Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—1995 | April 1
    • 20. Kodi nchifukwa ninji chikondi cha Mulungu kwa ife sichili chodzikhululukira nacho pa kudzilingalira tokha kukhala wofunika kapena kudzikweza kwathu?

      20 Palibe Mkristu wolingalira bwino amene angaone umboni wotero wa chikondi cha Mulungu ndi kuŵerengera kukhala chodzikhululukira chake pa kudzilingalira kukhala wofunika kwambiri kuposa mmenedi iye alili. Paulo analemba kuti: “Ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagaŵira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.” (Aroma 12:3) Chotero pamene kuli kwakuti timasangalala kukhala m’chikondi cha Atate wathu wakumwamba, tiyeni tikhale olama maganizo ndi kukumbukira kuti kukoma mtima kwa Mulungu sitinakuyenerere.​—Yerekezerani ndi Luka 17:10.

      21. Kodi ndi bodza lausatana lotani limene tiyenera kukana nthaŵi zonse, ndipo ndi choonadi chaumulungu chotani chimene tiyenera kusinkhasinkha nthaŵi zonse?

      21 Aliyense wa ife achitetu zonse zimene angathe kukana malingaliro onse amene Satana amachirikiza m’dziko lino lakale lomafa. Zimenezo zimaphatikizapo kukana lingaliro lakuti tili opanda pake kapena osakondedwa. Ngati moyo m’dongosolo lino wakuphunzitsani kudziona inu eni monga chopinga chachikulu kwambiri chosakhoza kuchotsedwa ngakhale ndi chikondi chachikulu cha Mulungu, kapena kuona ntchito zanu zabwino kukhala zosanunkha kanthu kwakuti ngakhale maso ake oona zonse sangathe kuziona, kapena kuona machimo anu kukhala aakulu kambiri kwakuti sangatheke kukwiriridwa ndi imfa ya Mwana wake wamtengo wapataliyo, mwaphunzitsidwa bodza. Kanani mabodza otero ndi kunyansidwa nawo kwenikweni! Nthaŵi zonse tiyeni tikumbukire mawu a mtumwi Paulo ouziridwa a pa Aroma 8:38, 39: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”

  • Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino—MotanI?
    Nsanja ya Olonda—1995 | April 1
    • Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino​—MotanI?

      “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, . . . tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.”​—AHEBRI 10:24, 25.

      1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kuti Akristu oyambirira apeze chitonthozo ndi chilimbikitso pa kusonkhana kwawo pamodzi? (b) Kodi ndi uphungu wotani wa Paulo umene unasonyeza za kufunika kwa kusonkhana pamodzi?

      ANASONKHANA chobisala, ataunjikana m’nyumba yotsekedwa. Kunjako, kunali ngozi yokhayokha. Mtsogoleri wawo, Yesu, anali atangophedwa kumene poyera, ndipo anali atachenjeza otsatira ake kuti akachitiridwa moipa mofanana naye. (Yohane 15:20; 20:19) Koma pamene anali kulankhula monong’ona ponena za Yesu wawo wokondedwa, kukhala pamodziko mwina kunawachititsa kumva ngati osungika pang’ono.

      2 Pamene zaka zinapyola, Akristu anayang’anizana ndi mayesero osiyanasiyana ndi mazunzo. Mofanana ndi ophunzira oyambirira amenewo,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena