Kufalitsa Choonadi cha Baibulo ku Portugal
KUCHOKERA ku Caminha kumpoto kufika ku Vila Real de Santo Antônio kummwera, zikwi za mabwato okongola zimaonekera m’mbali mwa Gombe la Atlantic la Portugal la makilomita 800. Asodzi a nsomba ‘atsikira kunyanja naloŵa m’zombo’ kwa zaka mazana, akumapanga nsomba kukhala chakudya chachikulu cha Apwitikizi.—Salmo 107:23.
Kwa zaka 70 zapitazi, usodzi wina wakhala ulikuchitika m’Portugal. Mboni za Yehova zakhala zikubweretsa uthenga wabwino kwa zikwi makumi za nsomba zophiphiritsira. (Mateyu 4:19) Mu May 1995 panali chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu 44,650—kugaŵidwa kwa wofalitsa mmodzi pa anthu 210. Theka la kugaŵa kumeneku ndilo kugaŵa kwa m’mizinda ina.
Pokhala ndi antchito ambiri, magawo olalikiramo m’malo ambiri amafoledwa pafupifupi mlungu uliwonse. Motero Mboni zachipwitikizi nzaluso kwambiri pa kugwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana kuti zigaŵane chiyembekezo chawo cha Baibulo ndi ena. Inde, izo zimazindikiradi kufunika kwa kufalitsa choonadi cha Baibulo m’njira iliyonse yotheka.—1 Akorinto 9:20-23.
Kuthandiza Okonda Chipembedzo
Malinga ndi chiŵerengero cha anthu mu 1991, 70 peresenti ya azaka 18 kapena okulirapo ku Portugal amati ndi Aroma Katolika. Ngakhale zili choncho, chidziŵitso cha Baibulo pakati pa anthuwo nchochepa. Nyuzipepala yotchedwa Jornal de Notícias inati: “Limeneli ndilo limodzi la masoka aakulu kwambiri a chitaganya cha Katolika: Umbuli wa Baibulo!” Kodi nchifukwa ninji zili choncho? Nyuzipepala yachipwitikizi yotchedwa Expresso ikuyankha. Ponena za msonkhano wa ansembe 500 ku Fátima, nyuzipepalayo inati: “Malinga ndi mabishopu, nkofunika kuti wansembe asamakhale ndi zochitachita zina zambiri kotero kuti akhazikikenso kotheratu m’malo ake monga ‘mlaliki.’ . . . Ngati wansembe amasumika moyo wake wonse pa kulalikira Uthenga Wabwino, iye sadzakhala ndi nthaŵi ya kuchita zinthu zina.”
Mosiyana ndi zimenezo, Mboni za Yehova ku Portugal nzokangalika kufalitsa choonadi cha Baibulo m’njira iliyonse yotheka. Chifukwa chake, Akatolika oona mtima ambiri akupeza chidziŵitso cha Baibulo.
Carlota anali Mkatolika wodzipereka ndipo anali wa m’kagulu ka achichepere ka m’chipembedzocho. Analinso mphunzitsi pasukulu ya ana pamene Antônio, Mboni, anali kugwira ntchito. Monga mpainiya wokhazikika, kapena mtumiki wanthaŵi yonse, Antônio nthaŵi zonse ankalankhula ndi antchito anzake ponena za Baibulo panthaŵi ya chakudya chamasana. Tsiku lina Carlota anamfunsa za chikhulupiriro cha moto wa helo ndi kulambira Mariya. Antônio anamsonyeza zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani zimenezi, ndipo zimenezo zinali chiyambi cha makambitsirano ambiri a Baibulo. Pamene Carlota anafika pamsonkhano kwa nthaŵi yoyamba pa Nyumba ya Ufumu ya kumeneko, anasangalala kwambiri. Komabe, nthaŵi ya misonkhanoyo inawombana ndi nthaŵi ya kagulu kachipembedzo kamene iye analimo. Anaona kuti anafunikira kupanga chosankha. Kodi akanachitanji?
Carlota anasonkhanitsa kagulu konse ka achichepere ndi kufotokoza kuchokera m’Baibulo chifukwa chimene anali kuchokera m’chipembedzocho. Onse anatsutsa lingaliro lake, kusiyapo mtsikana wachichepere wotchedwa Stela, amene anamvetsera mosamalitsa. Pamene Carlota analankhula naye pambuyo pake, Stela anafunsa mafunso ambiri ponena za chiyambi cha moyo ndi chifuno chake. Carlota anampatsa buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?a nayamba naye phunziro la Baibulo.
Panthaŵiyo Carlota anapita patsogolo mwauzimu, anabatizidwa mu June 1991, nayamba kutumikira monga mpainiya wokhazikika pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi. Mu May 1992, iyeyo ndi Antônio anakwatirana, akumapitiriza pamodzi utumiki waupainiya pampingo woyandikana nawo pamene pali kusoŵa kwakukulu. Nanga bwanji za Stela? Anabatizidwa mu May 1993 ndipo tsopano akutumikira monga mpainiya wokhazikika.
Francisco wachichepere anali wachipembedzo kwambiri. Sande iliyonse ankapita ku Misa mmaŵa ndi kumapemphero a Korona masana. Ankatumikira monga sacristan, akumathandiza wansembe pochita Misa. Ankapemphera ndi kwa Mulungu kuti akakhale “woyera mtima” tsiku lina!
Francisco ankafunadi kukhala ndi Baibulo, ndipo tsiku lina bwenzi lake linambwereka. Anadabwa kuona kuti Mulungu ali ndi dzina, Yehova. (Eksodo 6:3; Salmo 83:18) Pamene anaŵerenga pa Eksodo 20:4, 5 kuti Mulungu samalola kugwiritsira ntchito mafano polambira, anadabwadi kwambiri! Poona kuti tchalitchi chinali chodzaza ndi mafano, anapemphera kwa Mulungu kuchokera pansi pa mtima kuti amthandize kumvetsetsa zinthu zonsezo zimene zinamsokoneza. Masiku angapo pambuyo pake anakumana ndi amene kale anali mnzake wapasukulu ndi kumfunsa chifukwa chake anasiyira sukulu yamadzulo.
“Tsopano ndimapita kusukulu yamadzulo yabwino koposa,” anayankha motero mnzakeyo.
“Ndi sukulu yanji imeneyo, ndipo ukuphunziranji?” anafunsa motero Francisco. Anadabwa kwambiri ndi yankho la mnzake.
“Ndikuphunzira Baibulo ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova,” mnzakeyo anamuuza motero. “Kodi ungafune kupita nane?”
Francisco sanakhulupirire zimene anaona pamsonkhano wake woyamba—nkhope zachimwemwe, zomwetulira; anthu olankhulana mwachikondi, ndi mwaubwenzi; ana atakhala pamodzi ndi makolo awo ndi kumamvetsera zimene zinali kulankhulidwa.
“Ndinali mlendo weniweni, koma ndinamva ngati mmodzi wa banjalo!” anatero Francisco. Kuyambira pamenepo iye amapezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. Tsopano Francisco akutumikira monga mkulu pampingo, ndipo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aŵiri, iye amasangalala ndi malonjezo aakulu a Ufumu opezeka m’Mawu a Mulungu.
Kuuza Choonadi Achibale
Manuela, mpainiya wokhazikika kudera la ku Lisbon, anasodza nsomba zauzimu zochuluka chifukwa cha kulimbikira kwake kuchitira umboni mwachikondi kwa anthu onse, kuphatikizapo achibale ake. Pakati pawo panali mlongo wake wakuthupi, José Eduardo, amene anaphunzira luso la kudzitetezera, ndi kugwiritsira ntchito zida. Anali ataswa malamulo nthaŵi zambiri kotero kuti pomalizira pake anaŵeruzidwa pa milandu 22 namangidwa zaka 20 m’ndende. Anali wachiwawa kwambiri kwakuti ngakhale andende anzake ankamuwopa, ndipo anaikidwa m’chipinda chayekha cholindidwa koposa.
Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri Manuela moleza mtima ankapita kukachezera José Eduardo, koma nthaŵi zonse ankakana uthenga wake wa Baibulo. Pomalizira pake, pamene buku la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? linatulutsidwa, analilandira, ndipo phunziro la Baibulo linayamba. Pomwepo anasintha kwambiri khalidwe lake. Mlungu umodzi pambuyo pake anapereka yekha umboni kwa andende 200, ndipo mlungu wotsatirapo kwa enanso 600. Anapatsidwa ndi chilolezo cha kuchezera andende anzake m’zipinda zina. Chifukwa cha kusintha kwakukulu kwa khalidwe lake, zaka zake zinachepetsedwa kukhala zaka 15. Atakhala m’ndende zaka 10, anamasulidwa chifukwa cha kudzisungira. Kuchokera pamenepo papita zaka zisanu, ndipo José Eduardo tsopano ndi Mboni yobatizidwa ya Yehova, akumatumikira monga mtumiki wotumikira pampingo wakwawo. Indedi ndi chitsanzo cha ‘mmbulu wokhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa’!—Yesaya 11:6.
Chifukwa cha kuyesetsa kwake kosalekeza pa kulalikira kwa am’banja mwake, Manuela asangalala kuthandiza mwamuna wake ndi am’banja mwake ena anayi kukhala achangu mu utumiki wa Yehova. Mwamuna wake tsopano ndi mtumiki wotumikira.
“Ndidzawapitikitsa ndi Chidyali ndi Mkwapulo”
Maria do Carmo ankakhala ku mlaga wina wa ku Lisbon pamene Mboni zinamfikira. Anakondwera ndi zimene anamva ndipo anapempha mwamuna wake, Antônio, ngati akanamlola kukhala ndi phunziro la Baibulo panyumba. “Usaziganizire nkomwe zimenezo!” anayankha motero. “Ngati ndidzapezapo Mboni za Yehova m’nyumba mwathu, ndidzawapitikitsa ndi chidyali ndi mkwapulo.” Ndiponso, Antônio anali mphunzitsi wa karate wa third-degree black belt. Motero Maria do Carmo anaganiza kuti azichitira phunziro lake la Baibulo kwina.
Pambuyo pake, Antônio anali kupita ku England ku maphunziro a masiku asanu ndi atatu a karate, ndipo Maria do Carmo analongedza mosamala m’sutukesi yake Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.b Popeza Antônio anali ndi nthaŵi yaikulu paulendo wake, anaŵerenga bukulo. Pamene anali kubwerera, chimphepo chinawomba ndegeyo mwamphamvu, ndipo inavutika potera. Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wake, Antônio anapemphera kwa Yehova.
Pamene Antônio anafika kunyumba, Mboni imene inali kuchititsa phunziro kwa mkazi wake inamuitanira kumsonkhano. Iye anavomera ndipo anaona kuti aliyense anali waubwenzi. Makonzedwe a phunziro la Baibulo anapangidwa, ndipo posapita nthaŵi, Antônio anadziŵa kuti anafunikira kupanga zosankha. Chotulukapo chake chinali chakuti analeka kuphunzitsa karate nayamba kuphunzitsa ophunzira ake mokhalira ndi moyo wamtendere tsopano ndi kunthaŵi zonse. Mmodzi wa iwo, nayenso wokhala ndi black belt, ali Mkristu wobatizidwa tsopano.
Ponena za Antônio, anabatizidwa mu April 1991. Tsiku limodzi pambuyo pa ubatizo wake, anayamba kutumikira monga mpainiya wothandiza. Patapita miyezi isanu ndi umodzi anayamba kutumikira monga mpainiya wokhazikika, ndipo mosataya nthaŵi anayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 12. Mu July 1993 anaikidwa monga mtumiki wotumikira mumpingo.
M’Magawo Ofoledwa Kaŵirikaŵiri
M’madera ambiri a dzikoli, magawo amafoledwa pafupifupi mlungu uliwonse. Kodi ndi motani mmene Mboni zimapitirizira ntchito yawo ya “kusodza” mobala zipatso?
João amayesetsa kulankhula ndi anthu onse panyumba iliyonse. Pamene anafika panyumba ya mkazi wina, iye anafunsa ngati panalinso ena amene anali kukhala panyumbapo. Mkaziyo anayankha kuti anali kukhala ndi mwamuna wake ndi ana ake aamuna aŵiri, koma anati sikwapafupi kulankhula nawo popeza anali kugwira ntchito ndipo anali kufika panyumba madzulo okha. Motero João anapitiriza umboni wake pa nyumba zina. Patapita ngati ola limodzi ndi theka, mwamuna wina anamfikira.
“Munanena kuti mukufuna kulankhula nane,” mwamunayo anatero kwa João. “Ndiuzeni chonde zimene mukufuna.”
“Koma pepani, sindikudziŵani,” anayankha motero João, atadabwa. “Kodi ndinu yani?”
“Ndine Antônio, ndimakhala m’khwalala limene lino. Munali mwauza amayi kuti mukufuna kulankhula ndi banja lonse, motero ndadza kudzamva zimene munali kufuna.”
João anapereka umboni wabwino kwa Antônio namyambitsa phunziro la Baibulo. Pambuyo pa phunziro lachiŵiri, Antônio anapempha kuti azichita phunzirolo kaŵiri pamlungu. Patangopita miyezi inayi, iye anatsagana ndi João ndi kuyamba kulalikira uthenga wabwino m’khwalala limene anali kukhala. Patapita miyezi itatu, anabatizidwa.Posachedwapa amayi wake anayamba kuphunzira Baibulo. Sitaona nanga kufunika kwa kulankhula ndi apabanja onse mu utumiki!
Zokumana nazo zotere zodzetsa chimwemwe zimasonyeza kuti pakali usodzi wauzimu wochuluka wofunika kuchitika m’madzi a Portugal. Yehova wadalitsa Mboni zachangu kumeneko ndi zikwi za maphunziro a Baibulo opita patsogolo. Pamene akufunafuna njira zowonjezereka kuti afalitse choonadi cha Baibulo kwa onse, mawu a mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Filipi akukwaniritsidwadi ku Portugal lerolino kuti: “Monsemo . . . Kristu alalikidwa.”—Afilipi 1:18.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
SPAIN
PORTUGAL
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
Mboni ku Portugal zimagwiritsira ntchito mpata uliwonse kudziŵikitsa choonadi cha Baibulo