Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kulimbikitsa Omvera ndi Kuwatsitsimutsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    • Sonyezani Kuti Mukusangalala ndi Zimene Mulungu Akuchita Tsopano. Pofuna kulimbikitsa abale anu, auzeni zimene Yehova akuchita tsopano lino. Kunena zinthu zimenezo m’njira yosonyeza kuti mukusangalala nazo kudzachititsa omvera anunso kusangalala nazo.

      Sonyezani mmene Yehova amatithandizira kupirira mavuto. Iye amatisonyeza njira yabwino koposa yokhalira ndi moyo. (Yes. 30:21) Amafotokoza zifukwa zimene kwakhalira upandu, kupanda chilungamo, umphaŵi, matenda, ndi imfa, ndipo amatiuzanso mmene ati adzazithetsere zonsezo. Iye watitchinga ndi gulu la abale lachikondi. Watipatsa mwayi wamtengo wapatali wa pemphero. Watipatsanso mwayi wokhala Mboni zake. Watiunikira zakuti Kristu anakhazikitsidwa kale pa mpando wachifumu kumwamba ndi kuti masiku otsiriza a dziko lakaleli akuthamangira kumathero kwake.—Chiv. 12:1-12.

      Kuwonjezera pa madalitso onsewo pali misonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikuluikulu. Mukamafotokoza madalitso ameneŵa m’njira yosonyeza kuti mumawayamikiradi, mudzalimbikitsa ena kuti asamanyalanyaze kusonkhana pamodzi ndi abale awo.—Aheb. 10:23-25.

      Timapezanso nyonga mwa kumva malipoti onena za mmene Yehova wadalitsira ntchito yathu mu utumiki wa kumunda. M’zaka 100 zoyambirira pamene Paulo ndi Barnaba anali paulendo wopita ku Yerusalemu, ‘anakondweretsa kwambiri abale onse’ mwa kuwafotokozera tsatanetsatane wa mmene amitundu anali kutembenukira. (Mac. 15:3) Inunso mungakondweretse abale mwa kuwafotokozera zokumana nazo zolimbikitsa.

      Mukhoza kuwalimbikitsanso mwa kuwathandiza kuona phindu la zimene akuchita. Ayamikireni potenga mbali mu utumiki wachikristu. Athokozeni aja amene amachita zochepa zokha chifukwa cha ukalamba kapena matenda koma amapirirabe mokhulupirika. Akumbutseni kuti Yehova saiŵala chikondi chimene iwo asonyeza pa dzina lake. (Aheb. 6:10) Chikhulupiriro chopambana pa chiyeso ndi chuma cha mtengo wapatali. (1 Pet. 1:6, 7) M’pofunika kuwakumbutsa mfundo imeneyi abale athu.

      Lankhulani Mwachidaliro za Madalitso a M’tsogolo. Malonjezo ouziridwa a zinthu zilinkudza ndi gweronso lalikulu la chilimbikitso kwa onse okonda Mulungu. Mwina ambiri mwa omvera anu amva mobwerezabwereza za malonjezo amenewo. Koma mwa chiyamikiro chimene mumasonyeza polankhula za malonjezo ameneŵa, mukhoza kuonetsa kuti ndi enieni, mumapereka chidaliro chakuti zidzachitikadi, ndipo mumachititsa mitima ya omverawo kusefukira ndi chiyamiko. Kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kungakuthandizeni kuchita zimenezo.

      Yehova mwiniyo ndiye Wolimbikitsa Wamkulu ndi Wopereka nyonga kwa anthu ake. Komabe, mukhoza kuthandizana naye pakulimbikitsa ena ndi kuwapatsa nyonga. Pamene mulankhula ku mpingo, tengerani mwayi umenewo kuchita zimenezo.

  • Pitanibe Patsogolo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    • Pitanibe Patsogolo

      KODI mwayesa kugwiritsa ntchito maluso onse a kulankhula amene mwaphunzira mu sukuluyi? Kodi mwatsiriza zochita zoperekedwazo? Kodi mumagwiritsa ntchito luso lililonse pokamba nkhani zanu, kaya m’sukuluyi kapena pamisonkhano ina, komanso mu utumiki wa kumunda?

      Pitirizani kupindula ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kaya mwakhala mukukamba nkhani kwa utali wotani, zilipo mbali zimene mungapitebe nazo patsogolo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena