Nyimbo 106
Tisamalire Mayendedwe Athu
1. Tisamalire Kuyenda kwathu,
Tikhale maso m’kuchenjera,
Tiombole nthaŵi poti
Satana alamula.
Tisamalire Malankhulidwe,
Tikhale maso ndi anzeru.
2. Tisamalire Kulalikira,
Tilimbikitsetu ofatsa.
Mwa kuphunziranso nawo,
Tidzawathandizadi.
Tisamalire Kaphunzitsidwe,
Tiwathandizetu ofatsa.
3. Tisamalire Kupatsa moni
Kwa opezeka mu’tumiki.
Monga Kristu Mbusa wathu,
Tisamalire “nkhosa.”
Tisamalire Kupatsa moni,
Ndi kusakhumudwitsa yense.