-
Nyengo ya Chikumbutso ndi Nthawi Yochita ZambiriUtumiki wa Ufumu—2005 | February
-
-
[Tchati patsamba 5]
Zitsanzo za Ndandanda Yochitira Upainiya Wothandiza Njira Zopangira Ndandanda ya Maola 12 a mu Utumiki wa Kumunda Mlungu Uliwonse
M’mawa—Lolemba Mpaka Loweruka
Lamlungu lingalowe m’malo mwa tsiku lina lililonse.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba M’mawa 2
Lachiwiri M’mawa 2
Lachitatu M’mawa 2
Lachinayi M’mawa 2
Lachisanu M’mawa 2
Loweruka M’mawa 2
Onse Pamodzi: 12
Masiku Awiri Athunthu
Mukhoza kusankha masiku ena alionse awiri pa mlungu (Mogwirizana ndi masiku amene mungasankhe, ndandanda imeneyi ingakupatseni maola 48 okha pa mwezi.)
Tsiku Nthawi Maola
Lachitatu Tsiku Lonse 6
Loweruka Tsiku Lonse 6
Onse Pamodzi: 12
Madzulo Awiri ndi Loweruka ndi Lamlungu
Mukhoza kusankha madzulo alionse awiri a m’kati mwa mlungu.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba Madzulo 1 1⁄2
Lachitatu Madzulo 1 1⁄2
Loweruka Tsiku Lonse 6
Lamlungu M’mawa Kapena Masana Okha 3
Onse Pamodzi: 12
Masana Atatu ndi Loweruka
Lamlungu lingalowe m’malo mwa tsiku lina lililonse.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba Masana 2
Lachitatu Masana 2
Lachisanu Masana 2
Loweruka Tsiku Lonse 6
Onse Pamodzi: 12
Ndandanda Yanga ya mu Utumiki
Sankhani chiwerengero cha maola a tsiku lililonse.
Tsiku Nthawi Maola
Lolemba
Lachiwiri
Lachitatu
Lachinayi
Lachisanu
Loweruka
Lamlungu
Onse Pamodzi: 12
-
-
Zofunika Kukumbukira pa ChikumbutsoUtumiki wa Ufumu—2005 | February
-
-
Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
Chikumbutso cha chaka chino chidzachitika Lachinayi, pa March 24. Akulu asamalire zinthu izi:
◼ Pokonza nthawi ya mwambowu, onetsetsani kuti musapereke zizindikiro dzuwa lisanalowe.
◼ Aliyense, ngakhale wokamba nkhani, auzidwe nthawi yeniyeni ndi kumene kudzachitikire mwambowu.
◼ Mupezeretu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2003, tsamba 14 ndi 15.
◼ Mbale, matambula, thebulo labwino ndi nsalu za pathebulo ziyenera kubwera ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake nthawi yabwino.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu ayeretsedweretu bwinobwino.
◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi operekera zizindikiro ndipo muwauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu, ndiponso kuti afunika adzavale zovala zopatsa ulemu ndiponso kudzikonza bwino.
◼ Konzani zokapereka zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense amene akudwala ndipo satha kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kuti anthu asadzapanikizane pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika magalimoto.
-