Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 9
  • Moyo Wabanja Woyambirira wa Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wabanja Woyambirira wa Yesu
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Anakulira ku Nazareti
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Ankateteza ndi Kusamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Analandira Chitsogozo cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 9

Mutu 9

Moyo Wabanja Woyambirira wa Yesu

PAMENE Yesu akukula m’Nazarete, uwo uli mzinda wocheperapo, wosanunkha kanthu. Wamangidwa pamalo amapiri achigawo chotchedwa Galileya, osati kutali ndi Chigwa cha Yezreeli chokongolacho.

Pamene Yesu, mwinamwake ali pafupifupi ndi zaka ziŵiri zakubadwa, akubweretsedwa kuno kuchokera ku Aigupto ndi Yosefe ndi Mariya, mwachiwonekere ndiye mwana yekha wa Mariya. Koma osati kwa nthaŵi yaitali. M’nthaŵi yokwanira, Yakobo, Yosefe, Simoni, ndi Yuda akubadwa, ndipo Mariya ndi Yosefe akufikiranso kukhala makolo a asungwana. Potsirizira pake Yesu, ali ndi abale ake ndi alongo osachepera pa asanu ndi mmodzi.

Yesu alinso ndi achibale ake ena. Tikudziŵa kale za mbale wake wokulirapoyo Yohane, amene amakhala ku Yudeya pamtunda wamakilomitala ambiri. Koma amene akukhala pafupi kwambiri m’Galileya ndiye Salome, amene mwachiwonekere ali mchemwali wa Mariya. Salome ngwokwatidwa ndi Zebedayo, chotero anyamata awo aŵiri Yakobo, ndi Yohane, akakhala abale a Yesu. Sitidziŵa kuti kaya, pokula, Yesu anathera nthaŵi yambiri ndi anyamata ameneŵa, koma pambuyo pake akufikira kukhala atsamwali apafupi.

Yosefe afunikira kugwira ntchito zolimba kuti achirikize banja lake lomakulalo. Iye ndiwopala matabwa. Yosefe akulera Yesu monga mwana wake, chotero Yesu akutchedwa “mwana wa mmisiri wa mitengo.” Yosefe akuphunzitsa Yesu kukhalanso wopala matabwa, ndipo akuphunzira bwino lomwe. Ndicho chifukwa chake anthu pambuyo pake akuti ponena za Yesu, “Simmisiri wa mitengo uyu.”

Moyo wabanja la Yosefe uli wozikidwa pakulambiridwa kwa Yehova Mulungu. Mogwirizana ndi Chilamulo cha Mulungu, Yosefe ndi Mariya akupereka malangizo auzimu kwa ana awo ‘pamene akhala pansi m’nyumba yawo, pamene ayenda panjira, pamene agona, ndi pamene adzuka.’ Ku Nazarete kuli sunagoge, ndipo tingathe kukhala otsimikizira kuti Yosefe amapitanso ndi banja lake mokhazikika kukalambira kumeneko. Koma mosakayikira iwo akupeza chisangalalo chachikulu koposa m’maulendo awo okhazikika omka kukachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Mateyu 13:55, 56; 27:56; Marko 15:40; 6:3; Deuteronomo 6:6-9.

▪ Kodi ndiabale ake aang’ono angati ndi alongo amene Yesu ali nawo, ndipo maina a ena a iwo ndani?

▪ Kodi ndiati amene ali achibale ena odziŵika atatu a Yesu?

▪ Kodi ndintchito yakuthupi iti imene Yesu potsirizira pake akuchita, ndipo chifukwa ninji?

▪ Kodi ndimalangizo ofunika otani amene Yosefe akupereka kubanja lake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena