Nyimbo 59
Kuyamikira Zikumbutso za Mulungu
1. Achimwemwe ndiomvera M’lungu,
Amfuna ndi mtima wonse,
Amamvera msanga malamulo
Samasiya zilangizo.
Akondwa ndi malamulowo,
Nasimba za chifundo chake.
Amakonda malamulo ake,
Ndi kuyembekeza M’lungu.
2. Chifundo cha M’lungu nchodabwitsa;
Chipitirira miyamba!
Chiweruzo chake chitisunga,
Nkana atinamizira.
Okonda lamulo la M’lungu;
Madalitso awo sadzatha.
Monga wofunkha asangalala,
Tisangalale mu Mawu.
3. Pempho lathu limke kwa
Yehova Kuti timvetse mawuwo.
Amve pemphero ndi kutiyanja
Natipulumutse ife.
Tikhale owona kwa M’lungu,
Ndi kuchita zonena zake.
Yehova Mulungu wolungama.
Amatilimbikitsatu.