Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 218-tsamba 222
  • Kuulula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuulula
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Kuulula Machimo—Kodi Ndiko Njira ya Munthu kapena ya Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kuulula Machimo—Kodi Pali Cholakwika?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tiziulula Ndiponso Kulapa Machimo Athu?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Mulungu Angandikhululukire Machimo Anga?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 218-tsamba 222

Kuulula

Tanthauzo: Chilengezo kapena kuvomereza, poyera kapena mtseri, (1) cha zimene munthuyo amakhulupirira kapena (2) cha machimo ake.

Kodi dzoma la kuyanjana, kuphatikizapo kuulula konong’ona (kuulula kwamunthu kochitidwira m’khutu la wansembe), monga momwe kukuphunzitsidwira ndi Tchalitchi cha Katolika Nzamalemba?

Dongosolo mu limene wansembe amatchulidwira

Dongosolo lozoloŵereka, logwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri, nlakuti: “Ndidalitseni, Abambo, pakuti ndachimwa. Papita [nthaŵi yaitali] kuyambira pa Kuulula kwanga kotsirizira.”—Magazine a U.S. Catholic, October 1982, p. 6.

Mat. 23:1, 9, JB: “Yesu anati, . . . ‘Simuyenera kutcha aliyense padziko lapansi atate wanu, popeza muli naye Atate mmodzi yekha, ndipo iyeyo ali kumwamba.’”

Machimo amene angakhululukidwe

“Tchalitchi nthaŵi zonse chaphunzitsa kuti tchimo lirilonse, mosasamala kanthu za mmene lingakhalire lalikulu, lingakhululukidwe.”—The Catholic Encyclopedia (lokhala ndi nihil obstat ndi imprimatur), R. C. Broderick (Nashville, Tenn.; 1976), p. 554.

Aheb. 10:26, JB: “Ngati, pambuyo pa kupatsidwa chidziŵitso cha chowonadi, tingachite machimo alionse mwadala, pamenepo sipatsalanso nsembe iriyonse kaamba ka iwo.”

Marko 3:29, JB: “Munthu aliyense akachitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa konse: ali ndi liwongo la uchimo wamuyaya.”

Mmene kuulula kungasonyezedwere

Kaŵirikaŵiri woululitsayo amalangiza woululayo kunena mapemphero a “Atate Wathu” ndi “Tikuwoneni Mariya” nthaŵi zenizeni zingapo.

Mat. 6:7, JB: “M’mapemphero anu musamabwebweta [ndiko kuti, kulankhula mawu mobwerezabwereza mopanda tanthauzo] monga momwe akunja amachitira, pakuti iwo amalingalira kuti mwa kugwiritsira ntchito mawu ambiri adzadzichititsa kumvedwa.”

Mat. 6:9-12, JB: “Muyenera kupemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, . . . tikhululukireni mangaŵa athu.” (Palibe m’Baibulo pamene timalamulidwa kupemphera kwa kapena kupyolera mwa Mariya. Wonani Afilipi 4:6, ndiponso tsamba 258, 259, pamutu wakuti “Mariya.”)

Aroma 12:9, JB: “Musalole chikondi chanu kukhala cha chiphamaso, koma mowona mtima funani chabwino mmalo mwa choipa.”

Kodi Yesu sanavomereze atumwi ake kukhululukira machimo?

Yoh. 20:21-23, JB: “‘Monga momwe Atate anandituma ine, chotero ndikukutumani inu.’ Atanena izi anauzira pa iwo nati: ‘Landirani Mzimu Woyera. Pakuti awo amene inu mudzakhululukira machimo awo, akhululukidwa; pakuti awo amene simukhululukira machimo awo, iwo sakhululukidwa.’”

Kodi ndimotani mmene atumwi anamvetsetsera ndi kugwiritsira ntchito zimenezi? Mulibe cholembedwa m’Baibulo cha chochitika chimodzi m’chimene mtumwi anamvetsera kuulula kwamtseri ndiyeno nalengeza kukhululukidwa. Komabe, zofunika za kukhululukidwa ndi Mulungu zalembedwa m’Baibulo. Atumwiwo, motsogozedwa ndi mzimu woyera, anali kupenda anthu alionse paokha okwaniritsa zofunika zotero ndipo pamaziko a zimenezo analengeza kuti Mulungu anali atawakhululukira iwo kapena kusawakhululukira. Mwachitsanzo, wonani Machitidwe 5:1-11, ndiponso 1 Akorinto 5:1-5 ndi 2 Akorinto 2:6-8.

Wonaninso mutu waukulu wakuti “Kuloŵa Mmalo Kwautumwi.”

Malingaliro a akatswiri onena za chiyambi cha kuulula konong’ona amasiyana

The Catholic Encyclopedia, la R. C. Broderick, imati: “Kuyambira m’zaka za zana lachinayi kuulula konong’onera m’khutu kwakhala njira yovomerezedwa.”—P. 58.

New Catholic Encyclopedia imati: “Olemba mbiri ogwirizana ambiri, ponse paŵiri Akatolika ndi Aprotestanti, amabwerera mmbuyo kuchiyambiyambi cha kuulula kwamtseri monga chilango chozoloŵereka kumatchalitchi a Ireland, Wales, ndi Britain, kumene Masakramenti, kuphatikizapo Kulapa, kaŵirikaŵiri kunachitidwa ndi bambo mfumu ndi ansembe ake. Mwa machitachita a kuulula kochitidwa kwa ansembe ndipo chitsogozo chauzimu chapoyera ndi chamtseri monga chitsanzo, kuulula kobwerezabwereza ndi kuulula kwa kudzipereka kumawonekera kukhala kutayambitsidwa kaamba ka anthu wamba. . . . Komabe, kunali kokha m’zaka za zana la 11 pamene machimo amtseri anakhululukidwa panthaŵi ya kuululidwa ndipo kukwaniritsidwa kwa kuulula kusanachitike.”—(1967), Vol. XI, p. 75.

Wolemba mbiri A. H. Sayce akusimba kuti: “Mabukhu amadzoma amasonyeza kuti ponse paŵiri kuulula kwapoyera ndi kwamtseri kunachitidwa m’Babulo. Ndithudi, kuulula kwamtseri kukuwonekera kukhala njira yakale kwambiri ndi yozoloŵereka koposerapo.”—The Religions of Ancient Egypt and Babylonia (Edinburgh, 1902), p. 497.

Kodi nchiyani chimene chiri zikhulupiriro za Mboni za Yehova ponena za kuulula?

Kuvomereza chikhulupiriro cha munthuwe mwa chilengezo chapoyera

Aroma 10:9, 10, NW: “Pakuti ngati ulengeza poyera ‘mawu a mkamwa mwako’ amenewo, kuti Yesu ndiye Ambuye, ndi kusonyeza chikhulupiriro mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumutsidwa. Pakuti ndi mtima munthu amasonyeza chikhulupiriro cha chilungamo, koma ndi mkamwa munthu amapanga chilengezo chapoyera cha chipulumutso.”

Mat. 10:32, 33: “Chifukwa chake yense amene adzavomereza ine [Yesu Kristu] pamaso pa anthu, inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa atate wanga wakumwamba. Koma yense amene adzandikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamkana iye pamaso pa atate wanga wakumwamba.”

Pamene munthu achimwira Mulungu

Mat. 6:6-12: “Iwe popemphera loŵa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali mtseri . . . Atate wathu wakumwamba dzina lanu liyeretsedwe . . . mutikhululukire mangaŵa anthu, monga ifenso takhululukira amangaŵa athu.”

Sal. 32:5: “Ndinavomereza choipa changa kwa inu [Mulungu], ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.”

1 Yoh. 2:1: “Akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.”

Pamene munthu aliyense payekha achimwira munthu mnzake kapena pamene achimwiridwa

Mat. 5:23, 24: “Ngati uli kupereka mtulo wako paguwa lansembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”

Mat. 18:15: “Ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize panokha iwe ndi iye.”

Luka 17:3: “Akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa umkhululukire.”

Aef. 4:32: “Mukhalirane okoma mtima wina ndi mnzake, amtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”

Pamene munthu aphatikizidwa m’cholakwa chachikulu ndipo afuna chithandizo chauzimu

Yak. 5:14-16: “Kodi pali wina adwala [mwauzimu] mwa inu? Adziitanire akulu ampingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye; ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye [ndi Mulungu]. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupemphere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe.”

Miy. 28:13: “Wobisa machimo ake sadzawona mwaŵi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitiridwa chifundo.”

Bwanji ngati anthu ochita machimo safunafuna chithandizo?

Agal. 6:1: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu mubweze woteroyo mu mzimu wachifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.”

1 Tim. 5:20: “Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse [ndiko kuti, awo amene amadziŵa za nkhaniyo], kuti otsalawo achite mantha.”

1 Akor. 5:11-13: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, ngakhale kukadya naye wotere, iyayi. . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena