Nyimbo 9
Madalitso a Yehova Alemeleretsa
1. Yehova amatidalitsadi,
Pomwe timtumikira (mogwirizana).
Timakondwa kwambiri pobzala
Mawu opatsa nzeru.
2. Ngakhale mazunzo ngochuluka,
Ndipo timapilira (osalefuka),
Poti tiwona chifundo cha Ya,
Timalimbika mtima.
3. Ngati tichita zomwe tingathe,
Kuchita zabwinozo (moyenelera),
Yehova wokhulupirikayo,
Adzakondwera nafe.
4. Chotero tikhaletu achangu.
Tikhale ndi dalitso (mutidalitse)!
Adzavumbula chikondi chake;
Popandadi ululu.