‘Lankhulani Mawu a Mulungu Mopanda Mantha’
1 Kodi nthawi zina mumachita mantha kulankhula za chikhulupiriro chanu mukapatsidwa mwayi kusukulu kapena kuntchito? Kodi zimakuvutani kulalikira mwamwayi kwa achibale ndi anansi anu kapena kwa anthu amene simukuwadziwa? Kodi n’chiyani chingatithandize tonsefe ‘kulankhula Mawu a Mulungu mopanda mantha’ tikakhala ndi mpata?—Afil. 1:14.
2 Musachite Mantha: Kodi mungachite mantha kuteteza mnzanu wapamtima kapena wachibale amene amunenera zinthu zonama? Yehova, Bwenzi lathu lapamtima, waneneredwa zinthu zambiri zonama kwa zaka zambiri. Tili ndi mwayi wapadera wopereka umboni ndi kuikira kumbuyo Mulungu wathu wamkulu. (Yes. 43:10-12) Chifukwa cha kukonda Yehova kwambiri, sitichita manyazi kapena mantha kulankhula molimba mtima popereka umboni wa choonadi.—Mac. 4:26, 29, 31.
3 Kumbukirani kuti uthenga wathu ndi uthenga wabwino. Anthu akaulabadira, adzapeza madalitso osatha. Choncho, tikamaganizira kwambiri za ubwino wa ntchito yolalikira m’malo moganizira za ife eni kapena za adani athu, tidzatha kulalikira mopanda mantha.
4 Zitsanzo za Ena: Ngati tiganizira za anthu okhulupirika amene analankhula mawu a Mulungu mopanda mantha, tingathe kulankhula molimba mtima. Mwachitsanzo, Inoke analankhula molimba mtima polengeza za chiweruzo cha Yehova kwa anthu ochimwa ndiponso osaopa Mulungu. (Yuda 14, 15) Mokhulupirika, Nowa analalikira kwa anthu opanda chidwi. (Mat. 24:37-39) Akhristu oyambirira amene anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” anapitiriza kulalikira ngakhale ankatsutsidwa kwambiri. (Mac. 4:13, 18-20) Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amakhala ndi nkhani zamakono za anthu amene analeka kuopa anthu chifukwa chokhulupirira Yehova, ndipo anakhala alaliki achangu.
5 Ndithudi, kuganizira za moyo wa atumiki okhulupirika akale amene akumana ndi mavuto, kungatithandize kulimba mtima. (1 Maf. 19:2, 3; Maliko 14:66-71) Iwo ‘analimba mtima mwa Mulungu wathu’ ndipo analankhula mopanda mantha. Ifenso tingachite chimodzimodzi.—1 Ates. 2:2.