Mutu 5
Kubadwa kwa Yesu—Kuti Ndipo Liti?
WOLAMULIRA wa Roma, Kaisara Augusto, wapereka lamulo lakuti aliyense ayenera kubwerera kumzinda wake wobadwira kukalembetsedwa m’kaundula. Chotero Yosefe akupita kumalo ake obadwira, mzinda wa Betelehemu.
Anthu ambiri ali ku Betelehemu kudzalembetsa, ndipo malo okhalamo okha amene Yosefe ndi Mariya angapeze ndiwo m’khola. Mmenemu, mmene abulu ndi nyama zina zimasungidwira, Yesu akubadwiramo. Mariya akumkulunga iye munsalu namgoneka iye modyera ng’ombe, malo amene mumakhala chakudya cha nyama.
Ndithudi kunali motsogozedwa ndi Mulungu kuti Kaisara Augusto apange lamulo lake la kalembera. Zimenezi zinatheketsa Yesu kukabadwira ku Betelehemu, mzinda umene Malemba ananeneratu kuti udzakhala malo obadwira wolamulira wolonjezedwayo.
Ndiusiku wapadera wotani nanga umenewu! Kuthengo kuunika koŵala kukuunikira mozungulira gulu la abusa. Ndiwo ulemerero wa Yehova! Ndipo mngelo wa Yehova akuwauza kuti: “Musawope pakuti wonani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwerero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi amene ali Kristu Ambuye. Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera.” Mwadzidzidzi angelo ena ambiri anawonekera naimba kuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.”
Pamene angelo akuchoka, abusawo akunena kwa wina ndi mnzake kuti: “Tipitiretu ku Betelehemu, tikawone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziŵitsira ife.” Iwo akupita mofulumira ndipo akupeza Yesu kumene mngelo anawauza kuti adzampeza. Pamene abusa akunena zimene mngelo anawauza, onse amene akumva azizwa. Mariya akusunga mawu onsewo ndi kukondwera mumtima mwake.
Anthu ambiri lerolino amakhulupirira kuti Yesu anabadwa pa December 25. Koma December ndinthaŵi yamvula, nyengo yozizira ku Betelehemu. Abusa sakanakhala ali kuthengo usiku wonse ndi zoŵeta zawo panthaŵi imeneyo ya chaka. Ndiponso, Kaisara wa Roma sakanafunikiritsa anthu amene anali kale ndi chikhoterero chompandukira kuti apange ulendo umenewo m’nthaŵi yozizira kwambiri imeneyo. Mwachiwonekere Yesu anabadwa nthaŵi ina m’chilimwe cha chakacho. Luka 2:1-20; Mika 5:2.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yosefe ndi Mariya akupita ku Betelehemu?
▪ Kodi ndichinthu chozizwitsa chotani chikuchitika usiku umene Yesu akubadwa?
▪ Kodi timadziŵa bwanji kuti Yesu sanabadwe pa December 25?