Kodi Mumalemekeza Malo Anu Olambirira?
1 Kuyambira pachiyambi penipeni pa uthenga wabwino, nthaŵi zonse Akristu anali ndi malo okhazikika ndi otsimikizika olambirira Mulungu. Baibulo limafotokozanso mfundo imeneyi, ndipo limatchula misonkhano yosiyanasiyana imene magulu a Akristu ankachita nthaŵi zonse. Masiku ano, Mboni za Yehova zimatsatira zimene atumwi anali kuchita. Izo zimagwiritsira ntchito malo osonkhanira otchedwa Nyumba ya Ufumu. Kumeneko zimaphunzitsidwa kukhala alaliki a uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14) Panyumba ya Ufumupo, izo zimaphunziranso Malemba, kupemphera, ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake. Zimenezi n’zogwirizana ndi langizo la m’Baibulo limene lili pa Ahebri 10:24, 25. Pamenepo pamati: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.”
2 Kugwiritsira Ntchito Moyenera Malo Athu Olambirira: Nsanja ya Olonda yachingelezi ya October 15, 1969 inati: “Mkhalidwe wauzimu umene umakhala pa Nyumba ya Ufumu ndi weniweni, ndipo umakhalapo chifukwa chokonda kwambiri kulambira koona ndiponso malangizo a m’Baibulo. Ndiponso, kuwala ndi kuoneka bwino kwa m’Nyumba ya Ufumuyo kumalimbikitsa anthu amene asonkhanawo kukhala ochezeka ndi aubwenzi, osati kupanikizika ndi mwambo wopatulika wosadziŵika bwino wa anthu.” Inde, pamakhalanso kusamala kuti nthaŵi zonse Nyumba ya Ufumu izigwiritsidwa ntchito mwaulemu.
3 N’zosangalatsa kuti Nyumba za Ufumu zambiri zikuyang’aniridwa bwino kwambiri. Komabe, zikuoneka kuti mipingo ina ifunika kusamala kwambiri pa nkhani imeneyi. Akulu ndi atumiki otumikira ayenera kupereka chitsanzo mwachangu posonyeza kulemekeza Nyumba ya Ufumu. Nthaŵi zambiri pamakhala mkulu mmodzi kapena aŵiri ndi atumiki otumikira amene amapatsidwa ntchito yoyang’anira nkhani zokhudza kusamalira Nyumba ya Ufumu. Kumene mipingo ingapo imagwiritsira ntchito nyumba imodzi, komiti ya akulu imayang’anira nkhani zimenezi. Kodi tikuchita bwanji pa nkhani imeneyi? Ngakhale kuti anthu ena amapatsidwa mwachindunji ntchito yoyang’anira zimenezi, atumiki otumikira ndi akulu onse ayenera kuonetsetsa kwambiri mmene nyumbayo ilili. Iwo amazindikira kuti Nyumba ya Ufumuyo yapatulidwira Yehova ndipo imagwiritsidwa ntchito pomulambira. Motero, onse ayenera kuonetsetsa kuti Nyumba ya Ufumu ndi yaukhondo m’kati ndi kunja komwe.
4 Akulu sayenera kuzengereza akaona kuti nyumbayo ikufunika kukonzedwa. (2 Mbiri 24:5, 13; 29:3; 34:8; Neh. 10:39; 13:11) M’mipingo ina, Nyumba ya Ufumu amaiyang’ana nthaŵi zonse kuti akaona penapake pofunika kukonza, akonze mwamsanga. Dziŵitsani ofesi ya nthambi ngati pali malo ena amene afunika ntchito yaikulu yokonza. Sungani chiŵerengero cha zinthu zogwiritsa ntchito pofuna kuonetsetsa kuti zipangizo zofunika zilipo ndipo mungazigwiritsire ntchito mosavuta. Ngati pali malo osungira zipangizo zogwiritsira ntchito ndiponso zoyeretsera, akulu ndi atumiki otumikira ayenera kumakhala ndi chidwi kuona mmene malowo alili, kuonetsetsa kuti ndi aukhondo nthaŵi zonse. Amene amagwira ntchito pa malo potengera mabuku ndi magazini pa Nyumba ya Ufumu angasonyeze kuti amafuna panyumbapo kukhala paukhondo mwa kuonetsetsa kuti makatoni opanda kanthu sali mbwee panyumbayo.
5 Mwakupereka chitsanzo, akulu ndi atumiki otumikira angathandize mpingo wonse kusonyeza changu cha pa Nyumba ya Ufumu. (Aheb. 13:7) Onse angasonyeze ulemu woyenera mwa kuyeretsa nawo pa nyumbapo ndiponso kuonetsetsa kuti kodi nyumba yonse ikuoneka bwanji. Pa Mateyu 18:20 Yesu ananena kuti: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.” Inde, Yesu amakondwera ndi zimene timachita pamene tisonkhana pamodzi kudzalambira Yehova. Zimenezi zimaphatikizapo misonkhano iliyonse imene imachitika m’nyumba za anthu ndiponso misonkhano yaikulu monga misonkhano yachigawo ndi yadera.
6 Kwa Mboni za Yehova miyandamiyanda, palibe malo ena amene ali apamtima kwambiri kuposa Nyumba ya Ufumu, malo awo amene amalambiriramo nthaŵi zonse. Izo zimalemekeza moyenera malowo. Zimasonyeza mzimu wakhama poisamalira, ndipo nthaŵi zonse zimayesetsa kuigwiritsira ntchito moyenera. Nanunso tsatiranitu langizo limene Yehova mwini anapereka lakuti: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu.”—Mlal. 5:1.