Nyimbo 90
Kulambira Yehova Ambuye Mfumu
1. Yehova Ambuye Mfumu,
Mwabwezera chowonadi.
Kuŵala kwawonekadi,
Khamu likulambirani.
2. Chiwonjezekocho chadza
Kwa otumikira inu.
Alemekeza Mulungu
Nalambira inu nokha.
3. Sadzaphunziranso nkhondo,
Atsogoza utumiki;
Amalambira mwa mantha
Amvera lamulo lanu.
4. Tikondwa m’tsiku lanuli,
Pamene Ufumu wadza!
Mwana wanu alamula;
Tiimba mosangalala.