Nyimbo 11
Otsalira a Asulami
1. “Msulami wokongola ndi wabwino,
Ubwino wauzimu ndi wambiri.
Kulankhula kwako nkokondweretsa.
Chiyanjano chako, chikundigwira.”
2. Atero mbusa wake, Kristu Yesu,
Afuna kugaŵana naye mphotho.
Ndimotani wolimba ngati khoma,
Akuyankhira kwa ’mbuye wakeyo?
3. “Kudzipereka sikungagulidwe
Chikondi chifanana ndi malaŵi.
Chikondi chowona sichimagonja.
Chikondi chako nchonga laŵi la Ya.”
4. “Otsalira” Msulami, usagonje.
Khala woyera kwa mwamuna wako.
Atsamwali ako a unamwali
Akondwa ndi mphotho udzapezayo.