Nyimbo 203
Yehova Amatsogolera Anthu Ake
1. M’lungu apereka chidziŵitso.
Alangiza anthu ake moleza mtima!
Watigaŵira kudzisankhira.
Amaika chowonadi m’mitima mwathu.
2. Munjira yake ndi nthaŵi yake,
Mwa mzimu woyera amavumbula zinthu.
“Kapolo” wake atidziŵitsa,
Mwachikondi mitima yathu ikondwera.
3. Chitsogozocho chiwongolera,
Chimapereka mphamvu kwa olungamawo.
Tikasinthadi m’kumvera kwathu,
Yehova adzatitsogoza m’dzina lake.
4. Tithokoza chithandizo chake,
Kuti tizindikire chowonadi chake.
Yehova ndi Bwenzi lathu ndithu;
Motsimikizira adzatitsogolera.