Chikhulupiriro Chinamsonkhezera Kuchitapo Kanthu
PAMENE Yehova anatuma Mose kutsogolera mtundu wa Israyeli kutuluka muukapolo wa Igupto, poyamba Mose anakana akumati: “Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosoŵa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa mkamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.” (Eksodo 4:10) Inde, Mose anamva kukhala wosayenerera ntchito yaikuluyo.
Mofananamo lerolino, atumiki a Yehova ambiri nthaŵi zina amamva kukhala osakhoza kukwaniritsa ntchito zimene apatsidwa. Mwachitsanzo, woyang’anira wachikristu wina wotchedwa Theodore akusimba kuti: “Pa zinthu zonse zimene Yehova amandipempha kuchita, utumiki wakumunda ndiwo wovuta koposa. Pamene ndinali wamng’ono, ndinali kupita pakhomo mwamsanga, kuyerekezera kuti ndikugogoda, ndi kuchokapo mwakachetechete, ndikumayembekezera kuti palibe adzandimva kapena kundiona. Pamene ndinali kusinkhuka, ndinasiya kuchita zimenezo, koma lingaliro lopita kukhomo ndi khomo linali kundidwalitsa mwakuthupi. Ngakhale lerolino, ndimadwala ndisanapite mu utumiki, komabe ndimapita.”
Kodi nchiyani chimene chinachititsa Mose ndi Mboni zamakono monga Theodore kulimbana ndi mantha otere? Baibulo limayankha kuti: “Ndi chikhulupiriro [Mose] anasiya Aigupto, . . . pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona Wosaonekayo.”—Ahebri 11:27.
Zoonadi, mwa kukhala ndi chikhulupiriro pa Yehova, Mose anatha kugonjetsa malingaliro ake a kumva kukhala wosakhoza kuchita zinthu ndi kukwaniritsa ntchito zake zimene anapatsidwa monga woweruza, mneneri, mtsogoleri wa mtundu, nkhoswe ya pangano la Chilamulo, mtsogoleri wankhondo, wolemba mbiri, ndi wolemba Baibulo.
Mofananamo, pamene tikhala ndi chikhulupiriro chonga cha Mose, tidzayenda monga ngati “kuona Wosaonekayo.” Chikhulupiriro chotero chimasonkhezera kulimba mtima, chikumatikhozetsa kunyamula mathayo athu achikristu—ngakhale pamene tikumva kukhala osakhoza kuchita zinthu.