Nyimbo 139
Mvetserani Mbiri ya Ufumu
1. Mvetserani Mbiri ya Ufumu lero
Yesu akuti: ‘Ndilamulira.
Posachedwa otsutsa adzachotsedwa;
Chotero thaŵani musachedwe konse.’
(Korasi)
2. Mwa mboni zake Yehova aitana:
‘Inu ofatsa, Sangalalani.
Posachedwa Kristu Awonetsa mphamvu
Pamene zovuta zonse zidzachoka.’
(Korasi)
3. Achimwemwe ndi anthu akumva lero
Ndi kumanena: ‘M’lungu ndimvera.’
M’lungu awasunga okhulupirika,
Omafuna choyamba Ufumu wake.
(KORASi)
Kwa oipa tinene alape,
Asandulize maganizo awo.
Aloleni apite kwa M’lungu
Ndipo adzakhululukira.