-
Mmene Mungayambitsire Maphunziro M’buku la Baibulo Limaphunzitsa ChiyaniUtumiki wa Ufumu—2006 | January
-
-
Mmene Mungayambitsire Maphunziro M’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
Ambirife tingasangalale kwambiri kuchititsa phunziro la Baibulo koma zimativuta kuyambitsa phunzirolo. Buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lingatithandize kutero. Mawu oyamba amene ali pa tsamba 3 mpaka 7 cholinga chake n’choyambitsa nkhani za m’Baibulo ndi mwini nyumba pogwiritsa ntchito bukuli. Ngakhale anthu amene angoyamba kumene kulowa m’munda sazivutika kuyambitsa maphunziro ndi bukuli.
◼ Mungayese njira iyi potsegula pa tsamba 3:
Tchulani nkhani inayake imene yafala kwanuko kapena tchulani vuto linalake limene lili m’maganizo mwa anthu ambiri a m’gawo lanu. Kenaka sonyezani mwininyumbayo mafunso amene alembedwa m’zilembo zakuda kwambiri pa tsamba 3, ndipo muuzeni kuti athirirepo ndemanga. Kenaka pitani pa tsamba 4 ndi 5.
◼ Mwina mungafune kuyamba ndi kugogomezera tsamba 4 ndi 5:
Munganene kuti, “Kodi zinthu zitasinthadi n’kukhala ngati mmene zilili pachithunzi ichi, sizingakhale bwino?” Kapena mungafunse kuti: “Kodi ndi lonjezo liti pa malonjezo awa limene mungakonde kuti likwaniritsidwe?” Mvetserani bwinobwino zimene munthuyo angayankhe.
Ngati mwininyumbayo atachita chidwi kwambiri ndi lemba linalake, musonyezeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani imeneyo pokambirana naye ndime zimene zikulongosola nkhaniyo m’bukuli. (Onani bokosi limene lili pa tsamba lino la mphatika.) Kambiranani monga mmene mungachitire pochititsa phunziro la Baibulo. Mungachite zimenezi ulendo woyamba, kwa mphindi zisanu kapena khumi.
◼ Njira inanso ndiyo yomulimbikitsa munthu kunena zakukhosi kwake popita pa tsamba 6:
Musonyezeni mwininyumbayo mafunso amene ali pansi patsambapo n’kumufunsa kuti, “Kodi munayamba mwadzifunsapo mafunso awa?” Ngati atachita chidwi ndi funso linalake pa mafunsowo, musonyezeni ndime za m’bukuli zomwe zikuyankha funsolo. (Onani bokosi limene lili pa tsamba lino la mphatika.) Mukayamba kukambirana nkhaniyi ndi munthuyo, ndiye kuti mukuchititsa phunziro la Baibulo.
◼ Mungapite pa tsamba 7 kuti musonyeze chitsanzo cha mmene timachitira phunziro la Baibulo:
Werengani ziganizo zitatu zoyambirira pa tsambali, ndipo kenaka pitani pa mutu 3, n’kuchita chitsanzo cha phunziroli pogwiritsa ntchito ndime 1 mpaka 3. Konzani zodzabweranso kuti mudzakambirane mayankho a mafunso a m’ndime 3.
◼ Mmene Mungakonzere Zodzabweranso:
Mukamamaliza phunziro loyamba, konzani zodzapitiriza zimene mwakambiranazo. Mwina mungathe kungonena kuti: “Mu mphindi zochepa chabe, taphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani yofunikira imeneyi. Nthawi ina, tingathe kudzakambirana za [funsani funso loti mudzakambirane]. Kodi mungakonde kuti mlungu wamawa ndidzabwere nthawi yomwe ino?”
Mmene tikuyandikira nthawi imene Yehova anaika, iye akupitiriza kutiphunzitsa kuti tikwanitse kuchita ntchito imene watipatsa. (Mat. 28:19, 20; 2 Tim. 3:17) Tiyeni tigwiritse ntchito bwino buku latsopanoli poyambitsa maphunziro a Baibulo.
-
-
Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa ChiyaniUtumiki wa Ufumu—2006 | January
-
-
Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
Mphatika ino ili ndi malangizo osiyanasiyana ofotokoza mmene mungagawire buku la Baibulo limaphunzitsa chiyani. Kuti malangizowa akhale othandizadi m’pofunika kumvetsetsa mfundo zake zofunikira n’kuzinena mogwirizana ndi mmene inuyo mumalankhulira nthawi zonse. Muzilankhula mogwirizana ndi anthu a m’gawo lanulo, ndipo dziwani bwino mfundo za m’bukuli zimene mungazigwiritse ntchito pokambirana ndi anthu. Mungathenso kugwiritsa ntchito njira zina zomwe zingathandize m’gawo lanulo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsamba 8.
Armagedo
◼ “Anthu ambiri akamva mawu akuti ‘Armagedo,’ amaganiza za nkhondo yopulula anthu kwadzaoneni. Kodi mungadabwe kumva kuti Armagedo ndi nkhondo yofunika kuiyembekezera mosangalala? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Chivumbulutso 16:14, 16.] Taonani mawu awa onena za mmene moyo udzakhalire, nkhondo ya Armagedo ikadzachitika.” Pitani pa tsamba 82 mpaka 84, ndipo werengani ndime 21.
Baibulo
◼ “Nthawi zambiri anthu amati Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti zingatheke bwanji kuti buku lolembedwa ndi anthu litchedwe Mawu a Mulungu? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 2 Petro 1:21 ndiponso ndime 5 pa tsamba 19 ndi 20.] Buku ili limayankha mafunsowa pogwiritsa ntchito Baibulo.” Asonyezeni mafunso amene ali pa tsamba 6.
◼ “Masiku ano, anthu akudziwa zinthu zambiri kuposa kale. Koma kodi mukuganiza kuti tingapeze kuti malangizo amene angatithandize kukhala ndi moyo wosangalala ndiponso wabwino? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 2 Timoteo 3:16, 17 ndi ndime 12 pa tsamba 23.] Buku ili likulongosola mmene tingakhalire ndi moyo wosangalatsa Mulungu ndiponso wotipindulitsa.” Aonetseni tchati ndiponso chithunzi chimene chili pa tsamba 122 ndi 123.
Banja
◼ “Tonsefe timafuna kukhala ndi mabanja osangalala. Kodi si choncho? [Asiyeni ayankhe.] Baibulo limatchulapo chinthu chinachake chimene aliyense m’banja angachite kuti banja likhale losangalatsa. Chinthu chake ndicho kutsanzira Mulungu posonyeza chikondi.” Werengani Aefeso 5:1, 2 ndiponso ndime 4 pa tsamba 135.
Imfa/Kuuka kwa Akufa
◼ “Anthu ambiri amadzifunsa kuti chimachitika n’chiyani kwenikweni tikafa. Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kudziwa zimenezi? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Mlaliki 9:5 ndiponso ndime 5 ndi 6 pa tsamba 58 ndi 59.] Buku ili limalongosolanso momwe anthu amene anamwalira adzapindulire m’tsogolo, lonjezo la Mulungu lomwe lili m’Baibulo loti adzaukitsa akufa likadzakwaniritsidwa.” Asonyezeni chithunzi chimene chili pa tsamba 75.
◼ “Munthu amene timamukonda akamwalira, mwachibadwa timafuna kudzamuonanso. Kodi si choncho? [Asiyeni ayankhe.] Anthu ambiri alimbikitsidwa ndi lonjezo la m’Baibulo lonena za kuuka kwa akufa. [Werengani Yohane 5:28, 29 ndiponso ndime 16 ndi 17 pa tsamba 71 ndi 72.] Mutu umenewu umayankhanso mafunso amenewa.” Asonyezeni mafunso amene ali koyambirira pa tsamba 66.
Masoka/Kuvutika
◼ “Pakaoneka masoka, anthu ambiri amakayikira zoti Mulungu amaganiziradi anthu ndiponso zoti iyeyo amaona anthu akamavutika. Kodi inuyo munayamba mwaganizirapo nkhani imeneyi? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 1 Petro 5:7 ndi ndime 11 pa tsamba 11.] Buku ili limafotokoza momwe Mulungu adzathetsere mavuto onse a anthu.” Asonyezeni mafunso omwe ali koyambirira pa tsamba 106.
Moyo Wosatha
◼ “Anthu ambiri amafuna kukhala ndi thanzi labwino ndiponso moyo wautali. Koma kodi zikanakhala zotheka, mukanakonda kukhala ndi moyo wosatha? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Chivumbulutso 21:3, 4 ndiponso ndime 17 pa tsamba 54.] Buku lino likulongosola mmene tingakhalire ndi moyo wosatha ndiponso mmene moyo udzakhalire lonjezo limenelo likadzakwaniritsidwa.”
Nkhondo/Mtendere
◼ “Anthu padziko lonse amafuna mtendere. Koma kodi inuyo mumaona kuti n’zotheka kuti padziko pano padzakhale mtendere? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Salmo 46:8, 9.] Buku ili limalongosola mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake ndi kubweretsa mtendere padziko lonse.” Asonyezeni chithunzi pa tsamba 35, ndipo werengani ndime 17 mpaka 21 pa tsamba 33 ndi 34.
Pemphero
◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti Mulungu amayankha bwanji mapemphero? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani 1 Yohane 5:14, 15 ndiponso ndime 16 mpaka 18 pa tsamba 170 mpaka 172.] Mutu umenewu umalongosolanso chifukwa chimene tiyenera kupemphera kwa Mulungu ndiponso zimene tiyenera kuchita kuti iye azimva mapemphero athu.”
Pokhala
◼ “M’madera ambiri, zikuvuta kwambiri kupeza malo abwino okhala omwe ali otsika mtengo. Kodi mukuganiza kuti nthawi inayake aliyense adzakhala ndi malo abwino okhala? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Yesaya 65:21,22 ndiponso ndime 20 pa tsamba 34.] Buku ili likulongosola mmene Mulungu adzakwaniritsire lonjezo lakeli.”
Yehova Mulungu
◼ “Anthu ambiri amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu amalakalaka atayandikana naye kwambiri. Kodi mukudziwa kuti Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyandikire kwa Mulungu? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Yakobo 4:8a ndiponso ndime 20 tsamba 16.] Buku ili analilemba n’cholinga choti lithandize anthu kudziwa zambiri zokhudza Mulungu, pogwiritsa ntchito Mabaibulo amene anthuwo ali nawo.” Asonyezeni mafunso omwe ali koyambirira pa tsamba 8.
◼ “Anthu ambiri amapemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti dzina la Mulungu ndani? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Salmo 83:18 ndiponso ndime 2 ndi 3 pa tsamba 195.] Buku limeneli limalongosola zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni zokhudza Yehova Mulungu ndi cholinga chake polenga anthu.”
Yesu Kristu
◼ “Anthu padziko lonse anamvapo za Yesu Kristu. Ena amanena kuti anali chabe munthu wotchuka basi. Ndiyeno pali ena amene amamulambira ngati Mulungu Wamphamvuyonse. Kodi inuyo mumaona kuti zimene munthu amakhulupirira pankhani ya Yesu Kristu zili ndi ntchito?” Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Yohane 17:3 ndiponso ndime 3 pa tsamba 37 ndi 38. Asonyezeni mafunso omwe ali koyambirira pansi pa mutu umenewo.
Zipembedzo
◼ “Anthu ambiri ayamba kuona kuti m’malo mothetsa mavuto ambiri amene tili nawowa, zipembedzo padziko lonse ndizo kwenikweni zikuyambitsa mavutowa. Kodi inuyo mukuganiza kuti zipembedzo zikutitsogolera ku njira yabwino? [Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Mateyu 7:13, 14 ndiponso ndime 5 pa tsamba 145 ndi 146.] Mutu uwu ukulongosola mfundo zisanu ndi chimodzi zodziwira kupembedza kumene Mulungu amavomereza.” Asonyezeni mfundo zimene azindandalitsa pa tsamba 147.
[Bokosi patsamba 5]
Njira Zouzira Anthu Kupereka Ndalama Mwakufuna Kwawo
“Ngati mutafuna kupereka kangachepe pofuna kuthandiza nawo pa ntchito yathu ya padziko lonse, zingakhale bwino kwambiri.”
“Mabuku athu sitigulitsa, koma timalandira kangachepe kalikonse kamene munthu angapereke pofuna kuthandiza nawo pa ntchito yathu ya padziko lonse.”
“Mwina mumadabwa kuti ntchito yathuyi timaiyendetsa bwanji. Ntchito imeneyi imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka padziko lonse mwakufuna kwawo. Ngati mungathe kupereka kangachepe panopo, tingayamikire kwambiri.”
-
-
(1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) MutuUtumiki wa Ufumu—2006 | January
-
-
(1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) Mutu
Njira yachidule yogawira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndiyo (1) kufunsa funso loti munthu anenepo maganizo ake, (2) kuwerenga lemba loyenerera, ndi (3) kumusonyeza mutu winawake m’bukuli umene ukulongosola nkhani mukukambiranayo pomuwerengera mafunso omwe ali koyambirira pansi pa mutuwo. Ngati mwininyumbayo ali ndi chidwi, mungagwiritse ntchito ndime zoyambirira za mutu umenewo pomusonyeza chitsanzo cha mmene timachitira phunziro la Baibulo. Njira imeneyi tingathe kuigwiritsa ntchito poyambitsa maphunziro pa ulendo woyamba kapena wobwereza.
◼ “Kodi mukuganiza kuti anthu a thupi lanyama ngati ifeyo tingathe kum’dziwa Mlengi, yemwe ali Wamphamvuyonse monga mmene lemba la m’Baibulo ili likunenera?” Werengani Machitidwe 17:26, 27, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 1.
◼ “Masiku ano pali mavuto ambiri, ndiye kodi mukuganiza kuti n’zotheka kupeza chitonthozo ndiponso chiyembekezo chimene chikunenedwa pa lemba ili?” Werengani Aroma 15:4, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 2.
◼ “Kodi mukanakhala ndi mphamvu zotha kusintha zinthu mukanatha kusintha zinthu kuti zikhale monga mmene lemba ili likulongosolera?” Werengani Chivumbulutso 21:4, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 3.
◼ “Kodi mukuganiza kuti kutsogolo kuno ana athu adzakhala m’dziko losangalatsa langati limene analilongosola mu nyimbo yakale iyi?” Werengani Salmo 37:10, 11, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 3.
◼ “Kodi mukuganiza kuti nthawi inayake mawu awa adzakwaniritsidwa?” Werengani Yesaya 33:24, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 3.
◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo ngati anthu akufa amadziwa zimene anthu amoyo akuchita?” Asiyeni ayankhe. Kenaka werengani Mlaliki 9:5, ndipo asonyezeni mutu 6.
◼ “Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kuti tsiku lina tidzaonanso okondedwa athu amene anamwalira, monga mmene Yesu ananenera pa mavesi awa?” Kenaka werengani Yohane 5:28,29, ndipo asiyeni ayankhe. Ndiyeno asonyezeni mutu 7.
◼ “Kodi mukuganiza kuti pakufunika chiyani kuti kufuna kwa Mulungu kuchitike padziko pano monga kumwamba, mogwirizana ndi zimene pemphero lotchuka ili limanenera?” Werengani Mateyu 6:9, 10, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 8.
◼ “Kodi mukuganiza kuti tikukhala mu nthawi imene inalongosoledwa mu ulosi uwu?” Werengani 2 Timoteo 3:1-4, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 9.
◼ “Anthu ambiri samvetsa kuti n’chifukwa chiyani mavuto a anthufe akumka aipiraipira. Kodi munayamba mwaganizirapo kuti zimene lemba ili likunena n’zimene zikuchititsa mavutowa?” Werengani Chivumbulutso 12:9, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 10.
◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo funso ngati ili?” Werengani Yobu 21:7, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 11.
◼ “Kodi mukuganiza kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo awa kungathandize anthu kukhala osangalala m’banja mwawo?” Werengani Aefeso 5:33, ndipo asiyeni ayankhe. Kenaka asonyezeni mutu 14.
Mungachitire lipoti phunziro la Baibulo ngati mwaphunzira maulendo awiri kuchokera pamene munasonyeza wophunzirayo kachitidwe kake ndipo zikuoneka kuti phunzirolo lipitirira.
-