Nyimbo 38
Kusonyeza Kukhulupirika
1. Yehova ali ndi anthu
Olengeza dzinalo,
Monga mpingo wogonjera
Ndi wodziperekadi.
Pagomelo lauzimu
Amadya moyamika,
Amkondweretsa mumawu
Ndi zochita zawozo.
2. Tikhale odalirika
Mumpingo wa Mulungu,
Tisonyeze chipiliro
Chinkana pamavuto.
Tetezani zinthu zake,
Zisawonongedwetu;
Pamene zawopsezedwa,
Tidzachenjezeratu.
3. Tithandizedi abale,
Ofo’ka, atsopano,
Muntchito ndi m’kuphunzira
Tithandize mofatsa.
Monga m’moyo wabanjawo,
Tidzadaliranabe,
Tiyenera kukhalabe
Okhulupirikadi.
4. Kukhulupirika kwathu,
Tiyeni tisonyeze
Kwa oyenererawonso
Poyendatu m’Chikristu.
Kusonyezatu Satana
Ngwonama, Ya ngwowona.
Tikakhulupirikatu,
Tidzakondweretsa Ya.