Nyimbo 16
Kondwererani Chiyembekezo Chaufumu!
1. Kondwani! Kondwani!
Kondwererani Ufumu!
Kondwani! Kondwani!
Ufumu wayamba!
Gwiritsani ufumuwo.
Khalani achangu.
Gwirani chiyembekezo.
Dziŵitsani onse.
Kondwani! Kondwani!
Dziwitsani Ufumuwo!
Kondwani! Kondwani!
Ufumu wayamba!
2. Kondwani! Kondwani!
Gwirani chiyembekezo!
Kondwani! Kondwani!
Dalirani M’lungu!
Yembekezerani zedi.
Musagwedezeke.
Simuyendanso mumdima;
Mwagudwa kuimfa.
Kondwani! Kondwani!
M’yembekezere Yehova!
Kondwani! Kondwani!
Peŵani Satana!
3. Imbani! Imbani!
Ufumu utilimbitsa!
Imbani! Imbani!
Tumikirani Ya!
Tukulani maso anu!
Ndinthaŵi yotuta,
Mumatulutsa zipatso,
Poyandika nkhosa.
Imbani! Imbani!
Mulungu alimbikitsa!
Imbani! Imbani!
Gwiritsa umphumphu!