Nyimbo 149
“Mulungu Sakhoza Kunama”
1. M’lungu analonjeza Abrahamu,
Kuti adzadalitsa kwakukulu.
Abrahamu anakhulupilira;
Chifukwa M’lungu sakhoza kunama.
2. Kusonyeza kusasintha kwakeko,
Analoŵapo ndi lumbiro lake,
Tiyembekeza ndikumlemekeza,
Chifukwa M’lungu sakhoza kunama.
3. Kulimbitsa chikhulupiro chathu,
M’lungu ’natsimikiza mwalumbiro.
Tingagonjetse owukira onse;
Chifukwa M’lungu sakhoza kunama.
4. Yehova Wakumwamba ndiwowona,
Samasiyatu konse omgonjera.
Tidalira mawu, lumbiro lake
—Chifukwa M’lungu sakhoza kunama.