Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Wachingelezi wa dzina Losaiŵalika limeneli . . . m’matembenuzidwe amakono a bukhu la Masalmo mulibe chikaikiro chirichonse ponena za matchulidwe olondola kwambiri kukhala Yahweh; koma kokha kuchokera ku umboni wothandiza wosankhidwa mwachindunji pamaziko achikhumbo cha kukondweretsa makutu ndi maso a anthu onse m’nkhani yamtundu uwu, mu imene chinthu chachikulu chiri kuvomerezedwa kosavuta kwa dzina la Mulungu lodziŵika.”—(London, 1911), p. 29.

      Pambuyo pakukambitsirana matchulidwe osiyanasiyana, profesala Wachijeremani Gustav Friedrich Oehler anati: “Kuyambira tsopano kunkabe mtsogolo ndikugwiritsira ntchito dzina lakuti Yehova, chifukwa chakuti, kwenikweni, dzinali tsopano lakhala lozoloŵereka kwambiri m’chinenero chathu, ndipo silingaloŵedwe mmalo.”—Theologie des Alten Testaments, kope lachiŵiri (Stuttgart, 1882), p. 143.

      Wophunzira Wachijesuit Paul Joüon akufotokoza kuti: “M’matembenuzidwe athu, mmalo mwa mpangidwe (woyerekezeredwa) wakuti Yahweh, tagwiritsira ntchito mpangidwe wakuti Jéhovah . . . umene uli mpangidwe wovomerezedwa m’kulemba wogwiritsiridwa ntchito m’Chifrenchi.”—Grammaire de l’hébreu biblique (Rome, 1923) mawu amtsinde pa p. 49.

      Maina ambiri amasintha pang’ono pamene asunthidwa kuchoka m’chinenero china kunka ku chinzake. Yesu anabadwa ali Myuda, ndipo dzina lake m’Chihebri mwinamwake linali kutchulidwa kuti Ye·shuʹa‛, koma olemba ouziridwa a Malemba Achikristu sanakaikire kugwiritsira ntchito mpangidwe Wachigiriki wa dzinalo, I·e·sousʹ. M’zinenero zina zochuluka kwambiri matchulidwewo ngosiyana pang’ono, koma timagwiritsira ntchito momasuka mpangidwe umene uli wozoloŵereka m’chinenero chathu. Ziri chimodzimodzi ndi maina ena Abaibulo. Pamenepa, kodi ndimotani, mmene tingasonyezere ulemu woyenerera kwa Munthu amene ali mwini dzina lofunika koposa onse? Kodi kungakhale mwakusanena konse kapena kusalemba dzina lake chifukwa chakuti kwenikweni sitidziŵa mmene linali kutchulidwira poyambapo? Kapena, mmalo mwake, kodi kukakhala mwa kugwiritsira ntchito matchulidwe ndi masupelo amene ali ofala m’chinenero chathu, pamene titamanda Mwiniyo ndi kudzisungira ife eni monga olambira ake m’njira imene imamlemekeza?

      Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kudziŵa ndi kugwiritsira ntchito dzina lake la Mulungu?

      Kodi muli ndi unansi wapafupi ndi munthu aliyense amene simumadziŵa dzina lake? Kaŵirikaŵiri kwa anthu amene Mulungu ali wopanda dzina ali kokha mphamvu yopanda moyo, saali munthu weniweni, osati munthu amene iwo amadziŵa ndi kukonda ndi amene angalankhule naye m’pemphero kuchokera pansi pa mtima. Ngati iwo apemphera, mapemphero awo amangokhala dzoma chabe, kubwerezedwa kwamwambo kozoloŵereka kwa mawu oloŵezedwa pamtima.

      Akristu owona ali ndi ntchito yochokera kwa Yesu Kristu ya kupanga anthu amitundu yonse kukhala ophunzira. Pophunzitsa anthu amenewa, kodi kukakhala kotheka motani kudziŵa Mulungu wowona kukhala wosiyana ndi milungu yonama ya amitundu? Kuli kokha mwakugwiritsira ntchito dzina Lake, monga momwe Baibulo lenilenilo limachitira.—Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 8:5, 6.

      Eks. 3:15: “Mulungu ananena . . . kwa Mose, Ukatero ndi ana Israyeli, Yehova, Mulungu wamakolo anu . . . anandituma kwa inu; iri ndidzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndichikumbukiro changa m’mibadwo mibadwo.”

      Yes. 12:4: “Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.”

      Ezek. 38:17, 23: “Atero Ambuye Yehova . . . momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”

      Mal. 3:16: “Iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi bukhu lachikhumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.”

      Yoh. 17:26: “[Yesu anapemphera kwa Atate wake kuti:] Ndinazindikiritsa iwo [otsatira ake] dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi ine mwa iwo.”

      Mac. 15:14: “Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.”

      Kodi Yehova wa mu “Chipangano Chakale” ndiye Yesu mu “Chipangano Chatsopano”?

      Mat. 4:10, NW: “Yesu anati kwa iye: ‘Choka, Satana! Pakuti kwalembedwa, “Ndiye Yehova [“Ambuye,” KJ ndi ena] Mulungu wako amene uyenera kumlambira, ndipo ndi kwa iye yekha kumene uyenera kupereka utumiki wopatulika.”’” (Mwachiwonekere Yesu sanali kunena kuti iye mwiniyo anayenera kulambiridwa.)

      Yoh. 8:54: “Yesu anayankha [Ayuda]: Ngati ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu.” (Malemba Achihebri amadziŵikitsa poyera Yehova kukhala Mulungu amene Ayuda anadzinenera kukhala akulambira. Yesu anati, sikuti iyemwini anali Yehova, koma kuti Yehova anali Atate wake. Panopa Yesu anamveketsa bwino kwambiri kuti iye ndi Atate wake anali anthu olekana.)

      Sal. 110:1: “Yehova ananena kwa Ambuye wanga [wa Davide], Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.” (Pa Mateyu 22:41-45, Yesu anafotokoza kuti iye mwiniyo anali “Ambuye” wa Davide, wotchulidwa m’salmo limeneli. Chotero Yesu saali Yehova koma ndiye munthuyo amene mawu a Yehova panopa analunjikitsidwako.)

      Afil. 2:9-11: “Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa iye [Yesu Kristu] nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo lirilonse lipinde la za m’mwamba ndi za padziko ndi za pansi padziko, ndi malirime onse avomereze kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. [Dy imati: “ . . . lirime lirilonse liyenera kuvomereza kuti Ambuye Yesu Kristu ali muulemelero wa Mulungu ndi Atate.” Kx ndi CC ali ndi mawu ofanana, koma mawu amtsinde a Kx amavomereza kuti: “ . . . mwinamwake Chigiriki chiri kwakulukulu chotembenuzidwa moyenerera kuti ‘kuulemerero,’” ndipo NAB ndi JB amalitembenuza motero.]” (Tawonani kuti Yesu Kristu panopa akusonyezedwa kukhala wosiyana ndi Mulungu Atate ndipo ngwogonjera kwa Iye.)

      Kodi ndimotani mmene munthu angakondere Yehova ngati angafunikirenso Kumuwopa?

      Baibulo limatiuza kuti tiyenera ponse paŵiri kukonda Yehova (Luka 10:27) ndi kumuwopa. (1 Pet. 2:17; Miy. 1:7; 2:1-5; 16:6) Kuwopa Mulungu koyenerera kudzatipangitsa kukhala osamala kwambiri kupeŵa kuchititsa mkwiyo wake. Kukonda kwathu Yehova kudzatisonkhezera kufuna kuchita zinthu zimene zimamkondweretsa, kusonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka kusonyeza kwake chikondi ndi kukoma mtima kwachifundo kosaŵerengeka.

      Zitsanzo: Mwana moyenerera amakhala ndi mantha oyenera a kusakondweretsa atate wake, koma kuyamikira zonse zimene atate wake amamchitira kuyeneranso kusonkhezera mwanayo kusonyeza chikondi chenicheni kwa atate wake. Katswiri wosambira mwa chithandizo chamakina osambirira anganene kuti amakonda nyanja, koma kuiwopa koyenerera kumamchititsa kuzindikira kuti pali zinthu zina zimene ayenera kupeŵa kuchita. Mofananamo, kukonda kwathu Mulungu kuyenera kugwirizanitsidwa ndi mantha oyenerera a kusachita kanthu kalikonse kamene kadzachititsa kuti timkwiyitse.

  • Yesu Kristu
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Yesu Kristu

      Tanthauzo: Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Mwana yekha wolengedwa ndi Yehova yekha. Mwanayo ndiye wachisamba wa chilengedwe chonse. Kudzera mwa iye zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi zinalengedwa. Ndiye munthu wachiŵiri kwa munthu wamkulu koposa onse m’chilengedwe chonse. Ali Mwana ameneyu amene Yehova anatuma kudziko lapansi kudzapereka moyo wake kukhala dipo la anthu, mwa kutero anatsegula njira yomka kumoyo wamuyaya kaamba ka ana a Adamu amene akasonyeza chikhulupiriro. Mwana mmodzimodzi ameneyu, wobwezeretsedwa ku ulemerero wakumwamba, tsopano akulamulira monga Mfumu, limodzi ndi ulamuliro wa kuwononga oipa onse ndi kukwaniritsa chifuno choyambirira kaamba ka dziko lapansi cha Atate wake. Mpangidwe Wachihebri wa dzina lakuti Yesu umatanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso”; Kristu ndiro liwu lofanana ndi Lachihebri Ma·shiʹach (Mesiya), kutanthauza “Wodzozedwa.”

      Kodi Yesu Kristu anali munthu weniweni, wa m’mbiri?

      Baibulo lenilenilo ndiro umboni waukulu wakuti Yesu Kristu ndimunthu wa m’mbiri. Cholembedwa cha Uthenga Wabwino sichiri mafotokozedwe osamvekera bwino a zochitika panthaŵi ina yosadziŵika bwino ndipo pamalo osatchulidwa dzina. Chimafotokoza bwino momvekera nthaŵi ndi malo mwatsatanetsatane kwambiri. Mwachitsanzo, wonani Luka 3:1, 2, 21-23.

      Wolemba mbiri Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba Josephus anasonya ku kuponyedwa miyala kwa “Yakobo, mbale wa Yesu amene anali kutchedwa Kristu.” (The Jewish Antiquities, Josephus, Bukhu XX, gawo 200) Umboni wachindunji ndi wabwino kwambiri ponena za Yesu, wopezedwa m’Bukhu XVIII, chigawo 63, 64, wakaikiridwa ndi ena amene amanena kuti uyenera kukhala kaya utawonjezeredwa pambuyo pake kapena kupititsidwa patsogolo ndi Akristu; koma kukuvomerezedwa kuti mpambo wa mawu ndi kalembedwe ziri kwakukulukulu za Josephus, ndipo mawuŵa akupezeka m’malemba onse apamanja amene ali opezeka.

      Tacitus, wolemba mbiri Wachiroma amene anakhalako

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena