Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 4/15 tsamba 27
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Akula ndi Priskila—Banja Lopereka Chitsanzo Chabwino
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Lalikirani ndi Cholinga Chopanga Ophunzira
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Malo a Nyimbo Pakulambira Kwamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 4/15 tsamba 27

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwazimvetsa bwino nkhani za m’makope aposachedwa a Nsanja ya Olonda? Ngati mwatero, mudzakondwa kukumbukira zotsatirazi:

◻ Kodi ndi motani mmene mabanja ambiri lerolino atsatirira chitsanzo chabwino chimene anasiya Akula ndi Priskila?

Akula ndi Priskila anatumikira m’mipingo ingapo yosiyanasiyana. Mofanana nawo, Akristu amakono ambiri achangu adzipereka kusamukira kumene kuli kusoŵa kwakukulu. Iwonso amakhala ndi chimwemwe ndi chikhutiro poona zinthu za Ufumu zikukula ndi pokhoza kukhala ndi mabwenzi achikristu apamtima.​—12/15, tsamba 24.

◻ Kodi lingaliro la Baibulo pa moŵa nlotani?

Lingaliro la Baibulo pa moŵa nlolinganiza. Baibulo limanenadi kuti vinyo ali mphatso yochokera kwa Mulungu. (Salmo 104:1, 15) Komanso, limaletsa kumwa kopambanitsa. (Luka 21:34; 1 Timoteo 3:8; Tito 2:3; 1 Petro 4:3)​—12/15, tsamba 27.

◻ Kodi mbali yapadera m’buku la Baibulo la Hagai njotani?

Ngakhale kuti buku la Hagai lili ndi mavesi 38 okha, dzina la Mulungu likupezeka nthaŵi 35. Ulosi umenewu umatha mphamvu yake pamene dzina lamtengo wapatali la Yehova alichotsamo ndi kuikamo dzina laulemu la “Ambuye.”​—1/1, tsamba 6.

◻ Kodi tingaphunzireponji pa machimo a Davide ndi Manase?

Ngakhale kuti Yehova anakhululukira Davide ndi Manase, amuna ameneŵa​—ndi Aisrayeli onse​—anavutika ndi zotulukapo za machitidwe awo auchimo. (2 Samueli 12:11, 12; Yeremiya 15:3-5) M’njira yofananayo, ngakhale kuti Yehova amakhululukira ochimwa, pangakhalebe zotulukapo za machitidwe awo zimene iwo sangapeŵe.​—1/1, tsamba 27.

◻ Kodi ‘mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino’ wa Ufumu wa Mulungu ali ‘okongola’ motani? (Yesaya 52:7)

Mapazi ndiwo amayendetsa munthu pokalalikira kwa ena. Mapaziwo amaimiradi munthuyo. Chotero kwa ambiri omwe amamva uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuulabadira, mapazi a amithenga otero alidi okongola.​—1/15, tsamba 13.

◻ Kodi ndi mbali ziŵiri ziti zimene ntchito ya ‘kulalikira uthenga wabwino’ ili nazo? (1 Akorinto 9:16)

Choyamba, tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Mbali yachiŵiri ya ntchito imeneyi imaloŵetsamo kuphunzitsa awo amene amalabadira chilengezo cha Ufumu.​—1/15, tsamba 23.

◻ Kodi ndi mapindu aumwini ati omwe timapeza mwa kuimba nyimbo za Ufumu pamisonkhano ya mpingo?

Kuimba kumatipatsa mpata wofotokoza malingaliro athu kwa Mlengi wathu. (Salmo 149:1, 3) Pamene tiimba mochokera mumtima pampingo, zingakonzekeretse maganizo athu ndi mtima wathu kaamba ka programu yotsatira. Kungatisonkhezere kuchita zambiri pakulambira Yehova.​—2/1, tsamba 28.

◻ Kodi tsiku la kufa lingapose motani tsiku la kubadwa? (Mlaliki 7:1)

Tsiku la imfa lingapose tsiku la kubadwa ngati munthuyo anapanga dzina labwino kwa Yehova, amene akhoza kuukitsa okhulupirika amene amwalira. (Yohane 11:25)​—2/15, tsamba 12.

◻ Kodi nchifukwa ninji buku la Mlaliki liyenera kutithandiza aliyense payekha?

Lingathandize aliyense wa ife kuwongolera kaonedwe kathu ka moyo ndi zimene timasumikapo maganizo. (Mlaliki 7:2; 2 Timoteo 3:16, 17)​—2/15, tsamba 16.

◻ Kodi Mboni za Yehova zili zoumirira mwambo?

Ayi. Pamene kuli kwakuti zili ndi zikhulupiriro zolimba zachipembedzo, sizili zoumirira mwambo malinga ndi tanthauzo limene liwulo lakhala nalo. Sizimachita zionetsero ndi chiwawa kwa aja omwe sagwirizana nazo. Zimatsanzira Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu.​—3/1, tsamba 6.

◻ Kodi kusadziŵa nthaŵi yeniyeni imene Yesu adzadza kudzapereka chiweruzo cha Mulungu kumawakhudza motani Akristu?

Kumachititsa Akristu kukhala maso nthaŵi zonse ndi kuwapatsa mpata tsiku ndi tsiku wa kusonyeza kuti akutumikira Yehova ndi zolinga zopanda dyera.​—3/1, tsamba 13.

◻ Kodi tiyenera kulingalira chiyani tisanasumire mlandu mbale amene watinyenga?

Tiyenera kulingalira za zimene zingachitikire ifeyo, ena ophatikizidwamo, mpingo, ndi akunja. (1 Akorinto 6:7)​—3/15, tsamba 20.

◻ Kodi chimwemwe chenicheni chingapezeke motani?

Chimwemwe chenicheni ndicho mkhalidwe wa mtima, wozikidwa pa chikhulupiriro chenicheni ndi unansi wabwino ndi Yehova. (Mateyu 5:3)​—3/15, tsamba 23.

◻ Kodi Mkristu ayenera kuchitanji ataitanidwa ku ntchito yaujuli?

Mkristu aliyense woitanidwa ku ntchito yaujuli ayenera kusankha njira imene ayenera kutsatira, malinga ndi chidziŵitso chake cha Baibulo ndi chikumbumtima chake. (Agalatiya 6:5)​—4/1, tsamba 29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena