Imfa
Tanthauzo: Kulekeka kwa kugwira ntchito konse kwa moyo. Pamene kupuma, kugunda kwamtima, ndi kugwira ntchito kwa ubongo zileka, mphamvu ya moyo pang’ono ndi pang’ono imaleka kugwira ntchito m’maselo athupi. Imfa ndiyo kusiyana ndi moyo.
Kodi munthu analengedwa ndi Mulungu kuti afe?
Mosemphana ndi zimenezi, Yehova anachenjeza Adamu kusakhala wosamvera, kumene kukanatsogolera ku imfa. (Gen. 2:17) Pambuyo pake, Mulungu anachenjeza Aisrayeli motsutsana ndi kudzisungira kumene kukanatsogolera ngakhale ku imfa yamwamsanga kwa iwo. (Ezek. 18:31) M’nthaŵi yokwanira anatumiza Mwana wake kukafera anthu kotero kuti awo amene akakhulupirira m’kakonzedwe kameneka akakhale nawo moyo wosatha.—Yoh. 3:16, 36.
Salmo 90:10 limanena kuti nthaŵi yozoloŵereka ya moyo wamunthu ndiyo zaka 70 kapena 80. Zimenezo zinali zowona pamene Mose analemba, koma sizinali choncho kuyambira pachiyambi. (Yerekezerani ndi Genesis 5:3-32.) Ahebri 9:27 amati: “Popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi.” Izinso, zinali zowona pamene zinalembedwa. Koma sizinali choncho Mulungu asanapereke chiŵeruzo pa Adamu wochimwayo.
Kodi nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa?
Yehova analenga anthu aŵiri oyamba ali angwiro, okhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha. Anapatsidwa ufulu wakudzisankhira. Kodi akamvera Mlengi wawo mwachikondi ndi chiyamikiro kaamba ka zonse zimene anali atawachitira? Iwo anali oti nkukhoza kotheratu kuchita choncho. Mulungu anauza Adamu kuti: “Koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadye umenewo udzafa ndithu.” Mogwiritsira ntchito njoka monga cholankhulira, Satana ananyenga Hava kuswa lamulo la Yehova. Adamu sanadzudzule mkazi wake koma anagwirizana naye m’kudya chipatso choletsedwacho. Monga momwedi anali ataneneratu, Yehova anapereka chilango cha imfa pa Adamu, koma asanaphe aŵiri ochimwa amenewo, Yehova mwachifundo anawalola kubala ana.—Gen. 2:17; 3:1-19; 5:3-5; yerekezerani ndi Deuteronomo 32:4 ndi Chivumbulutso 12:9.
Aroma 5:12, 17, 19 amati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu] ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa. . . . Ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu . . . Monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa.”
1 Akor. 15:22: “Mwa Adamu onse amafa.”
Wonaninso mutu waukulu wakuti “Choikidwiratu.”
Kodi nchifukwa ninji makanda amafa?
Sal. 51:5: “Wonani, ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo mayi wanga anandilandira mu zoipa.” (Wonaninso Yobu 14:4; Genesis 8:21.)
Aroma 3:23; 6:23: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu . . . Mphotho yake ya uchimo ndi imfa.”
Mulungu “samatenga” ana kwa makolo awo, monga momwe ena auzidwira. Ngakhale kuli kwakuti dziko lapansi limatulutsa chakudya chokwanira, magulu adyera andale zadziko ndi amalonda kaŵirikaŵiri amalepheretsa kugaŵiridwa kwake kwa awo ochifuna koposa, zikumachititsa imfa chifukwa cha nthenda ya kudya mosakwanira. Ana ena amafera m’ngozi, monga momwe amachitira akulu. Koma tonsefe tiri ndi choloŵa cha uchimo; tonsefe tiri opanda ungwiro. Tinabadwira m’dongosolo limene aliyense, ponse paŵiri wabwino ndi woipa—potsirizira pake amafa. (Mlal. 9:5) Koma Yehova ‘akulakalaka’ kugwirizanitsa ana ndi makolo awo kupyolera mwa chiukiriro, ndipo mwachikondi iye wapanga makonzedwe akutero.—Yoh. 5:28, 29; Yobu 14:14, 15; yerekezerani ndi Yeremiya 31:15, 16; Marko 5:40-42.
Kodi akufa ali kuti?
Gen. 3:19: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”
Mlal. 9:10: “Chirichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti kulibe ntchito ngakhale kulingilira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda [“lithinda,” KJ, Kx; “dziko la akufa,” TEV], uli kupitako.”
Kodi chiyani chimene chiri mkhalidwe wa akufa?
Mlal. 9:5: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.”
Sal. 146:4: “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake [“maganizo.” KJ, 145:4 mu Dy; “kuganiza kwake konse,” NE; “makonzedwe,” RS, NAB] zitayika.”
Yoh. 11:11-14: “Lazaro bwenzi lanthu alimtulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. . . . Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.” (Ndiponso Salmo 13:3)
Kodi pali mbali yamunthu imene imapitirizabe kukhala ndi moyo pamene thupi lifa?
Ezek. 18:4: “Moyo [“moyo,” RS, NE, KJ, Dy, Kx; “mwamuna,” JB; “munthu,” TEV] wochimwawo ndiwo udzafa.”
Yes. 53:12: “Anathira moyo [“moyo,” RS, KJ, Dy; “moyo,” TEV; “iye mwini,” JB, Kx, NAB] wake ku imfa.” (Yerekezerani ndi Mateyu 26:38.)
Wonaninso mitu yaikulu yakuti “Moyo (Soul)” ndi “Mzimu.”
Kodi akufa angakhoze kuthandiza kapena kuvulaza amoyo mwanjira iriyonse?
Mlal. 9:6: “Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano.”
Yes. 26:14: “Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka.”
Bwanji za malipoti opangidwa ndi anthu amene anatsitsimulidwa pambuyo pa kunenedwa kukhala atafa ndi amene analankhula za moyo wina?
Kaŵirikaŵiri, pambuyo pooti munthu waleka kupuma ndipo mtima wasiya kugunda, pamatenga mphindi zingapo kuti kuleka kugwira ntchito kwapang’onopang’ono kwa mphamvu ya moyo m’maselo athupi kuyambe. Ngati thupi liri lozizidwa kwambiri, mchitidwe umenewo ungachedwetsedwe kwa maola angapo. Kaamba ka chifukwa ichi, nthaŵi zina kumakhala kotheka kutsitsimula anthu mwa kuwatsitsimula mouzirira mpweya. Iwo anali chimene chimatchedwa “kukomoka,” koma maselo a thupi lawo anali chikhalirebe amoyo.
Anthu ambiri otsitsimulidwa kuchokera ku “kukomoka” sanakumbukira chirichonse. Ena amasimba zokumana nazo za kuyandama m’malere. Ena amanena kuti anawona zinthu zokongola; ena anawopsedwa ndi chokumana nacho chawo.
Kodi pali kalongosoledwe ka madokotala ka chirichonse cha zokumana nazo zimenezi?
Nkonzi wa The Arizona Republic ya zamankhwala analemba kuti: “Pamene nyonga ya thupi iri yochepetsetsa, monga ngati pogonekedwa ndi mankhwala, kapena chifukwa cha nthenda kapena kuvulala, chotero kulamulira kwachibadwa kugwira ntchito kwa thupi kumazimiririka molinganira. Chotero, nsanganizo za mahomoni aminyeŵa ndi makatekolamaini a dongosolo lamitsempha zimatulutsidwa zochuluka mosalamulirika. Chotulukapo, pakati pa zinthu zina, ndicho kuwona masomphenya, zokulitsidwa pambuyo pa kutsitsimuka, akukhala atafa ndi kubwereranso kumoyo.”—May 28, 1977, p. C-1; ndiponso magazine a mankhwala a Jeremani otchedwa Fortschritte der Medizin, No. 41, 1979; Psychology Today, January 1981.
Koma kodi umboni wa awo amene anatsitsimulidwa sumatsimikiziridwa ndi anthu kwa amene akufa okondedwawo awonekera ndi kukhala nawo?
Chonde, ŵerenganinso, malemba ogwidwa poyambirirapo onena za mkhalidwe wa akufa. Kodi chiyani chimene Mawu a Mulungu a chowonadi amatiuza ponena za mkhalidwe wa akufa?
Kodi ndani amene amafuna kuti anthu akhulupirire mwa njira ina? Pambuyo pooti Yehova wachenjeza makolo athu oyambawo kuti kusamvera kukawabweretsera imfa, kodi anatsutsa ndani? “Njoka [yogwiritsiridwa ntchito ndi Satana; wonani Chivumbulutso 12:9] inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai.” (Gen. 3:4) Ndithudi, pambuyo pake, Adamu ndi Hava anafa. Pamenepo, mwachiwonekere, kodi ndani amene anatulukira lingaliro lakuti mbali ya mzimu yamunthu imapulumuka imfa yathupi? Monga momwe tawonera kale, izi sindizo zimene Mawu a Mulungu amanena. Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli wakale chinatsutsa machitachita akufunsira akufa monga “kudetsedwa” ndi “zonyansa.” (Lev. 19:31; Deut. 18:10-12; Yes. 8:19) Kodi Mulungu wachikondi akanatsutsa machitachita awa ngati amoyo anali kulankhulana kokha ndi okondedwa awo amene anali atafa? Kumbali ina, ngati mizimu ya ziŵanda inali kuvala matupi a akufa ndi kusokeretsa anthu ndi kupereka ku malingaliro awo malingaliro amene zimapitiriza bodza, kodi sikukanakhala chikondi kuti Mulungu atetezere atumiki ake ku chinyengo chotero?—Aef. 6:11, 12.
Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizimakhala ndi phande m’miyambo ya makolo ya maliro?
Kulira maliro kaamba ka imfa ya wokondedwa nkwachibadwa ndipo kungasonyezedwe moyenerera
Pambuyo pa imfa ya bwenzi lake lapamtima Lazaro, “Yesu analira.” (Yoh. 11:35) Nthaŵi zina chisoni chimene atumiki a Mulungu anakumana nacho kulirira akufa chinali chachikulu.—2 Sam. 1:11, 12.
Koma chifukwa cha chiyembekezo cha chiukiriro, Akristu amauzidwa kuti: “Sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.”—1 Ates. 4:13.
Atumiki a Yehova samatsutsa miyambo yonse yophatikizidwa ndi akufa
Gen. 50:2, 3: “Yosefe anauza akapolo ake asing’anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi . . . ndipo anatha masiku makumi anayi a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi.”
Yoh. 19:40: “Anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.”
Miyambo imene imatsutsana ndi Mawu a Mulungu imapeŵedwa ndi awo amene amafuna kumkondweretsa
Miyambo ina imalengeza poyera mkhalidwe wachisoni wamunthu. Koma Yesu anati: “Pamene ponse musala kudya [chifukwa cha chisoni] musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zawo, kuti awonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, alandiriratu mphotho zawo. Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: kuti usawonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma adzakubwezera iwe.”—Mat. 6:16-18.
Miyambo ina imasonyeza chikhulupiriro chakuti munthu ali ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka pa imfa yathupi ndipo, chotero, akuzindikira zimene amoyowo akuchita. Koma Baibulo limati: “Akufa . . . sadziŵa kanthu bi.” (Mlal. 9:5) Ndiponso, limati “Moyo wochimawo ndiwo udzafa.”—Ezek. 18:4.
Miyambo yambiri imabuka kuchokera m’kukhulupirira kuti akufa afunikira chithandizo cha amoyo kapena mantha akuti iwo angavulaze amoyo ngati sakukondweretsedwa. Koma Mawu a Mulungu amasonyeza kuti akufa sakuvutika kapena kukondwera konse. “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Sal. 146:4; wonaninso 2 Samueli 12:22, 23.) “Chikondano chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano.”—Mlal. 9:6.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Chiri chifuniro cha Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Chimenecho chiri chikhulupiriro chofala kwambiri. Ndakupeza kukhala kothandiza kusanthula chimene Mulungu iye mwiniyo amanena za ichi.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘(Ŵerengani Genesis 2:17.) Ngati atate achenjeza mwana wake wamwamuna kuti kuchita chinthu chakutichakuti kukamuwonongetsera moyo, kodi mukananena kuti atateyo akufuna kuti mwanayo achichite?’ (2) ‘Pamenepa kodi nchiyani chimene kwenikweni chiri chifuno cha Mulungu kwa anthu? Yesu anati: “Chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wa kuyang’ana Mwana [ndiko kuti, kuzindikira ndi kuvomereza kuti Yesu alidi Mwana wa Mulungu] ndi kukhulupirira iye, akhale nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.” (Yoh. 6:40)’
‘Anthu adzafa nthaŵi zonse’
Mungayankhe kuti: ‘Ndithudi zimenezo ndizo zimene zachitika kwa anthu kufikira tsiku lathu, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Koma wonani lonjezo lodabwitsa loperekedwa ndi Mulungu pa Chivumbulutso 21:3, 4 (kapena Yesaya 25:8).’
‘Zimachitika ngati nthaŵi yako yakwana’
Mungayankhe kuti: ‘Anthu ochuluka amalingalira mmene mukuchitiramo. Kodi munali kudziŵa kuti unyinji wa Agiriki akale anali ndi lingaliro lofananalo? Iwo anakhulupirira kuti panali milungu yachikazi itatu imene imapima utali wa moyo umene munthu aliyense akakhala nawo. Koma Baibulo limafotokoza lingaliro losiyana kwambiri.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) (Ŵerengani Mlaliki 9:11.) Mwachitsanzo: Chidutswa cha konkire chingasweke kunyumba ndi kugwera pamunthu woyenda ndi miyendo. Kodi anachichititsa ndi Mulungu? Ngati ziri choncho, kodi nkolungama kuimba mlandu mwininyumbayo wa kunyalanyaza? . . . Monga momwe Baibulo limanenera, kwa woyenda ndi miyendoyo, chinali chochitika chosalinganizidwa ndi chosawonedweratu chakuti iye anali pamenepo pamene konkire inagwa.’ (2) ‘Baibulo limatiuza kuti ngati tipeŵa khalidwe loipa timatetezera moyo wathu. (Miy. 16:17) Ngati inu muli kholo, ndiri wotsimikiza kuti mumagwiritsira ntchito lamulo lamakhalidwe abwino limenelo kwa ana anu. Mumawachenjeza kusachita zinthu zimene zingachititse kutayika kwa moyo. Yehova akuchita chinthu chofanana kaamba ka anthu onse lerolino.’ (3) ‘Yehova amadziŵa chimene chiri mtsogolo. Kupyolera mwa Baibulo amatiuza mmene tingakhalire moyo kwanthaŵi yaitali kwambiri koposa anthu amene amanyalanyaza zimene limanena. (Yoh. 17:3; Miy. 12:28)’ (Wonaninso mutu waukulu wakuti “Choikidwiratu.”)