Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuthandiza Ena Kulemekeza Yehova
    Utumiki wa Ufumu—2002 | September
    • Kuthandiza Ena Kulemekeza Yehova

      1 Anthu padziko lonse akuuzidwa uthenga wofunika kwambiri, wakuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruzo chake; ndipo m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:6, 7) Ndi mwayi wathu kugwira nawo ntchito youza anthu uthenga umenewu. Kodi n’chiyani chimene anthu akufunika kudziŵa zokhudza Yehova kuti amuope ndi kum’lambira?

      2 Dzina Lake: Anthu akufunika kuti azitha kusiyanitsa dzina la Mulungu yekha woona ndi la milungu yambiri yonyenga imene anthu amalambira masiku ano. (Deut. 4:35; 1 Akor. 8:5, 6) Ndipotu, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito dzina lokwezeka lakuti Yehova maulendo oposa 7,000. Ngakhale kuti n’koyenera kuona pofunika kutchula dzina la Mulungu, tisamalibise kapena kupeŵa kuligwiritsa ntchito. Mulungu akufuna kuti anthu onse alidziŵe dzina lake.—Sal. 83:18.

      3 Makhalidwe Ake: Kuti anthu alemekeze Yehova, akufunika kudziŵa kuti iye ndi Mulungu wamtundu wanji. Tiyenera kuwaphunzitsa kuti ndi wachikondi kwambiri, wanzeru zoposa, wachilungamo chokhachokha ndiponso wamphamvuyonse. Komanso tiwaphunzitse za chifundo chake, kukoma mtima kwake ndi makhalidwe ake ena apadera. (Eks. 34:6, 7) Ayeneranso kuphunzira kuopa Mulungu ndi kum’lemekeza kwambiri chifukwa, kuti akhale ndi moyo m’pofunika kuti Yehova atiyanje.—Sal. 89:7.

      4 Kuyandikana ndi Mulungu: Kuti anthu apulumuke chiŵeruzo cha Mulungu chikubwerachi, akufunika kuitanira pa Yehova mwachikhulupiriro. (Aroma 10:13, 14; 2 Ates. 1:8) Izi sizikutanthauza kungophunzira dzina la Mulungu ndi makhalidwe ake basi. Tiyenera kuthandiza anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, ndikuti am’khulupirire ndi mtima wawo wonse. (Miy. 3:5, 6) Akamagwiritsa ntchito zimene akuphunzira, kupemphera kwa Mulungu moona mtima, ndi kuona kuti akuwathandiza pamoyo wawo, chikhulupiriro chawo chidzakula, ndipo zidzawathandiza kuyandikana ndi Yehova.—Sal. 34:8.

      5 Tiyenitu tilengeze mwachangu dzina la Mulungu ndi kuthandiza ena kuti am’khulupirire ndi mtima wawo wonse ndiponso kuti amuope. Tikhoza kuthandiza ena ambiri kudziŵa Yehova ndi kumulemekeza monga “Mulungu wa chipulumutso” chawo.—Sal. 25:5.

  • Samalirani Chuma Chimene Timagwiritsa Ntchito mu Utumiki wa Mulungu
    Utumiki wa Ufumu—2002 | September
    • Samalirani Chuma Chimene Timagwiritsa Ntchito mu Utumiki wa Mulungu

      1 Mfumu Yosiya pokonzekera kukonzanso kachisi, anauza anthu ogwira ntchitoyo kuti: “Sanawaŵerengera ndalamazo zoperekedwa m’dzanja lawo, pakuti anachita mokhulupirika.” (2 Maf. 22:3-7) Momwe anthu ameneŵa anagwiritsira ntchito zinthu zimene anaikizidwa, kunasonyeza kuti ankasamalira zinthu zopatulika. Ifenso masiku ano potumikira uthenga wabwino wa Mulungu, tifunika kusonyeza kukhulupirika pogwiritsa ntchito zinthu zimene taikizidwa.

      2 Mu Utumiki Wakumunda: Kuzindikira kuti uthenga wa m’mabuku athu ndi wofunika kwambiri ndiponso kuti pamafunika ndalama zambiri kuti awapange, kumatipangitsa kuwasamala kwambiri. Tisamagaŵe chisawawa mabuku athu kwa anthu amene sayamikira kwenikweni uthenga wa Baibulo. Ngati munthu wasonyeza chidwi pang’ono ndi uthenga wabwino, tingam’patse thirakiti osati mabuku.

      3 Gaŵirani mabuku mosonyeza kuti mumazindikira kufunika kwake. Peŵani kusiya mabuku pamtetete, pomwe angauluzike n’kungoti balala. Peŵani kuwononga magazini, mwa kuŵerenga amene mwatsala nawo kunyumba musanakawonjezere ena. Ngati nthaŵi zonse mumatsala ndi magazini, chepetsani oda yanu.

      4 Mabuku Anuanu: Tiziitanitsa mabuku okhawo amene timafunikadi. Makamaka tichepetse kuitanitsa mabaibulo a chikuto chofeŵa, mabaibulo a malifalensi, ndi mabuku ena, monga Concordance, Index, mavoliyumu a Insight, ndiponso buku la Proclaimers, zomwe ndi zinthu zimene zimafuna ndalama zambiri.

      5 Kodi mumalemba dzina ndi adiresi yanu m’mabuku anu? Izi zimathandiza kuti lina likasoŵa musamaitanitse lina. Ngati mwataya buku la nyimbo, Baibulo kapena buku lophunzirira, mukhoza kukalipeza ku zinthu zotayika pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo amsonkhano.—Luka 15:8, 9.

      6 Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito mwanzeru mabuku athu. Iyi ndi njira imene tingasonyezere kukhulupirika kwathu pogwiritsa ntchito zinthu za Ufumu zimene Yehova watiikiza.—Luka 16:10.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena