Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Kwa Mboni za Yehova Zinzathu,
Pampata uliwonse umene mtumwi Paulo anali nawo, anali kuyamikira okhulupirira anzake ndi kuwauza kuti amawakonda. Iye analembera Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikuyamika Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu kaamba ka nonsenu, chifukwa chakuti chikhulupiriro chanu chikusimbidwa m’dziko lonse.” (Aroma 1:8) Inde, Akhristu a m’nthawi ya Paulo amenewo anali kudziwika mu ufumu wonse wa Roma kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba, ndiponso kuti anali kulalikira mwachangu. (1 Ates. 1:8) N’zosadabwitsa kuti Paulo ankawakonda kwambiri abale ake.
Mofanana ndi Paulo, ifenso timayamikira Yehova nthawi iliyonse tikaganiza za inu. Timakukondani kwambiri nonsenu. Ndipo khalani otsimikiza kuti Yehova amakonda aliyense wa inu. Ena mwa inu mukutsutsidwa kwambiri, koma mukupitirizabe kulalikira. Mzimu wopanda mantha umene mumasonyeza umakondweretsa kwambiri mtima wa Yehova.—Miy. 27:11.
Tikukhulupirira kuti mukamaganizira zochita za Mboni za Yehova masiku ano, mumaona umboni wokwanira wakuti Ambuye Yesu Khristu akupita “kukagonjetsa ndi kukatsiriza kugonjetsa kwake” ndiponso kuti palibe chida chosulidwira otsatira a Khristu chimene chidzapambana.—Chiv. 6:2; Yes. 54:17.
Kwa Akhristu a ku Filipi, Paulo analemba kuti: “Ndimayamika Mulungu wanga . . . chifukwa cha chopereka chimene mwapereka ku uthenga wabwino.” (Afil. 1:3-5) Mmenemu ndi mmene ifenso a m’Bungwe Lolamulira timamvera tikamaganiza za inu. M’chaka chautumiki cha 2007, ofalitsa 6,691,790 anathera maola okwana 1,431,761,554 polalikira uthenga wabwino m’mayiko 236 padziko lonse. Mukuchitatu khama kwambiri pantchito yopititsa patsogolo uthenga wabwino. Anthu ambirimbiri athandizidwa chifukwa cha khama lathu tonse, ndipo zimenezi zimabweretsa chitamando kwa Yehova.
Panthawi ina, Paulo anasonyeza kuti anali kumvera chisoni kwambiri abale ake. Iye analembera amene anali ku Tesalonika kuti: “Timakumbukira nthawi zonse . . . chipiriro chimene muli nacho chifukwa cha chiyembekezo chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.” (1 Ates. 1:2, 3) N’zoona kuti moyo uli ndi mavuto ambiri. Timakumana ndi mavuto osiyanasiyana, koma kupirira n’kofunika. Kodi ndi mavuto otani amene inuyo mukukumana nawo? Kodi ndinu wokhumudwa chifukwa cholephera kuchita zambiri muutumiki wa Yehova popeza mukudwala kwambiri? Kodi mwamuna kapena mkazi wanu amene munakhala naye kwa nthawi yaitali anamwalira? (Miy. 30:15, 16) Kodi zikuoneka ngati mukulephera kupeza munthu wokonda Yehova ngati inuyo woti mukwatirane naye, koma inuyo mukufunabe kutsatira uphungu wa m’Malemba wa kukwatira kokha mwa Ambuye? (1 Akor. 7:39) Kodi mukuyesetsa kulera ana anu ngakhale kuti muli ndi mavuto aakulu a zachuma? Kaya zinthu zili bwanji pamoyo wanu, ngati mupitiriza kuika zinthu za Ufumu patsogolo, tsimikizani kuti Yehova ‘sadzaiwala ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.’ Abale ndi alongo, chonde musaleke “kuchita zabwino.”—Aheb. 6:10; Agal. 6:9.
Kodi n’chiyani chidzakuthandizani kupirira? Mofanana ndi Akhristu a ku Tesalonika, “chiyembekezo . . . mwa Ambuye wathu Yesu Khristu” n’chimene chidzakuthandizani. Pachifukwa chomveka bwino, Paulo anayerekezera “chiyembekezo cha chipulumutso” ndi chisoti cholimba zedi chimene chingathandize Mkhristu kupewa kukayikakayika ndiponso maganizo olakwika.—1 Ates. 5:8.
Kunena zoona, mukamakhala achimwemwe popirira, mumayankha zitonzo za Satana pa nkhani ya woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Satana amati atumiki a Mulungu mwachibadwa ndi adyera, ndipo ngakhale kuti angakonde kutumikira Mulungu kwa nthawi yochepa, iwo angasiye kumulambira atakumana ndi mayesero ochuluka, kapena ataona kuti dongosolo la zinthu lino silikutha panthawi imene iwo anali kuganizira. Muli ndi mwayi wosonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza lamkunkhuniza. Tsiku lililonse mumayandikira nthawi imene mudzalandira madalitso omwe mukuyembekezera.
Mofanana ndi Paulo amene anasangalala kupeza mipata yoyamikira abale ake chifukwa cha chikhulupiriro chawo champhamvu, chifukwa chogwira ndi mtima wonse ntchito yolalikira, ndiponso chifukwa cha kupirira kwawo, ifenso tikusangalala kukhala ndi mwayi wokuyamikirani ndi kukutsimikizira kuti timakukondani. Pitirizani kugwira ntchito yabwinoyi.
Pemphero lathu n’lakuti mupezenso madalitso ochuluka auzimu m’chaka chikubwerachi. Tikukufunirani zabwino zonse.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova