Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Lalikirani Choonadi Chonena za Yesu
    Utumiki wa Ufumu—2002 | November
    • Lalikirani Choonadi Chonena za Yesu

      1 Akristu odzozedwa, mothandizana ndi anzawo a nkhosa zina, ali ndi ntchito yochitira ‘umboni za Yesu.’ (Chiv. 12:17) Imeneyi ndi ntchito yofunika kwambiri, chifukwa chakuti chipulumutso n’chotheka kudzera mwa Yesu yekhayo basi.—Yoh. 17:3; Mac. 4:12.

      2 ‘Njira, Choonadi, ndi Moyo’: Yesu anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yoh. 14:6) Tingalankhule ndi Mulungu m’pemphero komanso tingakhale naye pa ubwenzi wabwino kudzera mwa Yesu yekha basi, amene ndi “njira.” (Yoh. 15:16) Yesu ndi “choonadi” chifukwa chakuti maulosi ndiponso zinthu za m’Malemba Achihebri zinakwaniritsidwa mwa iye. (Yoh. 1:17; Akol. 2:16, 17) Zoonadi, ntchito yeniyeni ya ulosi woona ndiyo kuunikira udindo wake waukulu pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu. (Chiv. 19:10) Komanso, Yesu ndi “moyo.” Kuti onse apeze mphatso ya moyo wosatha, ayenera kukhulupirira nsembe ya dipo imene anapereka.—Yoh. 3:16, 36; Aheb. 2:9.

      3 Mutu Komanso Mfumu Yolamulira: Anthu ayeneranso kuzindikira ulamuliro waukulu umene Yehova wapereka kwa Mwana wake. Yesu waikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, amene ‘anthu ayenera kumumvera.’ (Gen. 49:10) Komanso, Yehova wamuika iye kukhala Mutu wa mpingo. (Aef. 1:22, 23) Tifunika kuthandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kudziŵa momwe Yesu amayang’anira mpingo ndiponso momwe amagwiritsira ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kupereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.”—Mat. 24:45-47.

      4 Mkulu wa Ansembe Wachifundo: Popeza kuti Yesu pamene anali padziko lapansi pano anakumana ndi mayesero ndi mavuto, “akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.” (Aheb. 2:17, 18) N’zolimbikitsa kwambiri kwa anthu opanda ungwiro kudziŵa kuti Yesu amamva chifundo ndi zofooka zawo ndipo amawapempherera mwachikondi. (Aroma 8:34) Pa maziko a nsembe ya Yesu ndi mwa ntchito yake monga Mkulu wa Ansembe, tingalankhule ndi Yehova ‘molimbika mtima’ kuti tipeze ‘thandizo panthaŵi yakusoŵa.’—Aheb. 4:15, 16.

      5 Kulimbikira kwathu kuuza ena choonadi chonena za Yesu kuwalimbikitsetu iwowo kuti nawonso amumvere ndi kum’tumikira.—Yoh. 14:15, 21.

  • Thandizani Woyang’anira Phunziro Lanu la Buku la Mpingo
    Utumiki wa Ufumu—2002 | November
    • Thandizani Woyang’anira Phunziro Lanu la Buku la Mpingo

      1 Tonse timapindula kwambiri ndi Phunziro la Buku la Mpingo. Mwezi watha, tinakambirana njira zimene woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo amakwaniritsira ntchito yake. Koma kodi tingatani kuti tim’thandize ntchito imene amagwira kotero kuti ife ndi anthu ena tipindule?

      2 Pezekanipo Mlungu Uliwonse: Chifukwa chakuti magulu a phunziro la buku amakhala ndi anthu ochepa, zimathandiza kwambiri mukapezekapo. Chikhale cholinga chanu kupezekapo mlungu uliwonse. Mungathandizenso mwa kufika nthaŵi yabwino, chifukwa zimenezi zimathandiza woyang’anira kuyamba msonkhanowo moyenera.—1 Akor. 14:40.

      3 Mayankho Olimbikitsa: Njira ina imene mungathandizire ndiyo kukonzekera bwino ndi kukayankha zolimbikitsa. Kaŵirikaŵiri mayankho amene amakhala ndi mfundo imodzi amakhala abwino, ndipo izi zimalimbikitsanso ena kuyankha. Peŵani kuyankha ndime yonse. Ngati mfundo ina pa ndimeyo yakukhudzani mtima, pangitsani makambiranowo kukhala osangalatsa mwa kunena mfundo yanuyo.—1 Pet. 4:10.

      4 Ngati muli ndi mwayi woŵerenga ndime pa phunzirolo kuti gulu lonse lipindule, yesetsani kukwaniritsa mbali yanuyo. Kuŵerenga bwino kumathandiza kuti phunzirolo likhale labwino kwambiri ndiponso losangalatsa.—1 Tim. 4:13.

      5 Umboni wa Kagulu: Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda imachitikira m’malo ambiri a phunziro la buku, ndipo kupezekapo kwanu pamisonkhano imeneyi kumathandiza woyang’anira potsogolera ntchito yolalikira. Onani misonkhano imeneyi kukhala mpata wodziŵana bwino ndi abale anu ndiponso wowalimbikitsa.

      6 Malipoti a Utumiki Wakumunda: Kupereka malipoti anu a utumiki wakumunda mwamsanga kumapeto a mwezi uliwonse, ndi njira inanso imene mungathandizire woyang’anira. Mungam’patse pamanja malipoti anuwo kapena mungaike m’bokosi loikamo malipoti a utumiki wakumunda pa Nyumba ya Ufumu. Mlembi angatengenso m’bokosi limeneli malipoti a utumiki wakumunda amene oyang’anira maphunziro a buku anasonkhanitsa.

      7 Anthu amayamikira ntchito imene mumagwira pothandiza woyang’anira Phunziro lanu la Buku la Mpingo. Koposa zonse, khalani ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ‘adzakhala ndi mzimu wanu.’—Afil. 4:23.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena