino. Ena a aneneri Achihebri a nthaŵi Yachikristu chisanayambe kuphatikizaponso Yesu Kristu ndi ziŵalo zina za mpingo woyambirira Wachikristu anali okhoza kuchita machiritso ozizwitsa mwa mzimu wa Mulungu.
Kodi kuchiritsa kozizwitsa m’tsiku lathu kumachitidwa mwa mzimu wa Mulungu?
Kodi mphamvu ya kuchita zozizwitsa ingachokere ku magwero ena osakhala Mulungu wowona?
Mose ndi Aroni anawonekera pamaso pa Farao wa Igupto kudzapempha kuti Aisrayeli aloledwe kumka ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova. Monga umboni wa kuchirikizidwa ndi Mulungu, Mose anauza Aroni kuponya ndodo yake pansi ndipo inasandulika chinjoka. Chozizwitsa chimenecho chinachitidwa mwa mphamvu ya Mulungu. Koma pamenepo ansembe ochita matsenga a Igupto anaponya ndodo zawo pansi ndipo nazonso, zinasandulika zinjoka. (Eks. 7:8-12) Kodi ndimwamphamvu ya yani imene iwo anachita chozizwitsa chawocho?—Yerekezerani ndi Deuteronomo 18:10-12.
M’zaka za zana la 20 kuchiritsa kwachikhulupiriro kukuchitidwa m’maserevesi ochitidwa ndi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Pakati pa zipembedzo zosakhala Zachikristu pali asing’anga, afiti, ofuna mankhwala, ndi ena amenenso amachiritsa; kaŵirikaŵiri amagwiritsira ntchito matsenga ndi kuombedza. “Ochiritsa nthenda zamaganizo” ena amanena kuti kuchiritsa kwawo sikuli kogwirizana ndi chipembedzo. M’zochitika zonsezi, kodi mphamvu yochiritsa imachokera kwa Mulungu wowona?
Mat. 24:24: “Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzawonetsa zizindikiro zazikulu [“zozizwitsa,” TEV] ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge ngati nkotheka, osankhidwa omwe.”
Mat. 7:15-23: “Yang’anirani, mupeŵe aneneri onyenga . . . ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuchita zamphamvu zambiri? [“zozizwitsa,” JB, NE, TEV] Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”
Kodi kuchiritsa kwa malingaliro m’tsiku lathu kumachitidwa mwanjira yofanana ndi kuchiritsa kozizwitsa kwa Yesu ndi ophunzira ake oyambirira?
Mtengo wa maserevesi: “Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mat. 10:8) (Kodi ochiritsa amakono akuchita zimenezo—kupereka kwaulere, monga momwe Yesu analamulirira?)
Mlingo wa chipambano: “Khamu lonse lija linafuna kumkhudza iye [Yesu]; chifukwa munatuluka mphamvu mwa iye, nichiritsa onsewa.” (Luka 6:19) “Ananyamulanso natuluka nawo odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo. Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, ali kutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.” (Mac. 5:15, 16) (M’tsiku lathu, kodi onse amene amapita kwa ochiritsa achipembedzo kapena tiakachisi tachipembedzo kukafunafuna kuchiritsidwa amachiritsidwa?)
Kodi njira ya moyo ya ziŵalo za magulu amene “ochiritsa” ali mbali yake imapereka umboni wakuti ali ndi mzimu wa Mulungu?
Monga kagulu kodi iwo amasonyeza zipatso zamzimu monga chikondi, kuleza mtima, kufatsa, ndi kudziletsa mwanjira yapadera?—Agal. 5:22, 23.
Kodi iwo kwenikweni saali “mbali yadziko,” kukana kuphatikizidwa konse m’zochitika za ndale zadziko za dziko? Kodi iwo akhalabe oyera paliwongo lamwazi m’nthaŵi yankhondo? Kodi iwo ali ndi mbiri yabwino chifukwa cha kupeŵa kudzisungira kwachisembwere kwadziko?—Yoh. 17:16; Yes. 2:4; 1 Ates. 4:3-8.
Kodi Akristu owona lerolino amadziŵika mwamphamvu yawo ya kuchiritsa kozizwitsa?
Yoh. 13:35: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Ichi ndicho chimene Yesu ananena. Ngati ife timamkhulupiriradi, timayang’ana chikondi, osati kuchiritsa kozizwitsa, monga umboni wa Chikristu chowona.)
Mac. 1:8: “Komatu mudzalandira mphamvu, mzimu woyera atadza pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Mwamsanga asanasiye atumwi ake kubwerera kumwamba, Yesu anawauza kuti iyi, inali ntchito yofunika imene iwo akachita, osati kuchiritsa. Wonaninso Mateyu 24:14; 28:19, 20.)
1 Akor. 12:28-30: “Mulungu anaika ena m’Eklesia, poyamba atumwi, achiŵiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malirime a mitundumitundu. Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa? Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi?” (Chotero, Baibulo limasonyeza momvekera bwino kuti si Akristu owona onse akakhala ndi mphatso za kuchiritsa.)
Kodi Maliko 16:17, 18 samasonyeza kuti mphamvu ya kuchiritsa odwala ikakhala chizindikiro chodziŵikitsa okhulupirira?
Maliko 16:17, 18: “Zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: M’dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano; adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja awo pa odwala, ndipo adzachira.”
Mavesi amenewa amawoneka m’malembo apamanja ndi matembenuzidwe ena Abaibulo a m’zaka za zana lachisanu ndi chisanu ndi chimodzi C.E. Koma m’malembo Achigriki akale kwambiri, a Sinaiticus ndi Vatican MS. 1209 a m’zaka za zana lachinayi samawonekeramo. Dr. B. F. Westcott, katswiri wodziŵa malembo a Baibulo, ananena kuti “mavesi . . . saali mbali ya malongosoledwe oyambilira koma ali owonjezeredwa.” (An Introduction to the Study of the Gospels, London, 1881, p. 338) Wotembenuza Baibulo Jerome, m’zaka za zana lachisanu, ananena kuti “pafupifupi mavoliyamu onse Achigriki [ali] opanda chigawochi.” (The Last Twelve Verses of the Gospel According to S. Mark, London, 1871, J. W. Burgon, p. 53) New Catholic Encyclopedia (1967) imati: “Mpambo wake wa mawu ndi kalembedwe nzosiyana kwambiri ndi mbali yotsala ya Uthenga kotero kuti sikuli kothekera konse kuti Marko iye mwiniyo anaulemba [ndiko kuti, mavesi 9-20].” (Vol. IX, p. 240) Palibe cholembedwa chosonyeza kuti Akristu oyambirira anamwa poizoni kapena kugwira njoka kutsimikizira kuti anali okhulupirira.
Kodi nchifukwa ninji mphatso zotero monga ya kuchiritsa mozizwitsa zinaperekedwa kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba?
Aheb. 2:3, 4: “Tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife; pochita umboni pamodzi nawo Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu zamitundumitundu ndi zogaŵira za mzimu woyera, monga mwa chifuniro chake.” (Ndithudi, pano panali umboni wokhutiritsa, wakuti mpingo Wachikristu, umene panthaŵiyo unali watsopano, unalidi wa Mulungu. Koma pambuyo pa kukhazikitsidwa kwake mokwanira, kodi kukakhala kofunika kutsimikiziranso mobwerezabwereza?)
1 Akor. 12:29, 30; 13:8, 13: “Ali aneneri onse kodi? . . . Ali nazo mphatso zamachiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malirime? . . . Chikondi sichitha nthaŵi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malirime adzaleka . . . Tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.” (Pamene zinakwaniritsa chifuno chake, mphatso zozizwitsa zimenezo zinali kudzatha. Koma mikhalidwe yosayerekezereka imene iri chipatso cha mzimu wa Mulungu ikasonyezedwabe m’miyoyo ya Akristu owona.)
Malinga ngati munthu wachiritsidwa, kodi ziridi nkanthu ndi mmene kumachitidwira?
2 Ates. 2:9, 10: “Kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mumphamvu yonse [“mitundu yonse ya zozizwitsa,” JB], ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka, popeza chikondi cha chowonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo.”
Luka 9:24, 25, NW: “Aliyense akafuna kupulumutsa moyo wake [“umoyo,” RS, JB, TEV] iye adzautaya; koma amene aliyense akataya moyo wake chifukwa cha ine, adzaupulumutsa uwo. Pakuti munthu apindulanji, akapeza dziko lonse lapansi natayika iye mwini, kapena kuwonongeka?”
Kodi nchiyembekezo chanji chimene chiripo cha kuchiritsidwa kowona panthenda zonse?
Chiv. 21:1-4: “Ndipo ndinawona mmwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, . . . ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”
Yes. 25:8: “Iye wameza imfa kunthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse.” (Ndiponso Chivumbulutso 22:1, 2)
Yes. 33:24: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Kodi mumakhulupirira m’kuchiritsa?’
Mungayankhe kuti: ‘Aliyense amene samakhulupirira kuti Mulungu ali ndi mphamvu ya kuchiritsa samakhulupirira Baibulo. Koma sindingachitire mwina kusiyapo kudabwa kuti kaya anthu akuchita molondola ndi nkhaniyi lerolino.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) Tandilolani ndikuŵerengereni lemba, ndiyeno muwone ngati mudzapeza chizoloŵezi chimene chiri chosiyana kwambiri m’tsiku lathu. (Mat. 10:7, 8) . . . Koma kodi mukuwonanso kanthu kena pano kamene Yesu adanena kuti ophunzira akanachita, kamene ochiritsa lerolino sangakhoze kuchita? (Iwo sangathe kuukitsa akufa.)’ (2) ‘Ife sindife oweruza a anthu ena, koma nkokondweretsa kuti Mateyu 24:24 akutchula kanthu kena kamene tifunikira kukhala ochenjera kusachita.’
Kapena munganene kuti: ‘Inde ndimakhulupiriradi kuti zimene Baibulo limanena ponena za kuchiritsa nzowona. Koma kuchiritsa kulikonse kochitidwa m’dongosolo lino la zinthu kumangopindulitsa kwakanthaŵi, kodi sichoncho? Potsirizira tonsefe timafa. Kodi padzakhala nthaŵi imene munthu aliyense wokhala ndi moyo adzakhala ndi thanzi labwino ndipo osafunikiranso kufa? (Chiv. 21:3, 4)’