Nyimbo 91
Kuphunzitsidwa ndi Yehova
1. Ya watumiza cho’nadi;
Ndi Mlangizi Wamkulu.
Atsogolera nkhosazo
Monga Woyang’anira.
Nthaŵi ya kudziŵa yadza
Kuti ndi Wamkuludi,
Apereka malangizo
mwachikondi kwa ofatsa.
Mmisiri wake Kristuyo,
Anali mphunzitsidi.
Nanena za Tate wake,
Ndiponso za Ufumu.
Mongaditu anapiye,
Athandiza anthu onse.
Lerolino aphunzitsa
Onga nkhosa mukholalo.
2. Ya watipatsa abusa
Oyesa kuphunzitsa.
Lirime lawo lisonya
Ngowongoka mitima.
Othodwa awathandiza.
Adzudzula olakwa.
Mwa kuphunzitsa zowona;
asangalatsa Yehova.
Tiphunzitsidwadi ndi Ya;
Mwana’ke atsogoza.
Tiri ndi mwaŵi ndithudi
Cho’nadi tiri nacho.
Tikafunitsitsa awo
Okhumba chowonadichi,
Kuli mwa kulalikira,
Aphunzira kumlambira.
3. ‘Idzani mudziŵe za Ya,’
Ichi nchi’tano chathu.
Kuphunzitsa kuchitidwa
Kwa kuchipulumutso.
Mwa zolembedwa ndi mawu
Mbiri ya Ufumuwo
Ikulalikidwa m’dziko
ndi kumitundu yonseyo.
Monga antchito tifuna
Kukhulupirikabe
Tiyendebe m’chowonadi,
Tiimire Ufumu.
Mu’lamuliro wa Kristu
Oukitsidwa apeza
Malangizo opezera
Moyo padziko lapansi.